Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kugwiritsa Ntchito Zithunzi Pothandiza Anthu Owerenga Mabuku Athu

Kugwiritsa Ntchito Zithunzi Pothandiza Anthu Owerenga Mabuku Athu

Mabuku ambiri a Mboni za Yehova amakhala ndi zithunzi za mitundu yosiyanasiyana zimene zimafotokozera nkhani za m’mabukuwo. Koma m’mbuyomu, sikuti m’mabuku athu ambiri munkakhala zithunzi. Mwachitsanzo, magazini yoyambirira yachingelezi imene inkatchedwa kuti Zion’s Watch Tower, yomwe inatuluka chaka cha 1879, inalibe zithunzi. Kwa zaka zambiri mabuku athu ankangokhala ndi nkhani basi. Munkangopezeka chithunzi cha mtundu wakuda ndi woyera mwa apo ndi apo.

Masiku ano, m’mabuku athu mumakhala zithunzi zambiri. Zithunzi zambiri zimene mumaziona m’mabuku athu komanso pawebusaitiyi zimajambulidwa ndi akatswiri athu odziwa kujambula pamanja komanso ndi kamera. Akatswiriwa amafufuza mosamala kwambiri kuti ajambule zithunzi zophunzitsa zinthu zofunika kwambiri zokhudza mbiri yakale komanso mfundo zoona zimene Baibulo limaphunzitsa.

Mwachitsanzo taonani chithunzi chimene chasonyezedwa m’nkhaniyi, chomwe chikupezekanso m’mutu 19 wa buku lakuti ‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu.’ Chithunzichi chikusonyeza mzinda wakale wa Korinto. Mogwirizana ndi zimene chaputala 18 cha buku la Machitidwe chimanena, Paulo waimirira kumpando woweruzira milandu. Zimene akatswiri ofufuza zinthu zakale anapeza zinathandiza anthu amene anajambula chithunzichi kuti adziwe mmene malowo analili komanso mtundu wa miyala ya mabo imene anapangira malo oweruzira milandu, amene mwina Paulo anakaonekera pamaso pa Galiyo. Zimene akatswiri ofufuzawo anapeza zinathandizanso anthu ojambula zithunziwo kudziwa zinthu zina zokhudza zovala zimene anthu a ku Roma ankavala m’nthawi ya atumwi. N’chifukwa chake mukuona kuti Galiyo, yemwe akuoneka pakati pa chithunzicho, akuoneka atavala zovala zachifumu. Iye wavala mkanjo woyera wachifumu wokhala ndi mzera waukulu wapepo, komanso wakoleka nsalu yoyera paphewa lake yokhalanso ndi mzera wapepo. Wavalanso nsapato yooneka ngati jombo. Akatswiri ofufuza zinthu zakalewo ananena kuti Galiyo akakhala pampando woweruzira milandu womwe unkatchedwa kuti be’ma, ankayang’ana kumpoto chakumadzulo. Zimenezi zinathandiza ojambula kuona mbali yoti kuwala kuoneke kwambiri.

Kusunga Zithunzi Mwadongosolo

Zithunzi zimene zajambulidwa timazisunga mwanjira yakuti tisamavutike kuzipeza tikamafufuza nkhani kapena tikafuna kuzigwiritsanso ntchito m’mabuku ena. Kwa zaka zambiri m’mbuyomu, tinkasunga zithunzi zojambulidwa pamanja m’maenvelopu akuluakulu potengera mabuku amene munali zithunzizo. Zithunzi zojambulidwa ndi kamera zinkasungidwa potengera nkhani imene zithunzizo zikufotokoza. Chifukwa chakuti zithunzizi zinayamba kuchuluka, zinkakhala zovuta kupeza chithunzi chikakhala kuti chikufunika kuchigwiritsanso ntchito.

M’chaka cha 1991, tinamaliza kukonza pulogalamu ya pakompyuta yothandiza kosunga zithunzi komanso kuzipeza mosavuta ngati zikufunika. Mu pulogalamuyi, yomwe m’chingelezi imatchedwa kuti Image Services System, panopa tinasungamo zithunzi zoposa 440,000. Kuwonjezera pa zithunzi zimene zinatulutsidwa kale m’mabuku athu, mu pulogalamuyi munasungidwanso zithunzi masauzande ambiri zimene zidzagwiritsidwe ntchito m’tsogolo.

Mu pulogalamuyi mumasungidwanso zinthu zokhudza zithunzi monga nthawi komanso malo ojambulira, ndiponso mayina a anthu amene anajambulidwa. Zimenezi zimathandiza kuti tisamavutike kupeza chithunzi choyenerera chimene chinajambulidwa kale kuti chigwiritsidwenso ntchito m’buku latsopano.

Nthawi zina timapempha chilolezo choti tigwiritsire ntchito zithunzi zochokera ku mabungwe osiyanasiyana. Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti tikufuna chithunzi chosonyeza maring’i a pulaneti lotchedwa Saturn kuti tichigwiritse ntchito m’magazini ya Galamukani! Anthu amene ali m’dipatimenti yoona za zithunzi amafufuza chithunzi choyenera kenako amapempha chilolezo kwa amene anajambula chithunzicho. Poganizira za ntchito yathu ya padziko lonse yophunzitsa anthu Baibulo, ena amatiloleza kugwiritsa ntchito zithunzi zawo popanda kulipira. Ena amatiuza kuti tiwalipire kapena tilembe kuti chithunzicho anajambula ndi iwowo. Tikagwirizana, chithunzicho chimagwiritsidwa ntchito m’buku komanso timachisunga mu pulogalamu yathu yosungira zithunzi.

Masiku ano, mbali yaikulu m’mabuku athu ena imakhala ya zithunzi. Mwachitsanzo, pawebusaiti ino pamakhala nkhani zotchedwa Zithunzi Zofotokoza Nkhani za m’Baibulo. Tilinso ndi timabuku topezeka pawebusaiti komanso tosindikizidwa timene timakhala ndi zithunzi zosiyanasiyana monga kabuku kakuti Mverani Mulungu. Zinthu zimenezi zimatiphunzitsa mfundo zofunika kwambiri koma zimakhala ndi mawu ochepa. Mabuku athu onse komanso zinthu zina, kaya zofalitsidwa pawebusaiti ino kapena zochita kusindikizidwa, zimafotokoza nkhani za m’Baibulo.