Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Nsanja ya Olonda ya M’Chingelezi Chosavuta Kumva

Nsanja ya Olonda ya M’Chingelezi Chosavuta Kumva

Kuyambira mu July 2011, panayamba kutulukanso magazini ina ya Nsanja ya Olonda yophunzira yomwe imalembedwa m’Chingelezi chosavuta. Gulu la Mboni za Yehova linakonza zotulutsa magazini imeneyi mongoyeserera chabe kwa chaka chimodzi. Panopa chaka chatha chiyambireni kutulutsa magaziniyi ndipo a Mboni za Yehova aona kuti apitirizebe kutulutsa magaziniyi.

Ndipo kuyambira mu January 2013, magazini yophunzira ya Nsanja ya Olonda izilembedwanso m’zinenero zitatu zina mosavuta kumva. Zinenerozi ndi Chifalansa, Chipwitikizi ndiponso Chisipanishi.

Magazini ya Nsanja ya Olonda yophunzira yomwe imalembedwa m’Chingelezi chosavuta kumva inakonzedwa n’cholinga chothandiza anthu amene ali m’mipingo yachingelezi omwe anachita kuphunzira Chingelezicho.

Magazini yoyamba ya m’Chingelezi chosavuta kumvachi itangotuluka, anthu anayamba kulemba makalata oyamikira magaziniyi. Mwachitsanzo, Rebecca yemwe ali ndi zaka 64 ndipo amakhala ku Liberia koma sanapite kusukulu, analemba kuti: “Popeza ndikuphunzira kuwerenga, nthawi zina ndinkati ndikawerenga Nsanja ya Olonda sindinkaimvetsa. Koma ndimakonda Nsanja ya Olonda ya m’Chingelezi chosavuta kumvachi chifukwa ndimaimvetsa bwino.

Makolo ambiri akugwiritsira ntchito Nsanja ya Olonda ya m’Chingelezi chosavuta kumvachi pothandiza ana awo kukonzekera msonkhano wa Phunziro la Nsanja ya Olonda umene a Mboni za Yehova amachita.

Mwachitsanzo, mayi wina dzina lake Rosemary amene akulera adzukulu ake atatu analemba kuti: “Zinali zovuta kwambiri kuphunzira Nsanja ya Olonda ndi atsikanawa moti tinkagwiritsira ntchito dikishonale kuti timvetse tanthauzo la mawu ambiri. Choncho tinkathera nthawi yaitali tikufufuza tanthauzo la mawu osiyanasiyana a m’nkhani zina ndipo anawo ankasokonezeka n’kulephera kumvetsa mfundo zofunika za m’nkhaniyo. Panopa nthawi yathu imathera pa kuwerenga malemba komanso kuona mmene malembawo akugwirizanira ndi nkhaniyo.