Munthu Wina Anapulumutsidwa Akufuna Kudzipha Pansanja ya Sky Tower
Bambo wina wa zaka 80 dzina lake Graham Browne, yemwe ndi wa Mboni za Yehova, anathandiza munthu wina kuti asadziphe. Munthuyu amadwala matenda ovutika maganizo, ndipo ankafuna kuti adziponye kuchokera pansanja yaitali mamita 328, yotchedwa Sky Tower, yomwe ili ku Auckland m’dziko la New Zealand. Bambo Graham ananena kuti: “Munthuyu anauza apolisi kuti akufuna kulankhula ndi munthu wa Mboni za Yehova ndipo apolisiwo anandipempha kuti ndikalankhule naye.
“Anthu ogwira ntchito ku Sky Tower anandiveka zovala zothandiza kupewa ngozi komanso anamanga Baibulo langa ndi chingwe chachitali. Kenako apolisi anandikweza pakhonde la nsanjayo, lomwe anthu amakwerapo kuti aziona kutali ndipo lili ndi kampanda kotchinga m’mbali mwake. Khondeli lili m’mwamba kwambiri, mamita 192 kuchokera pansi. Pakhondepo pankaomba mphepo yamphamvu komanso yozizira kwambiri. Munthu amene ankafuna kudziponya pansiyo anakhala chapafupi ndithu ndi pamene ndinali ndipo anakhala m’kanjira, mphepete mwenimweni mwa khondelo, miyendo yake ili lendelende.
“Ndinakuwa kuti ndine wa Mboni za Yehova ndipo ndimafuna kumuthandiza. Kenako nditapemphera chamumtima, ndinatsegula Baibulo n’kuyamba kulankhula.
“Ndinamuuza nkhani yokhudza kupatulika kwa moyo, yomwe ndinali nditaikamba chaposachedwa ku Nyumba ya Ufumu yathu.
“Kenako ndinamuuza kuti, ‘Mulungu amakuona kuti ndiwe wofunika kwambiri ndipo anakupatsa moyo womwe ndi mphatso ya mtengo wapatali. Ndiye ukufunika kusonyeza kuti umayamikira mphatso imeneyi. Chonde, lowa mumpanda wotchinga khondeli.’
“Ndinawerenganso malemba angapo a m’Baibulo, monga Yohane 3:16. Lembali limati: ‘Pakuti Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.’
“Ndiye ndinamuuza kuti, ‘Mulungu amakukonda ndipo akufuna ukhale ndi moyo.’
“Poyamba munthuyo ankaoneka ngati analibe nazo ntchito zimene ndinkamuuzazo. Ndiye ndinapempha Yehova chamumtima kuti andithandize kumunyengerera munthuyo kuti asadziponye pansi. Kenako anaimirira n’kubwera pafupi ndi pamene ndinali, ndipo ankaoneka wokhumudwa kwambiri.”
“Munthuyo ananena kuti, ‘a Mboni za Yehova anabwera kunyumba kwanga chaposachedwapa koma ndinawathamangitsa. Ndikuona kuti ndinalakwa kwambiri. Chonde mundikhululukire.”
“Ndinamutsimikizira kuti, ‘Usakayikire ngakhale pang’ono kuti Mulungu akukhululukira. Ndipotu ngakhale enafe tinachitapo zimenezo tisanakhale a Mboni za Yehova.’
“Munthuyo anayankha kuti, ‘Zikomo kwambiri. Apa tsopano mtima wanga wakhala m’malo.
“Kenako ndinapitiriza kuti, ‘Ineyo ndavala zovala zodzitetezera pangozi. Koma ndikuchita mantha kwambiri kuti iweyo ungagwe n’kutaya moyo wako womwe ndi wamtengo wapatali. Zimenezo zingakhumudwitse Yehova kwambiri. Ndiye ndikukupempha kuti ulowe mumpanda wotchinga khondeli.’
“Ndinayamba kuona kuti wasintha maganizo ndipo anayankha modekha kuti, ‘CHABWINO ndikubwera.’
“Analowa mkati mwa mpanda wakhonde limene anthu amakwerapo kuti aziona kutali, ndipo apolisi anamutenga mwachangu. Ndinalankhulana naye pafupifupi ola limodzi kuti asadziponye pansi.”
A Mboni za Yehova amathandiza anthu ndi mtima wonse, makamaka amene ali ndi nkhawa. Padziko lonse lapansi, iwo amagwiritsira ntchito Baibulo pofuna kulimbikitsa anthu ndiponso powatsimikizira kuti Mulungu amawakonda kwambiri.