Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Mabaibulo Ochokera ku Japan

Mabaibulo Ochokera ku Japan

Pofuna kuthandiza anthu ambiri ofuna Mabaibulo a zikuto zolimba ndiponso abwino kwambiri, a Mboni za Yehova aika makina okonzera mabuku kufakitale yawo ya ku Ebina, m’dziko la Japan.

Poyamba, anthu ena ankada nkhawa kuti mwina makinawa sangagwire bwino ntchito chifukwa cha chivomerezi ndiponso tsunami zimene zinachitika ku Japan pa March 11, 2011, zomwe zinachititsa vuto lamagetsi.

Komabe pofika mu September 2011, ntchito yoika makinawa mufakitale inali ili mkati. Pasanapite miyezi itatu, makinawa anayamba kugwira ntchito moti Mabaibulo a Dziko Latsopano a m’Chitchainizi anali oyambirira kusindikizidwa.

Makina opangira mabukuwa alipo angapo ndipo iliyonse ndi yaitali mamita pafupifupi 400. Mapepala osindikizidwa akamadutsa m’makinawa, amamatidwa n’kukhala buku, kuikidwa chikuto, kusanjidwa, kuikidwa m’makatoni omwe kenako amawasanja pamalo amodzi.

Mu Umodzi Muli Mphamvu

Ntchito yoika makinawa inayenda bwino chifukwa chokonzekera bwino komanso kugwirizana. Mwachitsanzo, makinawa anafunika kuikidwa m’makontena okwana 34 n’kunyamulidwa kuchokera ku Ulaya kupita ku Japan.

Anthu 10 a Mboni za Yehova omwe ankagwira ntchito ku ofesi ya nthambi ya ku United States anapita ku Japan kukathandiza pa ntchitoyi. Ena anakhala ku Japan kwa miyezi 6 ndipo anaphunzitsa anthu a ku Japan mmene angagwiritsire ntchito makinawo komanso kuwakonza akawonongeka.

Anthu ogwira ntchito m’makampani opanga ndi kusindikiza mabuku a ku Japan anachita chidwi kwambiri ndi makina atsopanowo. Moti pa March 19, chaka cha 2012, anthu opitirira 100 ochokera ku makampaniwa anapita kufakitale komwe kuli makina athu atsopanowo kuti akadzionere okha. Iwo anagoma kwambiri.

Pa nthawi imene anthu odzaona makinawa ankachoka, aliyense anapatsidwa Baibulo la Dziko Latsopano limene linasindikizidwa ndi makina atsopanowa.

Panopa ofesi ya Mboni za Yehova ya ku Japan ikusindikiza Mabaibulo a zikuto zolimba omwe ikuwatumiza m’madera osiyanasiyana padziko lapansili monganso mmene maofesi a ku United States ndi Brazil amachitira.

“Sindidzasangalala Ngati Mmene Ndasangalalira Kuno”

Anthu a Mboni za Yehova komanso anthu ena ochokera m’makampani osiyanasiyana omwe anathandiza pa ntchito yoika makinawa m’fakitale ankasangalala kwambiri pa nthawi imene ankagwira ntchitoyi. Munthu wina yemwe si wa Mboni ananena kuti: “Munkandikonda kwambiri moti munali ngati abale anga.

Pa tsiku limene anamaliza kugwira ntchitoyi, munthu wina yemwe sanali wa Mboni ananena kuti: “Kumalo otsatira kumene ndidzakagwire ntchito sindidzasangalala ngati mmene ndasangalalira ku Watchtower kuno.