Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Ku France Kunachitika Chionetsero Chapadera cha Baibulo

Ku France Kunachitika Chionetsero Chapadera cha Baibulo

Mumzinda wa Rouen womwe uli kumpoto kwa dziko la France munachitika chionetsero cha 2014 cha zinthu za m’mayiko osiyanasiyana. Anthu ambiri amene anapita kuchionetserochi anachita chidwi kwambiri ndi malo ena omwe analembapo kuti “Baibulo ndi Lothandiza Kuyambira Kale, Panopa Komanso M’tsogolo.”

Panja pa malowa anaikapo ma TV akuluakulu ndipo ankaonetsa vidiyo ya mipukutu yakale ya Baibulo. Anthu ambiri ankachita chidwi ndi vidiyoyi. Ndipo akalowa ankawafotokozera mfundo za m’Baibulo, mbiri yake, mmene lilili lolondola pa nkhani za sayansi komanso kuti ndi buku lomwe lafalitsidwa kwambiri kuposa buku lina lililonse.

Pakhoma la pamalowa analembapo zomwe zinathandiza kuti Baibulo litetezedwe. Analembaponso zinthu zosonyeza kuti panopa Baibulo likupezeka m’njira zosiyanasiyana komanso kuti anthu ambiri akhoza kukhala ndi Baibulo lochita kusindikiza kapena pazipangizo zawo zamakono. Amene anafika pamalowa anapatsidwa Baibulo la Dziko Latsopano kwa ulere. Baibuloli linakonzedwa ndi a Mboni za Yehova ndipo likupezeka m’zinenero zoposa 120.

Anthu omwe anabwera pa chionetserochi anathokoza kwambiri a Mboni za Yehova chifukwa chothandiza anthu ambiri kupeza Baibulo m’njira zosiyanasiyana. Mayi wina amene amagwira ntchito yoyang’anira achinyamata atafika pamalowa ndi gulu la achinyamata, ananena kuti: “Baibulo ndi mphatso yathu ya mtengo wapatali ndipo ndi lothandiza kwambiri. Nthawi iliyonse ndikaliwerenga, ndimapeza njira yothetsera mavuto anga.”

Mayi wina wazaka 60 anadabwa atauzidwa kuti atha kutenga Baibulo kwa ulere. Mayiyu anati: “Aliyense ayambe kuwerenganso Baibuloli chifukwa ndi lothandiza.”