A Mboni ku Italy Anathandiza Anthu a M’dera Lawo
Chakumapeto kwa November 2016, m’tauni ya Moncalieri munagwa mvula yamphamvu ndipo zimenezi zinachititsa kuti madzi asefukire m’midzi ina yomwe ili kum’mwera kwa tauniyi. M’madera ena, madzi anachuluka kupitirira hafu mita kuya kwake. Nyuzipepala ina inati: “Madziwa anafika paliponse ndipo anakhudza aliyense.” Anthu pafupifupi 1,500 anasamutsidwa mwamsanga ndi akuluakulu a m’derali ndipo palibe amene anafa chifukwa magulu opulumutsa anthu anafika mofulumira ku malowo. Komabe katundu wa mabanja ambiri anawonongeka.
Anagwira Ntchito Mogwirizana Pothandiza Anthu Okhudzidwa
Ngoziyi itangochitika, a Mboni a m’derali anayamba kuthandiza anthu okhudzidwa nthawi yomweyo. Iwo anayamba kuchotsa matope ndi zinyalala m’nyumba za anthu omwe anakhudzidwawo komanso kupulumutsa katundu wa m’nyumba ndi zinthu zina. Gulu lina linkapita kukapereka chakudya ku banja lina lomwe linakhudzidwa ndi ngoziyo, komanso linanyamula zida zoti likagwiritse ntchito pothandiza banjalo, koma linapeza kuti msewu watsekedwa kuti anthu asadutse. Anthu omwe ankayang’anira pamalopo anawalola kuti adutse n’cholinga choti akathandize banjalo. A Mboni anathandiza a Mboni anzawo omwe anakhudzidwa ndi ngoziyo komanso anthu a zipembedzo zina.
Mwachitsanzo, zipinda za nyumba ina zomwe zili pansi panthaka zinadzadza ndi madzi. Opulumutsa anthu atamaliza kupopa madziwo, gulu la Mboni za Yehova linathandiza a Antonio omwe ndi a Mboni limodzi ndi banja lawo kuchotsa zinyalala m’chipinda chawo. Kenako a Mboniwo anathandizanso anthu ena omwe ankakhala m’nyumbayo. Iwo anaima pamzere n’kumapatsirana zinyalalazo ndipo pasanathe nthawi yaitali, anamaliza kuyeretsa zipinda zonse. Aliyense anayamikira kwambiri a Mboniwo chifukwa chowathandiza. Mayi wina dzina lake Viviana yemwe amakhalanso m’nyumbayo, anapita kwa mkazi wa a Antonio misozi ikulengeza m’maso n’kumuuza kuti: “Chonde mutithokozere kwa a Mboni anzanuwo, ndinu anthu abwino kwambiri.”
Anthu a m’mudzi wina womwe unakhudzidwa kwambiri ndi madzi osefukirawo, anaona a Mboni akuthandiza anthu omwe anakhudzidwa ndi kusefukira kwa madziku. Chifukwa chochita chidwi ndi zimene a Mboniwo ankachita, anthuwo anadzipereka kuti athandize nawo pa ntchitoyo ndipo ankatsatira malangizo a amene ankatsogolera ntchitoyo.
Anayamikira Chifukwa Anathandizidwa Kwambiri
Nyumba ya bambo wina inawonongeka kwambiri ndipo galaja yake inamira m’matope. A Mboni 8 anagwira ntchito yochotsa zinyalala m’galajayo kwa maola 4 mosalekeza, ndipo zimenezi zinadabwitsa kwambiri bamboyo. Poyamikira zimene a Mboniwo anamuchitira, bamboyo anakumbatira ena mwa anthuwo komanso analemba uthenga pamalo ochezera a pa intaneti woyamikira a Mboniwo chifukwa chomuthandiza kwambiri.
Bambo wina wa Mboni anati: “Tinathandiza anthu ambiri omwe si a Mboni ndipo ambiri mwa anthuwo ndi a zaka za m’ma 80. Ena mwa anthuwo ankagwetsa misozi pamene ankayamikira zimene tinawachitira.” Munthu wina yemwe ndi wodzipereka kwambiri pa tchalitchi cha Katolika m’derali anayamikira a Mboniwo chifukwa chogwira ntchito yothandiza anthu. Iye anati: “Zinali zosangalatsa kwambiri kuona tikuthandizana ngakhale kuti ndife osiyana zipembedzo.” Bambo wina anati: “Pepani kuti anthu amangokudziwani kuti mumalalikira m’nyumba zawo Lamlungu lililonse m’mawa basi, koma sadziwa kuti mumathandizanso anthu.”