“Mavidiyowa Ndi Abwino Kwambiri Kuposa Mafilimu Ambiri”
Chaka chilichonse, a Mboni za Yehova amapanga mavidiyo omwe amaonetsa pamisonkhano yawo yachigawo. Ambiri mwa mavidiyowa amajambulidwa m’chilankhulo cha Chingelezi. Ndiye kodi zimatheka bwanji kuti anthu omwe amachita misonkhanoyi m’zilankhulo zina azimva zomwe zili m’mavidiyowa? M’zilankhulo zambiri, mawu a m’zilankhulozo amajambulidwa padera ndipo kenako amaikidwa m’vidiyoyo. Kodi mavidiyo amene amapangidwa mwa njira imeneyi amathandiza bwanji anthu omwe amawamvetsera?
Zimene Anthu Ena Ananena Ataonera Mavidiyo M’chilankhulo Chawo
Tamvani zimene anthu ena omwe si a Mboni ananena atapanga nawo msonkhano wachigawo ku Mexico ndi ku Central America:
“Sikuti ndinangomva zomwe zimanenedwa m’vidiyoyo, koma zinali ngati ndili m’vidiyoyo. Inandifika pamtima kwambiri.”—Anatero munthu wina wamwamuna yemwe anachita nawo msonkhano wachigawo wa chilankhulo cha Popoluca ku Veracruz, Mexico.
“Ndinangomva ngati ndili m’tauni ya kwathu ndikucheza ndi mnzanga wapamtima. Mavidiyowa ndi abwino kwambiri kuposa mafilimu ambiri chifukwa ndimamva zonse zomwe zikunenedwa.”—Anatero munthu wina wamwamuna yemwe anachita nawo msonkhano wachigawo wa chilankhulo cha Nahuatl ku Nuevo León, Mexico.
“Nditaonera mavidiyo m’chilankhulo changa, ndinkangomva ngati anthu a m’mavidiyowo akulankhula ndi ineyo.”—Anatero munthu wina wamkazi yemwe anachita nawo msonkhano wachigawo wa chilankhulo cha Chol ku Tabasco, Mexico.
“Gululi lili ndi chidwi chofuna kuthandiza anthu kuphunzira m’chilankhulo chawo. Palibenso gulu lina ngati limeneli!”—Anatero munthu wina wamwamuna yemwe anachita nawo msonkhano wachigawo wa chilankhulo cha Cakchiquel ku Sololá, Guatemala.
Popeza kuti a Mboni za Yehova salemba ntchito akatswiri ojambula mawu a m’mavidiyo kapena anthu owerenga m’mavidiyo, komanso amajambulira m’madera osatukuka kwenikweni, kodi zimatheka bwanji kuti azijambula zinthu zapamwamba kwambiri?
“Ntchito Yabwino Kwambiri”
Ofesi ya nthambi ya ku Central America inatsogolera ntchito yojambula mavidiyo a misonkhano yachigawo ya 2016 a chilankhulo cha Chisipanishi ndi zilankhulo zinanso 38 za ku Central America. Anthu ongodzipereka okwana 2,500 anagwira nawo ntchitoyi. Ojambula mawu a m’mavidiyo a zilankhulozi komanso magulu omasulira, anajambulira mawuwo pa ofesi ya nthambi, m’maofesi omasulira mabuku, komanso m’madera ena omwe anamangamo masitudiyo osafuna zambiri. Maguluwa anajambula mawu a m’mavidiyowa m’malo oposa 20 ku Belize, Guatemala, Honduras, Mexico, ndi Panama.
Anthuwa ankafunika kugwira ntchito mwakhama komanso kupeza njira zothanirana ndi mavuto omwe analipo kuti amange masitudiyo osafuna zambiri. Pofuna kuti phokoso lisamalowe m’malo ojambulirawo, iwo anagwiritsa ntchito zinthu zosavuta kupezeka monga mabulangete komanso matiresi.
Anthu ambiri omwe anawerenga m’mavidiyo a zilankhulo zosiyanasiyana za ku Central America, analibe ndalama zokwanira ndipo analolera kusiya zinthu zina kuti apite kumalo ojambulira mavidiyowo. Ena mwa anthuwo anayenda ulendo wa maola 14. M’dera lina, bambo ndi mwana wake wamwamuna anayenda ulendo wapafupifupi maola 8 kuti akafike ku malo ojambulira mavidiyo.
Naomi ali wamng’ono ankathandiza anthu a m’banja lake kumanga masitudiyo osafuna zambiri. Iye anati: “Nthawi zonse tinkayembekezera mwachidwi mlungu umene zinthu zikujambulidwa. Bambo anga ankagwira ntchito mwakhama poonetsetsa kuti ntchitoyo itheke. Nthawi zina mayi anga ankaphika chakudya cha anthu 30 omwe abwera kudzagwira ntchitoyo.” Panopa Naomi amagwira ntchito pa ofesi ina yomasulira ku Mexico. Iye anati: “Ndine wosangalala kwambiri kuti ndimagwiritsa ntchito nthawi yanga kuthandiza anthu ena kuti amve uthenga wa m’Baibulo m’chilankhulo chawo chobadwira. Imeneyi ndiyo ntchito yabwino kwambiri yomwe ndingamagwire.”
Misonkhano yachigawo ya Mboni za Yehova imachitika padziko lonse chaka chilichonse ndipo aliyense akhoza kupezeka pamisonkhanoyi. Kuti mudziwe zambiri zokhudza misonkhano yachigawo, onani pa gawo lakuti MISONKHANO pa webusaiti yathu.