Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

“Mphatso Yochokera kwa Mulungu” Pachionetsero cha ku Treasure City

“Mphatso Yochokera kwa Mulungu” Pachionetsero cha ku Treasure City

Mzinda wa Cluj-Napoca, ndi umodzi mwa mizinda ikuluikulu m’dziko la Romania ndipo umadziwika kuti ndi Mzinda Wachuma (The Treasure City). Pa chionetsero cha mabuku chomwe chinachitika ku Gaudeamus kuyambira pa 20 mpaka 24 April, 2016, a Mboni za Yehova anathandiza anthu kuzindikira mfundo za makhalidwe abwino zomwe zimapezeka m’Baibulo. Iwo anapeza malo oikapo mabuku ndipo anakambirana ndi anthu ambiri amene ankachita chidwi ndi mavidiyo omwe ankaonetsedwa, mabuku komanso Mabaibulo omwe anasanjidwa pashelefu yawo.

Masukulu ambiri anabwera ku chionetserochi ndipo aphunzitsi ankabwera ndi ana a sukulu awo pamene panali a Mboni. Ana ambiri anasangalala kuonera mavidiyo akuti Khalani Bwenzi la Yehova, komanso ambiri ankafuna buku lakuti Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo ndiponso kabuku kakuti Phunzitsani Ana Anu. Mayi wina amene amagwira ntchito yosamalira ana ataona mavidiyo akuti Khalani Bwenzi la Yehova anauza mnzake wina wakuntchito kuti, “Tilembe dzina la webusaitiyi [www.pr418.com] kuti tizikaonetsa ana mavidiyo amakatuniwa.”

Nawonso achinyamata amene anabwera kuchokera m’masukulu osiyanasiyana anachita chidwi ndi mavidiyo amakatuni a achinyamata omwe ankaonetsedwa pa matabuleti. Ena mwa mavidiyo amene amaonetsedwa ndi monga Kodi ndi Chikondi Chenicheni Kapena Kungotengeka Maganizo?, Kodi Mungatani Kuti Anzanu Asiye Kukuvutitsani?, ndi yakuti Muzichita Zinthu Mwanzeru Mukamacheza ndi Anzanu pa Intaneti.

Wansembe wina wa tchalitchi cha Orthodox ndi mkazi wake anabwera maulendo angapo pamalo amene a Mboni anaika mabuku ndipo anatenga Baibulo la Dziko Latsopano ndi timabuku tina. Wansembeyu ananena kuti anachita chidwi kwambiri ndi gawo la “Kalozera wa Mawu wa M’Baibulo” komanso kuti pomasulira Baibuloli anafufuza m’zinthu zambiri zomwenso ndi zodalirika. Wansembeyu anapatsa a Mboni nambala yake ya foni ndipo anawauza kuti azimuimbira kuti apitirize kukambirana naye nkhani za m’Baibulo.

Kenako mkazi wake anafunsa kuti nkhani zokhudza ana angazipeze pati pawebusaiti ya jw.org ndipo a Mboniwo anamusonyeza gawo la “Ana” pawebusaitiyi. Nthawi yomweyo anaonera vidiyo yakuti Uzinena Zoona ndipo anasangalala kwambiri. Pambuyo poona zinthu zosiyanasiyana pawebusaitiyi, wansembe uja ananena kuti webusaitiyi ndi “mphatso yochokera kwa Mulungu.”