Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Laibulale ya M’thumba

Laibulale ya M’thumba

Pa October 7, 2013, a Mboni za Yehova anatulutsa pulogalamu yatsopano ya pa zipangizo za m’manja yotchedwa Laibulale ya JW. Pulogalamuyi ndi yaulere ndipo ingagwiritsidwe ntchito powerenga komanso pophunzira Baibulo. Mulaibulaleyi muli Mabaibulo osiyanasiyana okwana 6, monga King James Version, komanso Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika lachingelezi, lomwe linakonzedwanso mu 2013. *

N’chifukwa Chiyani Laibulaleyi Inapangidwa?

Masiku ano anthu ambiri akugwiritsira ntchito matabuleti kapena mafoni apamwamba potumizirana mauthenga kapena kulankhulana. Ndipo anthu amene amagwiritsira ntchito zipangizozi angapeze mabuku amene angawathandize kuphunzira Baibulo pa jw.org. Nanga n’chifukwa chiyani papangidwanso pulogalamu yatsopano ya Laibulale ya JW?

Choyamba, pulogalamu yatsopanoyi ikangoikidwa mufoni kapena muchipangizo china cham’manja, sipafunikanso kuilumikiza ku Intaneti. Chachiwiri, pulogalamuyi inapangidwa m’njira yothandiza munthu kupeza malemba mosavuta komanso kuphunzira Baibulo mozama. Kodi zimenezi zimachitika bwanji?

Laibulale ya JW ndi Yothandiza Kwambiri Pophunzira Baibulo

Pulogalamuyi ikangotsegula, imasonyeza maina amabuku a m’Baibulo. Mukasankha buku la m’Baibulo limene mukufuna kutsegula, mbali ina ya chipangizo chanu imaonetsa m’ndandanda wa machaputala a bukulo. Zimenezi n’zothandiza kupeza mavesi amene mukufuna mosavuta mwamsanga. Pulogalamuyi ili ndi zinthu zambiri zothandiza pophunzira Baibulo:

  • Mawu a m’munsi osonyeza njira ina imene mawu a m’mavesiwo angalembedwere komanso zinthu zina zothandiza zokhudzana ndi nkhaniyo.

  • Danga lapakati lokhala ndi mavesi a malifalensi.

  • Gawo lofufuzira limene lingasonyeze mawu onse amene ali ndi liwu lofanana ndi limene mukufufuza.

  • Kumayambiriro kwa buku lililonse la m’Baibulo kuli m’ndandanda wa nkhani zimene mungazipeze m’mabukuwo.

  • Bokosi losonyeza yemwe analemba buku la m’Baibulo lililonse, kumene linalembedwera, chaka chomwe linalembedwa komanso nthawi yomwe inadutsa kuti limalizidwe kulembedwa.

  • Gawo losonyeza zinthu zowala bwino monga mapu, matchati ndiponso zithunzi.

Mofanana ndi mabuku onse a Mboni za Yehova, munthu akhoza kupeza pulogalamu ya Laibulale ya JW popanda kuuzidwa kuchuluka kwa ndalama zoti apereke. Ndalama zonse zimene zinagwiritsidwa ntchito pokonza pulogalamuyi ndi zimene anthu amapereka mwakufuna kwawo. (2 Akorinto 9:7) Panopa mapulogalamu opitirira 1 miliyoni apangidwa kale dawunilodi. Nanunso tayesani kupanga dawunilodi laibulale ya m’thumba imeneyi kuti ikuthandizeni.

^ ndime 2 Mu January 2014, pulogalamuyi inakonzedwanso mwina ndi mwina ndipo anawonjezamo Lemba la tsiku ndiponso buku la nyimbo la Mboni za Yehova.