Akulalikira Anthu Amitundu Yosiyanasiyana ku Canada
Ku Canada kuli mitundu yosiyanasiyana ya anthu amene anali oyambirira kukhala m’dzikoli ndipo amalankhula zilankhulo zoposa 60. Anthu pafupifupi 213,000 amanena kuti chimodzi mwa zilankhulozi ndi chawo chobadwira.
A Mboni ambiri aphunzira zilankhulozi n’cholinga choti azilalikira anthu amenewa mowafika pamtima. Ku Canada, a Mboni za Yehova anakonza makalasi ophunzitsa zilankhulozi. Ndiyeno pofika chakumapeto kwa 2015, a Mboni okwana 250 anali atamaliza kuphunzira chilankhulo china cha anthuwa.
A Mboni za Yehova anamasuliranso mabuku ofotokoza Baibulo komanso timavidiyo m’zilankhulo 8 za mitundu yoyambirira ya anthu a ku Canada. Zilankhulo zake ndi izi: Chialigonikwini, Chibulakifutu, Chikilii cha Kuchigwa, Chikilii cha Kudambo Lakumadzulo, Chiinukituti, Chimohaku, Chiodawa ndi Chiojibwa cha Kumpoto. *
Anthu amene anaphunzira zilankhulozi amati ndi zovuta. Mwachitsanzo munthu wina dzina lake Carma anati: “Nditangoyamba kugwira ntchito ndi anthu omasulira mabuku m’Chibulakifutu ndinkaona ngati wina wandiphimba m’maso. Ndikutero chifukwa chakuti sindinkadziwa bwino chilankhulochi ndipo sindinkatha kuchiwerenga kapena kumva bwinobwino anthu akamalankhula.”
Munthu wina dzina lake Terence, yemwe amagwira nawo ntchito yomasulira mabuku m’Chikilii, anati: “Mawu ambiri ndi aatali komanso ovuta kutchula.” Munthu winanso dzina lake Daniel, yemwe amagwira ntchito yolalikira nthawi zonse pachilumba cha Manitoulin ku Ontario, anati: “Palibe mabuku ambiri ophunzitsa chilankhulo cha Chiodawa. Ndiye ngati munthu akufuna kuchiphunzira ayenera kungopeza agogo enaake odziwa bwino chilankhulochi kuti amuphunzitse.”
Kodi khama la a Mboniwa limangopita pa chabe? Ayi. Tikutero chifukwa chakuti mayi wina wachiojibwa ananena kuti khama limene a Mboni za Yehova amachita limawasiyanitsa ndi anthu a zipembedzo zina. Iye ananenanso kuti a Mboni akapita kunyumba za anthu n’kuwawerengera Malemba m’Chiojibwa, anthuwa amamasuka ndipo amafuna kumvetsera uthenga wa m’Baibulo.
Munthu wina dzina lake Bert anakulira kumalo a anthu achibulakifutu m’dera la Alberta. Iye anati: “Ndaonapo anthu angapo achibulakifutu akukumbatira mabuku achilankhulochi n’kunena kuti, ‘Bukuli analembera ineyo chifukwa lili m’chilankhulo changa.’ Ndaonaponso anthu ambiri misozi ikulengeza m’maso mwawo chifukwa choonera vidiyo yachilankhulo chawo.”
Mayi wina wolankhula Chikilii anasangalala kwambiri ataonera vidiyo yakuti, N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo? m’chilankhulo chake. Iye ananena kuti zinali ngati mayi ake akumulankhula.
Amayenda Maulendo Aatali Kuti Akalalikire
A Mboni ambiri amayesetsa kuti apite kumadera kumene kuli anthu amitundu yoyambirirawa kuti akawauze uthenga wolimbikitsa wa m’Baibulo. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Terence ndi mkazi wake dzina lake Orlean. Iwo anapita kudera lina kukalalikira ndipo anati: “Tinapita anthu angapo ndipo tinayenda m’misewu yovuta kwa maola 12 kuti tikalalikire kudera lina la anthu achiwojibwa. Anthuwo anasangalala kwambiri kumva uthenga wa m’Baibulo.”
Anthu ena anasamuka kunyumba zawo zabwino kupita kumadera a anthu azilankhulozi. Mwachitsanzo, bambo wina dzina lake Daniel ndi mkazi wake LeeAnn anakalalikira pachilumba cha Manitoulin kwa miyezi itatu. Atachita zimenezi, anasankha kuti angosamukira komweko. Daniel anati: “Timasangalala kuti panopa tili ndi nthawi yambiri yoti tidziwane ndi anthu a kuno ndiponso kuwathandiza kuti aziphunzira Baibulo.”
“Chifukwa Chakuti Ndimawakonda Kwambiri”
N’chifukwa chiyani a Mboni za Yehova akuyesetsa kulalikira anthu amitundu yosiyanasiyanawa? Mkazi wa Bert dzina lake Rose anati: “Ndine mmodzi mwa anthu amitundu yoyambirirawa ndipo ndaona ndekha kuti kutsatira mfundo za m’Baibulo n’kothandiza kwambiri. Izi zimandilimbikitsa kuti ndizithandizanso anthu ena.”
Orlean anati: “Ndimafuna kuti anthu olankhula Chikilii aphunzire za Mlengi wathu n’kumalola kuti aziwatsogolera. Ndi mwayi waukulu kwambiri kuwathandiza kuti akhale pa ubwenzi wolimba ndi Yehova komanso kuti aphunzire zimene angachite pothana ndi mavuto awo.”
Munthu wina dzina lake Marc amayesetsa kuthandiza anthu olankhula Chibulakifutu ndipo amamasulira nawo mabuku m’chilankhulochi. Koma n’chifukwa chiyani amachita zimenezi? Iye anayankha kuti: “Chifukwa chakuti ndimawakonda kwambiri.”
^ ndime 4 Anthu ena a ku United States amalankhulanso zina mwa zilankhulo zimenezi.