Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Ntchito Yolalikira Mwapadera Inayenda Bwino ku Lapland

Ntchito Yolalikira Mwapadera Inayenda Bwino ku Lapland

M’madera ambiri a ku Finland, Norway, ndi Sweden, kumapezeka anthu a mtundu wa Saami omwe ali ndi chikhalidwe, miyambo, komanso zilankhulo zawo. A Mboni za Yehova posachedwapa anachita zinthu ziwiri pofuna kulalikira uthenga wa m’Baibulo kwa a Saami.

Choyamba, mu nyengo yozizira ya mu 2015, a Mboni anayamba kupanga mabuku ndi mavidiyo ofotokoza nkhani za m’Baibulo a m’chinenero cha Saami. * Chachiwiri, pa ntchito yapadera yolalikira yomwe inachitika mu 2016 ndi mu 2017, a Mboni za Yehova anapita ku Lapland lomwe ndi dera lakutali komwe nyama zotchedwa mphalapala zimangoyendayenda. Iwo anagwiritsa ntchito nkhani zomwe anamasulira polalikira kwa anthu a mtundu wa Saami.

“Ntchito yofunika kwambiri kwa anthu a m’dera lino”

Pa ntchito yapadera yolalikira yomwe inachitika mu May 2017, a Mboni oposa 200 a ku Finland, Norway, ndi Sweden anadzipereka kupita m’midzi yambiri ing’onoing’ono yomwe ili m’madera otalikirana makilomita masauzande ambiri ku Lapland. Pokonzekera, a Mboni ena anaphunzira mawu a chilankhulo cha Saami ndipo zimenezi zinasangalatsa kwambiri anthu a mtundu wa Saami. A Denis omwe anapita kumudzi wotchedwa Karigasniemi anati: “Anthu a m’mudzimo anatiyamikira chifukwa choyesetsa kulankhula chilankhulo chawo ndipo anazindikira kuti chidwi chathu chinali chochokera pansi pamtima.”

Chifukwa choti anthu a mtundu wa Saami amakonda kwambiri chilengedwe ndi nyama zakutchire, iwo anayamikira kwambiri lonjezo la m’Baibulo lokhudza dziko lapansi la paradaiso. (Salimo 37:11) Mwachitsanzo, mzimayi wina wa mtundu wa Saami atayamba kuphunzira Baibulo pogwiritsa ntchito kabuku kakuti Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu n’kudziwa zimene Mulungu adzachitira mtundu wa anthu, mokuwa anadabwa kwambiri kuti n’chifukwa chiyani m’busa wa ku tchalitchi chake sanamuuzepo zokhudza dziko lapansi la paradaiso.

Anthu ambiri anayamikira a Mboni chifuwa chopita kukawayendera. Munthu wina wabizinesi anayamikira a Mboni ena awiri omwe anawaona. Iye anauza a Mboniwo kuti ankagwira ‘ntchito yofunika kwambiri kwa anthu a m’deralo’ ndipo anawauza kuti apite ku malo ake a bizinesi kuti akatenge chakudya chilichonse chomwe ankafuna. Wabizinesiyo anakakamira kuti ndalama za chakudyacho alipira ndi iyeyo.

Pa ntchito yolalikira yapaderayo, anthu a mtundu wa Saami anaonera mavidiyo pafupifupi 180 komanso anatenga mabuku ndi zinthu zina zoposa 500. Nthawi zambiri iwo ankapempha kuti awapatse buku lililonse la m’chilankhulo chawo. Kuonjezera pamenepo, anthu 14 a Chisaami anayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova.

“Amamasuliridwa ndi akatswiri odziwa bwino ntchito yawo”

Anthu ambiri omwe anawerenga mabuku a Mboni za Yehova anayamikira kuti mabukuwo anamasuliridwa bwino kwambiri. Bambo Nilla Tapiola omwe ndi mphunzitsi komanso membala wa gulu lomwe limayendetsa ntchito za nyumba ya malamulo ya Saami, ananena kuti: “Mabuku anu amamasuliridwa bwino kwabasi.” Iwo anafotokoza kuti mabukuwo “ndi osavuta kuwerenga komanso amalembedwa mogwirizana ndi malamulo a chilankhulo.” Bambo wina wa mtundu wa Saami yemwe amakhala kumpoto kwenikweni kwa Finland ananena kuti: “Mabukuwa amamasuliridwa ndi akatswiri odziwa bwino ntchito yawo.”

Ku Karigasniemi, pa malire a Finland ndi Norway, a Mboni anakambirana phunziro 1 m’kabuku kakuti Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu ndi mphunzitsi wina wa mtundu wa Saami. Posangalala ndi mmene kabukuko kanamasuliridwira, mphunzitsiyo anapempha chilolezo kwa a Mboniwo kuti akagwiritse ntchito kabukuko kuphunzitsira ana chilankhulo cha Saami kusukulu.

Mavidiyo ambiri ndi timapepala komanso kabuku kamodzi zinamasuliridwa m’chilankhulo cha Saami. Webusaiti ya jw.org ya chilankhulo cha Saami yakhala ikugwira ntchito kuyambira pa 29 February, 2016. Anthu olankhula Chisaami amalowa pawebusaitiyi maulendo oposa 400 pamwezi komanso amapanga dowunilodi mavidiyo, zinthu zongomvetsera ndi zinthu zina pafupifupi 350.

Anthu a mtundu wa Saami komanso a Mboni amene anakawayendera anthuwo, ananena kuti analimbikitsidwa ndi ntchito yapadera yolalikirayo. A Henrick ndi a Hilja-Mariai omwe anapita kumudzi wotchedwa Utsjoki, ananena kuti anthu a m’midzi imene a Mboni anakalalikirako ankatha “kuona kuti Baibulo limathandiza anthu a mtundu wa Saami m’njira zambiri.” Nawonso a Lauri ndi a Inga omwe anapitanso ku Utsjoki anati: “Ntchito yolalikirayi yatikumbutsa kuti Mulungu alibe tsankho. Ndife osangalala kuti tasonyeza chikondi chake kwa anthu omwe amakhala m’madera akutaliwa.”

^ ndime 3 Pali zilankhulo zambiri za Chisaami (kapena kuti Chisami). Buku la Encyclopædia Britannica linanena kuti “Chilankhulo chachikulu kwambiri cha North Sami chimalankhulidwa ndi anthu awiri pa anthu atatu alionse a mtundu wa Sami.” A Mboni za Yehova amamasulira mabuku ndi zinthu zina m’chilankhulo cha North Saami. M’nkhani ino, mawu oti “Saami” akuimira chilankhulo chimene anthu ambiri akumeneko amalankhula.