A Mboni za Yehova a ku Hungary Anayamikiridwa Chifukwa Chothandiza Kuti Madzi Asasefukire
Mu June 2013, mvula yochuluka kwambiri inapangitsa kuti mitsinje ya m’mayiko a m’chigawo chapakati ku Ulaya isefukire. M’dziko la Hungary, Mtsinje wa Danube unadzaza kwambiri ndipo aka kanali koyamba kuti udzaze choncho.
Zinthu zitafika poipa choncho, Unduna Woona za Moyo wa Anthu ku Hungary unapempha ofesi ya Mboni za Yehova ya m’dzikolo kuti ithandize pa ntchito yoteteza kuti mtsinje wa Danube usasefukire. A ku ofesi ya Mboniyo anapempha a Mboni a m’mipingo yapafupi ndi mtsinjewo kuti agwire nawo ntchito yoteteza kuti madzi asasefukire yomwe inakonzedwa ndi akuluakulu a m’dzikolo.
A Mboni atamva anadzipereka ndi mtima wonse kukagwira nawo ntchitoyi moti m’mawa wake a Mboni oposa 900 ochokera m’mipingo 72 anakagwira nawo ntchito yoika zinthu m’mbali mwa mtsinje wa Danube kuti usasefukire. Anthuwa anauzidwa kuti avale baji yolembedwa kuti “Mboni za Yehova” komanso dzina lawo ndi la mzinda umene achokera.
Woimira bungwe la Red Cross mumzinda wina, anatumiza uthenga wotsatirawu ku mpingo wina wa Mboni za Yehova: “Anthu inu ndi oyenera kukupatsani ulemu ndipo tikukuthokozani kwambiri chifukwa cha kugwira ntchitoyi modzipereka komanso mogwirizana. Munayenda mtunda wautali kudzagwira ntchitoyi zomwe si zophweka. Tisaname zoterezi zimasowa. Ndikumangokhalira kunena zabwino za inu mumzinda mwathu.”
Tcheyamani wa bungwe lothandiza anthu pa zinthu zogwa mwadzidzidzi, yemwenso ndi membala wa ku nyumba ya malamulo ya m’dziko la Hungary analembera kalata a Mboni za Yehova yowathokoza chifukwa cha ntchito yotamandika yomwe anagwira.