Anthu Oyambirira Kukhala ku America Anachita Chikondwerero ku New York
Anthu ambiri amaganiza kuti panopa anthu oyambirira kukhala ku America amakhala kumadera akumidzi. Komatu anthu 7 pa 10 alionse amitunduyi amakhala m’mizinda. Mumzinda wa New York, womwe ndi mzinda waukulu ku United States, munachitika chikondwerero cha anthu amenewa kuyambira pa June 5 mpaka 7, 2015. A Mboni za Yehova ena amumzindawu atadziwa za chikondwerero chimenechi anayamba kukonzekera kuti apite. Kodi n’chifukwa chiyani ankafuna kukakhala nawo pachikondwererochi?
A Mboni za Yehova amamasulira mabuku ofotokoza Baibulo m’zilankhulo zambiri, kuphatikizapo zilankhulo za anthu oyambirirawa monga Chibulakifutu, Chidakota, Chihopi, Chimohaku, Chinavaho, Chiodawa ndi Chikilii cha Kuchigwa. Pachikondwererochi a Mboni anaika ena mwa mabukuwa pamatebulo. Chinthu china chimene anaikapo ndi kapepala kothandiza anthu kuti azikhulupirira kuti kuli Mlengi.
Webusaiti yathu imakhalanso ndi mavidiyo ndiponso zinthu zina zongomvetsera za m’zilankhulozi. Pachikondwererochi a Mboni anaika zinthuzi kuti anthu amvetsere. Anthuwa anasangalala ndi zimenezi chifukwa zinthu zambiri zimene ena anabweretsa zinali m’Chingelezi kapena Chisipanishi basi.
Anthu ambiri amene anapezekako anachita chidwi kwambiri ndi khama lathu lomasulira mabuku m’zilankhulo zambiri za anthu oyambirira kukhala ku America. Anachitanso chidwi ndi ntchito yathu yolalikira imene timagwira m’mizinda ikuluikulu komanso kumadera akumidzi. Bambo wina atadziwa za ntchito yathu anapempha kuti tiziphunzira naye Baibulo. Iye anati: “Ndikufunitsitsa kuti mudzabwere kwathu kuti mudzandithandize kuphunzira Baibulo.”
Banja lina linapita pamene panali a Mboniwo koma sankatha kumvana chifukwa banjalo lili ndi vuto losamva. Koma kenako kunabwera wa Mboni wina amene amadziwa chinenero chamanja. Iye anacheza ndi banjali kwa maminitsi pafupifupi 30 ndipo anawathandiza kuti adziwe kumene kudzakhale msonkhano wa Mboni za Yehova wa chinenero chamanja pafupi ndi kwawo.
A Mboni za Yehova oposa 50 anapita kuchikondwerero cha masiku atatu chimenechi kuti akathandize anthu kudziwa zimene Baibulo limanena. Anthu analandira zinthu monga mabuku ndi timapepala zoposa 150.