Mwambo wa Omaliza Maphunziro a Kalasi Nambala 135 ya Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibulo
Pa September 14, 2013 anthu okwana 10,500 anasonkhana pa mwambo wa kalasi nambala 135 ya omaliza maphunziro a Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibulo. Mwambowu unachitikira kulikulu la maphunziro la Mboni za Yehova ku Patterson m’dera la New York. Sukuluyi imathandiza anthu a Mboni za Yehova omwe akhala akugwira ntchito yolalikira kwa nthawi yaitali kuti akhale aluso kwambiri pogwira ntchito yawoyi.
Tcheyamani wa mwambowu anali M’bale Guy Pierce wa m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova ndipo mawu ake otsegulira anachokera palemba la Mateyu 28:19, 20. Mawuwa amati: “Choncho pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga, . . . ndi kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulirani.”
M’bale Pierce anafotokoza kuti mawu a Yesu amenewa akugwirabe ntchito mpaka pano. Iwo ananenanso kuti tikamaphunzira ndi anthu, timawathandiza kuchita zimene Yesuyo analamula. Zimenezi zimaphatikizapo lamulo lake lakuti tizilalikira “uthenga wabwino . . . wa ufumu.” (Mateyu 24:14) Choncho munthu aliyense amene waphunzira, amayamba kugwira nawo ntchito yolalikira komanso yophunzitsa ena za Ufumu wa Mulungu. Kodi zotsatirapo zake n’zotani? M’bale Pierce anati: “Pamene chiwerengero cha anthu padzikoli chikuwonjezeka, anthu a Mulungu nawonso akuchuluka.”
“Anapereka Zoposa Zimene Akanatha.” M’bale Thomas Cheiky, wa m’Komiti ya Nthambi ya ku United States anakamba nkhani yomwe mutu wake unachokera palemba la 2 Akorinto 8:1-4. Ngakhale kuti Akhristu oyambirira a mumpingo wa ku Makedoniya anali osauka kwambiri, anapempha kuti athandize nawo abale a ku Yerusalemu omwe anali pamavuto. Nawonso ophunzira amene amaliza maphunziro a Giliyadi asonyeza kuti ndi owolowa manja komanso anasonyeza kuti ali ndi mtima wodzipereka.
Koma sitikukayikira kuti Akhristu a ku Makedoniya anali oganiza bwino moti sanapereke mopitirira malire mpaka kulephera kusamalira mabanja awo kapena kusokoneza kulambira kwawo Mulungu. M’bale Cheiky analangiza ophunzirawo kuti atsanzire chitsanzo cha Akhristu a ku Makedoniya pochita zinthu mosapitirira malire pa nkhani yopatsa.
“Mwamaliza Maphunziro Anu.” M’bale Samuel Herd yemwe ndi wa m’Bungwe Lolamulira anafotokoza chifukwa chimene ophunzirawo ayenera kumakumbukira zinthu zimene zinkachitika ali ku Sukulu ya Giliyadi. Iye anafotokozanso kuti zinthu zabwino zimene anthuwo anaphunzira kusukuluyi zingawathandize kwa nthawi yaitali. Anayerekezera zimenezi ndi zomwe zimachitika munthu ukamvetsera kanyimbo kabwino m’mawa. Kanyimbo kotero umakaganizirabe tsiku lonse.
M’bale Herd anakumbutsa ophunzirawo kuti Mulungu saiwala. Iye anapatsa dzina nyenyezi iliyonse ngakhale kuti zilipo mabiliyoni ambirimbiri, ndipo palibe nyenyezi imene angayiiwale dzina. (Salimo 147:4) Izi zikusonyezeratu kuti Mulungu sangaiwale khama limene ophunzirawo anachita pamene ankaphunzira ku Giliyadi. Iwo anasunga “chuma kumwamba” ndipo palibe amene angabe chumacho, chomwe ndi zinthu zabwino zokhudza ophunzirawo zimene Yehova amakumbukira.—Mateyu 6:20.
Popeza Mulungu amakumbukira ntchito imene ophunzirawo anagwira komanso chikondi chimene anamusonyeza pa nthawi ya sukuluyi, ophunzirawo ayenera kumasangalala akakumbukira moyo wawo wa ku Giliyadi. M’bale Herd ananenanso kuti: “Pamene mukukumbukira zimene munaphunzira kusukuluyi musamaiwale kuthokoza Yehova chifukwa ndi amene anakuthandizani. Mupitirizebe kukumbukira zimenezi chifuwa zidzakuthandizani kwambiri.”
“Muzidalira Yehova Chifukwa Ali ndi Mphamvu Zopanda Malire.” A Sam Roberson, omwe ndi mphunzitsi wa kusukulu ya Giliyadi, analimbikitsa ophunzira kuti azidalira mphamvu za Yehova polimbana ndi mavuto osati kudalira mphamvu zawo. Lemba la Aefeso 3:20 limanena kuti Mulungu “angathe kuchita zazikulu kwambiri kuposa zonse zimene timapempha kapena kuganiza.” Iye ali ndi mphamvu zopanda malire. M’pake kuti mawu a palembali amasonyeza kuti n’zovuta kumufotokoza ‘chifukwa angathe kuchita zazikulu kwambiri kuposa zonse zimene timaganiza.’
Yehova amapereka mphamvu zake zopanda malire kwa Mkhristu aliyense. Palibe vuto limene angalephere kulithetsa chifukwa Yehova ali ngati “msilikali woopsa” kapena “wamphamvu.” (Yeremiya 20:11) M’bale Roberson anakumbutsa ophunzirawo kuti Yehova adzawathandiza kuthana ndi mavuto a mtundu uliwonse amene angakumane nawo.
“Pitirizani Kukhala Aulemu mu Utumiki Wanu.” M’bale William Samuelson, yemwenso ndi mphunzitsi wa sukulu ya Giliyadi, anafotokoza kuti ophunzira a m’kalasiyi apeza ulemu pa utumiki wawo m’njira ziwiri. Ophunzirawo anapeza aulemu chifukwa cha ntchito imene ankagwira asanabwere kusukuluyi komanso pa nthawi imene ankachita maphunziro awo. Iwo akupitirizanso kupeza ulemu chifukwa akuimira Ufumu wa Mulungu womwe ndi boma loposa maboma onse padziko lapansi.
Kodi ophunzirawa angatani kuti apitirizebe kukhala aulemu? M’bale Samuelson anawalimbikitsa kuti apitirize kulemekeza Yehova komanso kulemekeza ena. Anawalimbikitsa kuti azikachita zinthu ngati mmene Yesu ankachitira ndi anthu ena akamawalangiza kapena kuwathandiza. Kodi chingachitike n’chiyani ophunzirawa akamatsatira malangizo amenewa? Mofanana ndi mtumwi Paulo, ophunzirawa adzaonjezera ulemu wawo ndiponso adzalemekeza utumiki wawo m’malo mofuna kuti azilemekezedwa.—Aroma 11:13.
“Ulamuliro wa Mahatchi Uli M’kamwa Mwawo.” M’bale Michael Burnett, yemwenso ndi mphunzitsi wa sukuluyi anafotokoza mmene timachitira zinthu mogwirizana ndi kukwaniritsidwa kwa lemba la Chivumbulutso 9:19. Iye anafotokoza kuti timachita zimenezi tikamatsatira zimene timaphunzira pa misonkhano yachikhristu n’kumalankhula molimba mtima tikamalalikira. Kenako anafunsa ophunzirawo kuti afotokoze komanso kuti achite chitsanzo cha zimene ankakumana nazo mu utumiki pa nthawi imene anali ku Giliyadi. Mwachitsanzo, wophunzira wina anayamba kukambirana ndi munthu wina wogulitsa mafuta pamalo ogulitsira mafuta a galimoto. Wophunzirayo anafunsa munthuyo funso lochititsa chidwi lakuti, “Kodi nthawi zoikidwiratu za anthu a mitundu ina zinayamba liti? Nanga zinatha liti?” (Luka 21:24) Tsiku lina wophunzirayu atapitanso kwa munthuyu, anamuthandiza kuyankha funsoli pogwiritsa ntchito Danieli chaputala 4 ndi zakumapeto m’buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
“Athandizidwa Kukhala Olimba Mtima.” M’bale Adrian Fernandez wa m’Komiti ya Nthambi ya dziko la United States anafunsa mafunso mabanja iwiri omwe anamaliza maphunziro awo. M’bale Helge Schumi anafotokoza kuti Baibulo limasonyeza zitsanzo za atumiki ena a Mulungu amene anayamba kunyada atapatsidwa utumiki wapadera. Choncho ophunzira a ku Giliyadi amalangizidwa mobwerezabwereza kuti ayenera kukhala odzichepetsa. (2 Mbiri 26:16) Nayenso M’bale Peter Canning anakumbutsa ophunzirawo mfundo ina imene anaphunzira m’kalasi yokhudza kuphunzira chinenero cha kumalo kumene angatumizidwe. Iye ananena kuti: “Mukapitirize kukhala odzichepetsa. Ndipo musakaope kulankhula chinenero chomwe mukuphunziracho poganiza kuti anthu angakuoneni ngati wopepera mukalakwitsa.” Ophunzira onse okwana 4 amene anafunsidwa mafunso anayamikira kwambiri zimene anaphunzira chifukwa zingawathandize pa utumiki wawo komanso zingawathandize kukhala olimba mtima.—Aheberi 13:9.
“Kondwerani Chifukwa Mayina Anu Alembedwa Kumwamba.” (Luka 10:20) M’bale Geoffrey Jackson wa m’Bungwe Lolamulira anakamba nkhani yaikulu pa mwambowu. Iye ananena kuti mosiyana ndi ena amene anachita nawo maphunziro a ku Giliyadi m’mbuyomu, ophunzira a sukuluyi masiku ano sapatsidwa utumiki watsopano kapena kutumizidwa kumadera amene kulibe olalikira za ufumu. Kodi zimenezi zinawakhudza bwanji?
Yesu anatumiza ophunzira ake okwana 70 kuti akalalikire. Iwo atabwerako anafotokoza zinthu zosangalatsa zimene anachita, monga kutulutsa ziwanda m’dzina la Yesu. (Luka 10:1, 17) Yesu anavomereza kuti zimene zinawachitikirazo zinalidi zosangalatsa, koma iye ananena kuti: “Komano, musakondwere ndi zimenezi, kuti mizimu yakugonjerani, koma kondwerani chifukwa mayina anu alembedwa kumwamba.” (Luka 10:20) Apatu Yesu anasonyeza kuti si nthawi zonse pamene zinthu zingawayendere bwino mu utumiki. Kuonjezera pa kusangalala ndi zimene amachita mu utumiki, ophunzirawo anayenera kusangalalanso kuti ndi okhulupirika kwa Yehova komanso kuti ‘mayina awo alembedwa kumwamba.’
M’bale Jackson ananena kuti: “Zimene Yesu anauza ophunzira ake 70 aja n’zothandizanso kwa ife masiku ano.” Tisamaone kuti zimene timakumana nazo mu utumiki ndi zokhazo zimene zingatipangitse kusangalala, kapena n’zimene zingasonyeze kuti tili ndi chikhulupiriro. Koma tikhoza kumasangalala komanso kusonyeza kuti ndife okhulupirika tikamayesetsa kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova ndiponso tikamachita khama mu utumiki wathu.
Yesu nayenso anakumana ndi zinthu zimene zikatha kumufooketsa. Mwachitsanzo iye atadyetsa khamu la anthu mozizwitsa, anthuwo anayamba kumutsatira. (Yohane 6:10-14, 22-24) Koma pasanapite nthawi, anthu ambiri anakhumudwa ndi zimene Yesuyo ankaphunzitsa, moti anasiya kumutsatira. (Yohane 6:48-56, 60, 61, 66) Mosiyana ndi enawo, ophunzira ake okhulupirika anatsimikiza kuti samusiya. Iwo anatipatsa chitsanzo chabwino kwambiri chifukwa sankangoganizira za zinthu zimene zingawachitikire koma ankaganizira za ubwenzi wawo ndi Yehova.—Yohane 6:67-69.
Mawu Omaliza. Pamapeto pa mwambowu ophunzirawo analandira masatifiketi awo. Kenako mmodzi wa ophunzirawo anawerenga kalata yoyamikira imene iwo analemba. Ndiyeno M’bale Pierce anamaliza ndi mawu pofotokoza kuti, anthu a Mulungu, kuphatikizapo omaliza maphunzirowa, si anthu apadera. (Machitidwe 4:13; 1 Akorinto 1:27-31) Ngakhale zili choncho, Yehova amayamikira khama lathu ndipo amatipatsa mzimu wake woyera. N’zoona kuti Yehova sangatione kuti ndife amtengo wapatali chifukwa cha maphunziro athu. Komabe, M’bale Pierce anafotokoza kuti: “Iye amationa kuti ndife amtengo wapatali ngati tili okhulupirika ndiponso odzipereka kwa iye.”