Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Anthu Okonda Mtendere Anasonkhana pa Mwambo wa Armada

Anthu Okonda Mtendere Anasonkhana pa Mwambo wa Armada

Kuyambira pa June 6 mpaka pa 16, 2013, anthu ochokera m’mayiko osiyanasiyana anasonkhana kudoko la Rouen kumpoto kwa dziko la France. Anthuwa anasonkhana pa mwambo wosangalatsa komanso waukulu kwambiri wotchedwa Armada.

Sitima zapamadzi zitalizitali komanso zokongola kwambiri padziko lonse zinayenda ulendo wamakilomita 120 mumtsinje wokhotakhota wa Seine m’tawuni yokongola ya Normandy. Sitimazi zinkapita kumwambo wapadera kwambiri ndipo zinafika padokoli omwe ndi lalitali makilomita 4. Kwa masiku 10, anthu amene anabwera ku mwambowu anali ndi mwayi wapadera wokaona kwa ulele mkati mwa sitima zakale komanso zazitali kwambirizi, zimene zinafika pa mwambowu.

Kodi n’chiyani chinachititsa anthu a misinkhu yosiyanasiyana kupita kumwambo wa Armada? Munthu amene anayambitsa mwambowu anafotokoza kuti, “anthu amakhala ndi mwayi woona sitima zikuluzikulu pa mwambo wa Armada.” Kunena zoona, anthu ambiri amene amafika ku mwambowu, ana ndi akuluakulu omwe, akaona sitimazi amaganizira za maulendo ataliatali ndiponso ufulu wawo.

Komanso anthu masauzande ambiri amene anabwera ku mwambowu anali ndi mwayi womva za mtundu wina wa ufulu, umene munthu amaupeza akadziwa zinthu zoona zimene Baibulo limaphunzitsa. (Yohane 8:31, 32) Pamene ankaona malo m’tawuni yokongola ya Rouen komanso kudutsa m’misewu yake ing’onoing’ono, alendowo ankaonanso mabuku a Mboni za Yehova amene anayalidwa pamatebulo a matayala. Alendowa akafika pamatebulo amabuku, ankapatsidwa buku lina lililonse limene ankafuna kwa ulele. Anthu ambiri odutsa ankachita chidwi ndi nkhani ya m’magazini ya Nsanja ya Olonda ya mutu wakuti, “Kodi Tsankho Lidzatha Liti?” Anthuwo anapemphedwanso kukamvetsera nkhani ya m’Baibulo m’Chifulenchi, m’Chingelezi ndi m’Chisipanishi.

Anthu ambiri anayamikira kwambiri zimene a Mboniwa anachita, moti munthu wina amene anaona koyamba a Mboni ali ndi tebulo lamabuku ananena kuti: “Ndasangalala kwambiri kukuonani muli m’mbali mwa msewu. Ndimalemekeza anthu amene amayesetsa kutsatira zimene amakhulupirira ngakhale kuti sindine wa Mboni.” Ndiponso anthu ena awiri achikulire anakumana ndi achinyamata a Mboni amene ankagwira nawo ntchito yolalikirayi. Anthuwo anauza anyamata a Mboniwo kuti: “Muzinyadira ntchito yanuyi.”