Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

A Mboni za Yehova Analandira Ulemu Chifukwa Chothandiza Akaidi

A Mboni za Yehova Analandira Ulemu Chifukwa Chothandiza Akaidi

Anthu 9 a Mboni za Yehova ku Australia, anapatsidwa masatifiketi a ulemu chifukwa chogwira ntchito yotamandika kwambiri yothandiza anthu omwe anamangidwa chifukwa cholowa m’dzikolo mopanda chilolezo. Anthuwa akusungidwa ku malo ena aakulu kwambiri m’dzikolo. Bungwe lina loyang’anira anthu oterewa lomwe lili pafupi ndi mzinda wa Derby kum’mwera kwa dziko la Australia, ndi lomwe linapereka masatifiketi aulemuwo.—Curtin Immigration Detention Centre *

Mlungu uliwonse, a Mboniwo amapita kukacheza komanso kukakambirana ndi anthuwo mfundo za m’Baibulo pofuna kukawalimbikitsa. Bambo Christopher Riddoch, omwe amalankhula ndi anthu pa nkhani zachipembedzo ndi za chikhalidwe pamalowa anati: “Anthuwa sachedwa kusintha chifukwa chocheza ndi a Mboniwa.” Bambowa anapitiriza kunena kuti: “A Mboni akayamba kucheza ndi anthuwa nkhawa zawo zimachepa mofulumira ndipo amayamba kukhala osangalala. N’zosangalatsa kuti a Mboni amaona kuti anthuwa ndi ofunika kwambiri ndipo amawaganizira.”

Bambo Riddoch ananenanso kuti a Mboniwo anapatsidwa masatifiketiwo n’cholinga chowathokoza chifukwa cha ntchito yawo yosintha miyoyo ya anthu omwe akuwasamalira. Bambowa ananenanso kuti mosakaikira mabanja ndiponso mipingo ya a Mboniwa inanyadira kudziwa kuti a Mboni anzawo achita zinthu zotamandika.

^ ndime 2 Malowa kungathe kukhala amuna 1,500.