Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kuthana ndi Tsankho

Kuthana ndi Tsankho

A Mboni za Yehova amakhulupirira zoti Mulungu amaona kuti mitundu yonse ya anthu ndi yofanana. (Machitidwe 10:​34, 35) Pogwiritsa ntchito Baibulo, timathandiza anthu kuthana ndi tsankho ngakhale atakhala kuti poyamba anali atsankho kwambiri.

Komanso sitichita nawo ziwawa kapena zionetsero zosonyeza kudana ndi mtundu kapena anthu ochokera kumayiko ena. Mwachitsanzo, m’nthawi imene chipani cha Nazi chinkazunza anthu, a Mboni za Yehova ku Germany komanso m’mayiko ena anakana kuzunza nawo anthu a mitundu ina Hitler atalamula. A Mboni ambirimbiri anaphedwa chifukwa chokana kuzunza anthu a mitundu ina.

Chitsanzo china ndi cha zimene zinachitika pa nkhondo yapachiweniweni imene inachitika ku Rwanda m’chaka cha 1994. A Mboni sanalowerere nkhondoyo ndipo ena anaphedwa kumene chifukwa choteteza anthu a mitundu ina amene ankafuna kuphedwa.

Popeza timafunitsitsa kuthandiza anthu a mitundu yonse, timasindikiza komanso kugawira mabuku ofotokoza nkhani za m’Baibulo m’zinenero pafupifupi 600. Ndipotu m’mipingo mwathu timalandira anthu a “m’dziko lililonse, fuko lililonse, mtundu uliwonse, ndi chinenero chilichonse.”​—Chivumbulutso 7:9.