A Mboni za Yehova Anagwira Ntchito Yosesa Mumzinda wa Rostov-on-Don
Pa 20 May 2015, mkulu woyang’anira mzinda wa Rostov-on-Don womwe ndi mzinda waukulu kwambiri kum’mwera kwa dziko la Russia, analemba kalata yoyamikira Mboni za Yehova. Mkuluyu anayamikira a Mboniwo chifukwa chogwira nawo ntchito yosesa mumzindawo.
Pa nthawi imene anthu a mumzindawu amakonza komanso kusesa mumzinda wa Rostov-on-Don, a Mboni za Yehova ochokera m’mipingo 4 anachotsa zinyalala zomwe zinali m’njira komanso m’mbali mwa mitsinje. M’maola ochepa okha, a Mboniwo anadzaza zinyalala m’matumba 300 omwe anakatayidwa pogwiritsa ntchito thiraki.
N’chifukwa chiyani a Mboni za Yehovawa anadzipereka chonchi? Mayi ena a zaka 67 dzina lawo a Raisa ananena kuti: “Inenso ndimaona kuti n’zofunika. Ndikufuna kuti mzinda wathu uzikhala waukhondo kuti aliyense azikhala m’dera losamalidwa bwino. Ndasangalala kwambiri kugwira nawo ntchitoyi ngakhale kuti ndi anthu ochepa amene angayamikire zomwe tachitazi. Komabe, Yehova waona zomwe tachita.” Bambo wina dzina lake Aleksander, anafotokozanso kuti: “Sikuti timangolalikira anthu, koma timagwiranso ntchito zina zothandiza anthuwo. Ndimamva bwino kwambiri ndikachita zinthu zinazake zothandiza anthu a m’dera lathu.”
Anthu omwe anaona a Mboni za Yehova akugwira ntchitoyi, anayamikira kwambiri kudzipereka kwawo. Munthu wina wa mumzindawo anadabwa atamva kuti a Mboniwo anangodzipereka kugwira ntchitoyo kwaulere. Kenako munthuyo anaganiza zogwira nawo ntchitoyo ndipo pamapeto pake ananena kuti: “Sindinkaganiza kuti kugwira ntchitoyi kungakhale kosangalatsa chonchi. Ndipo n’zodabwitsa kuti ambirinu simukhala mumzinda uno koma mwabwera kudzatithandiza.”
Mmodzi wa akuluakulu a mzindawo anaona kagulu kena ka a Mboni katasonkhanitsa matumba ambiri a zinyalala. Mkuluyo anajambula a Mboniwo ataima pafupi ndi matumba odzaza ndi zinyalalawo kuti akaonetse anthu ena ngati chitsanzo.