Baibulo Lolimba Kwambiri
A Mboni za Yehova amaona kuti Baibulo ndi buku lofunika kwambiri kuposa buku lina lililonse. Nthawi zonse, iwo amaliphunzira komanso amaligwiritsa ntchito pophunzitsa ena za uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. (Mateyu 24:14) Zimenezi zimachititsa kuti Mabaibulo awo asamachedwe kutha. Choncho, pokonza Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika limene linatuluka mu 2013, a Mboni anagwira ntchito yaikulu yoonetsetsa kuti Baibuloli likhale lokongola komanso lolimba kwambiri.
Choncho anthu a Mboni za Yehova amene amayendetsa ntchito yosindikiza mabuku ku Wallkill, m’dera la New York m’dziko la United States of America, anapita kukakambirana za mapulani osindikiza Baibuloli ndi mkulu wa kampani ina yopanga mabuku. A Mboniwo atauza mkuluyo za mapulani awo, iye anawauza kuti: “N’zosatheka kupanga Baibulo limene mukufunalo.” Iye ananenanso kuti: “N’zomvetsa chisoni kuti Mabaibulo ambiri amakhala okongola koma osalimba. Amangokonzedwa m’njira yakuti azioneka bwino akasiyidwa patebulo kapena pashelefu basi.”
Mabaibulo ena a Dziko Latsopano amene anasindikizidwa m’mbuyomu anali osalimba kwenikweni ndipo nthawi zina ankang’ambika kapena kuchoka chikuto, makamaka akamagwiritsidwa ntchito m’nyengo yotentha kwambiri. Motero, ena mwa anthu a Mboni amene amagwira ntchito yosindikiza mabuku, anayamba kufufuza njira yoti asindikize Mabaibulo olimba zedi, amene sangawonongeke ngakhale atamagwiritsidwa ntchito mwakathithi m’nyengo yotentha kapena yozizira kwambiri. Atafufuza, anasindikiza Mabaibulo angapo omwe anawatumiza m’madera osiyanasiyana otentha komanso ozizira kwambiri, n’cholinga choti anthu a Mboni akawagwiritse ntchito mongoyeserera.
Patatha miyezi 6, a Mboni amene amagwira ntchito yosindikiza mabuku aja anaitanitsa Mabaibulo amene anawatumiza m’madera osiyanasiyana, n’cholinga choti awaonenso. Iwo anasintha zina n’zina n’cholinga choti Mabaibulowo akhale olimba, kenako anasindikizanso ena n’kuwatumiza m’madera osiyanasiyana. Mabaibulo onse amene anatumizidwa kuti akayesedwe anali okwana 1,697. Ndipotu panachitika zinthu zina zimene zinayesadi ena mwa Mabaibulowa. Mwachitsanzo, Baibulo lina linaiwalidwa panja mwangozi ndipo linanyowa ndi mvula usiku wonse, ndipo lina linamira m’madzi osefukira a mvula yamphamvu. Zimene zinachitikira Mabaibulo amene ananyowawa komanso Mabaibulo ena onse zinathandiza anthu a Mboni za Yehova omwe amagwira ntchito yosindikiza mabuku kuti adziwe ngati Mabaibulowo anali olimba kwambiri kapena ayi.
Pa nthawi imene ntchito yoyesa Mabaibulo inali m’kati mu 2011, a Mboni anagula makina apamwamba kwambiri osindikizira mabuku komanso okonzera zikuto, omwe anawaika ku Ebina m’dziko la Japan ndiponso ku Wallkill. Cholinga chawo sichinali kungosindikiza Mabaibulo ambiri chabe, koma kuti Mabaibulo omwe angasindikizidwe m’malo awiri onsewa azioneka mofanana.
Mavuto a Zikuto
Chakumayambiriro kwa 2012, ntchito yosindikiza Mabaibulo a Dziko Latsopano amene anatulutsidwa mu 1984 inayambika ku Ebina, Japan komanso ku Wallkill. Mabaibulowa anali ndi zikuto zakuda komanso zameruni, zomwe zinali zofewa koma zosawonongeka msanga. Koma poikira zikuto Mabaibulowa, makina atsopanowa anagwiritsa ntchito guluu ndi kansalu kenakake, zinthu zomwe sanazigwiritse ntchito pa Mabaibulo omwe anayesedwa aja. Choncho kansalu kameneka ndi guluu zinachititsa kuti Mabaibulowo apindike zikuto kwambiri. Zonse zimene anthu ogwira ntchito yokonza Mabaibulowo anachita pofuna kuthana ndi vutoli zinakanika, moti ntchitoyi inaima.
Kampani imene inapanga kansaluko inavomereza kuti kansaluko kakagwiritsidwa ntchito pamodzi ndi guluu popanga zikuto zofewa, pamakhala mavuto oti zikutozo zimapindika. Kampaniyo inavomerezanso kuti n’zovuta kwambiri kuthana ndi vuto limeneli. Koma a Mboniwo sanasinthe n’kuyamba kusindikiza Mabaibulo a zikuto zolimba. Iwo anayesetsabe kufufuza njira yoti asindikizire Mabaibulo a zikuto zofewa, omwe sangawonongeke msanga. Patapita miyezi 4 akuyesera njira zosiyanasiyana, anapeza kansalu kena komanso guluu wamtundu wina. Iwo anatulukira zoti ngati atagwiritsa ntchito zinthu zimenezi pokonza zikuto, zikutozo zingakhale zokongola, zofewa ndiponso sizingawonongeke msanga. Choncho ntchito yosindikiza Mabaibulo ija inayambikanso.
Ntchito Yosindikiza Mabaibulo Inaimitsidwanso
Mu September 2012, anthu omwe ankagwira ntchito yosindikiza Mabaibulo anauzidwa kuti ntchito yosindikiza Mabaibulo amene anatuluka mu 1984 iime kaye. Anauzidwanso kuti atumize kumipingo Mabaibulo onse amene analipo ndipo azidikirira zoti ayambe kusindikiza Baibulo la Dziko Latsopano, lomwe linakonzedwanso. Panakonzedwa zoti Baibulo latsopanoli litulutsidwe pa October 5, 2013, pamsonkhano wapachaka wa bungwe la Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania.
Pa August 9, 2013, anthu a Mboni amene akugwira ntchito kumalo osindikizira mabuku ku Wallkill ndi ku Ebina analandira mafailo a Baibulo loti asindikize. Iwo analandira mafailo a Baibuloli kudzera pa kompyuta, ndipo tsiku lotsatira, anayamba ntchito yosindikizayo. Anthuwo anamaliza kusindikiza komanso kuikira chikuto Baibulo loyamba pa August 15. Kenako kwa masiku 7 otsatira, anthuwo anagwira ntchito mwakhama, masana ndi usiku, n’cholinga choti akwanitse kusindikiza, kuikira zikuto, ndiponso kutumiza Mabaibulo oposa 1,600,000, omwe ankafunika kuti munthu aliyense amene angafike pamsonkhano wapachaka uja alandire.
Mabaibulo atsopanowa ndi okongola komanso olimba zedi. Koma chomwe chikuchititsa kuti Mabaibulowa akhale apadera kwambiri ndi uthenga wake, womwe ungathandize anthu kudzapeza moyo wosatha. Patangotha tsiku limodzi chilandirireni Baibuloli, mayi wina wa ku United States analemba kuti: “Panopa ndikumvetsa mawu a Mulungu mosavuta chifukwa ndikugwiritsa ntchito Baibulo latsopanoli.”