Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Mwambo wa Omaliza Maphunziro a Kalasi ya Nambala 137 ya Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibulo

Mwambo wa Omaliza Maphunziro a Kalasi ya Nambala 137 ya Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibulo

Pa September 13, 2014, ophunzira a kalasi ya nambala 137 ya Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibulo anamaliza maphunziro awo. Mwambo womaliza maphunzirowa unachitikira ku Patterson m’chigawo cha New York komwe kuli likulu la maphunziro la Mboni za Yehova. Sukuluyi imaphunzitsa atumiki a Mboni za Yehova omwe akhala akutumikira kwa nthawi yaitali. Imawathandiza kuti awonjezere luso lawo polimbikitsa ndi kuthandiza anthu m’mipingo komanso m’maofesi a nthambi a kumene akutumikira. Anthu ena anaonera mwambowu ku likulu la maphunzirowa ku Patterson, pomwe ena anaonera pa TV m’madera ena a ku Canada, Jamaica, Puerto Rico, ndi ku United States komweko. Anthu onse amene anaonera mwambowu anakwana 12,333.

A Samuel Herd, omwe ndi a m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, ndi amene anali tcheyamani pa mwambowu. Iwo anayamba n’kufotokoza mmene maganizo a Yehova alili apamwamba kuposa athu. (Yesaya 55:8, 9) Ananena kuti ngakhale kuti ophunzira a m’kalasiyi aphunzira zinthu zambiri zokhudza Mulungu, zili ngati angoyepula pamwamba kapena kuti angodziwa “kambali kakang’ono chabe ka zochita zake.” (Yobu 26:14) M’bale Herd ananenanso kuti nthawi zonse tikasonkhana kuti tiphunzire maganizo a Mulungu timapindula, choncho onse amene aonere mwambowu apindulanso.

“Khalidwe Limene Mzimu Woyera Umatulutsa ndi . . . Kuleza Mtima.” (Agalatiya 5:22) A John Larson, a m’Komiti ya Nthambi ya ku United States, anafotokoza mfundo ziwiri zokhudza mmene tingasonyezere khalidwe la kuleza mtima, lomwe ndi limodzi mwa makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa. Choyamba, timafunika kulezera mtima Yehova. Tizichita zimenezi iye akamatiphunzitsa ndi kutithandiza kuti tikhale olimba m’chikhulupiriro. (1 Petulo 5:10) Chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhaniyi ndi Abulahamu. Iye analeza mtima pamene Yehova ankamuphunzitsa komanso pamene ankayembekezera kuti Yehova akwaniritse zimene anamulonjeza.​—Aheberi 6:15.

Mfundo yachiwiri, tiyenera kumadzilezera mtima tokha. Ophunzirawa atamaliza maphunziro awo, akhoza kumayembekezera zinthu zambiri. Ndiye ngati atayamba utumiki wawo koma zimene amayembekezerazo osachitika, akhoza kumadzifunsa kuti, ‘Kodi vuto langa n’chiyani?’ Malinga ndi zimene zinam’chitikira, M’bale Larson anawatsimikizira kuti akhoza kuthana ndi mavuto ngati atamadzilezera mtima komanso akamatumikira Mulungu modzipereka pamene iye akumalizitsa kuwaphunzitsa.​—Aheberi 6:11, 12.

“Mitima Yanu Ikhale Yodzichepetsa Kuti Mukhale ndi Moyo Kosatha.” M’bale Anthony Morris wa m’Bungwe Lolamulira ndi amene anakamba nkhaniyi, ndipo inachokera pa Salimo 22:26. Mbali yomaliza ya vesili imanena kuti “mitima yanu ikhale ndi moyo kosatha.” Kuti tidzalandire moyo wosathawu tiyenera kukhala odzichepetsa. M’bale Morris ananena kuti Yehova akhoza kusiya kutigwiritsa ntchito ngati sindife odzichepetsa. Mkhristu aliyense ngakhale amene watumikira Mulungu kwa nthawi yaitali akhoza kuiwala mfundo yofunika kwambiri yakuti ayenera kukhala wodzichepetsa ngati mmene Yesu Khristu analili.​—2 Petulo 1:9.

M’Baibulo muli zitsanzo za anthu amene anasonyeza kudzichepetsa ndi amene anasonyeza kudzikuza. Herode Agiripa anasonyeza kudzikuza chifukwa analandira ulemerero umene unayenera kupita kwa Mulungu. Zimenezi zinachititsa kuti mngelo wa Mulungu amukanthe ndipo kenako “anadyedwa ndi mphutsi n’kumwalira.” (Machitidwe 12:21-23) Koma Petulo anasonyeza kudzichepetsa pamene Yesu anamudzudzula chifukwa chosaganiza “maganizo a Mulungu, koma maganizo a anthu.” Iye sanakhumudwe kapena kukwiyira Yesu. (Mateyu 16:21-23) Petulo anavomereza kulangizidwa ndipo ndi chitsanzo chabwino pa nkhani ya kudzichepetsa.​—1 Petulo 5:5.

Pambuyo pa maphunzirowa, ophunzira ena anatumizidwa kuti azikatumikira ku maofesi a nthambi a Mboni za Yehova. Ndipo M’bale Morris anawachenjeza kuti akakakhala odzikuza sakasangalala ndi utumiki. Komatu zimakhala zovuta kuti munthu adziwe kuti ndi wodzikuza. Pofuna kuthandiza ophunzirawa kumvetsa mfundoyi, iye anafotokoza zomwe m’bale wina anachita akulu atamudzudzula chifukwa chosadzichepetsa. M’baleyu analemba kalata ku ofesi ya nthambi n’kunena kuti, “Ine ndine munthu wodzichepetsa kwambiri ndipo sindinaonepo munthu wodzichepetsa kuposa ine.” M’bale Morris analangiza ophunzirawa kuti asakhale ndi mtima umenewu. Iwo angapitirize kukhala odzichepetsa pokhapokha ngati atapewa kudziona ngati apamwamba chifukwa cha udindo wawo. Angapewenso kudzikudza ngati atazindikira kuti amene ali ndi udindo waukulu ndi Yehova Mulungu komanso Yesu Khristu.

“Akafuna Kupereka Mzimu Sachita Kuyeza Pamuyezo.” (Yohane 3:34) A Michael Burnett, omwe ndi mmodzi mwa alangizi a sukulu ya Giliyadi anakumbutsa ophunzirawa kuti mzimu woyera ukawathandiza kuthana ndi mavuto kapena nkhawa zomwe azikakumana nazo pa utumiki umene angapatsidwe. Mzimu wa Mulungu unathandiza Bezaleli kuti akwanitse kupanga chihema ngakhale kuti inali ntchito yovuta kwambiri. (Ekisodo 35:30-35) Mzimu wa Mulungu unathandizanso Bezaleli kuti aziphunzitsa ena ntchitoyi. Mzimu woyera ungathandizenso amene amaliza maphunziro a Giliyadi pokhapokha ngati azitsatira mfundo za m’Malemba zimene aphunzira m’kalasi.

M’nthawi ya Bezaleli, akazi a ku Isiraeli nawonso ankathandiza pa ntchito yomanga chihema. (Ekisodo 35:25, 26) Alongo amene anali m’kalasi ya Giliyadiyi nawonso asonyeza kuti ndi ‘akazi aluso’ chifukwa chakuti akuthandiza kwambiri amuna awo. Pomaliza nkhani yake, M’bale Burnett analimbikitsa ophunzirawa kuti: “Muziyesetsa kukhala odzichepetsa komanso omvera pogwiritsa ntchito maluso anu achibadwa. Mukatero, Yehova adzakupatsani mzimu wake woyera mosachita kuyeza.”

“Kodi Mudzavina Ndi Ine?” M’bale Mark Noumair yemwe ndi wothandiza Komiti Yoona za Ntchito Yophunzitsa ya Bungwe Lolamulira ndi amene anakamba nkhaniyi. Iye anagwiritsa ntchito chitsanzo cha zimene Mfumu Davide inachita pa nthawi imene inapititsa likasa la pangano ku Yerusalemu. (2 Samueli 6:12-14) Pa nthawiyo, Davide anasonyeza kudzichepetsa chifukwa anavina mosangalala ndi “akapolo aakazi a atumiki ake.” (2 Samueli 6:20-22) Akapolo aakaziwa anasangalala kwambiri chifukwa anavina ndi Mfumu Davide ndipo zimenezi zinali zosaiwalika pa moyo wawo. M’bale Noumair analimbikitsa ophunzirawa kuti nawonso ‘azikavina ndi akapolo aakazi.’ Iye anafunsa ophunzirawa kuti: “Kodi mukayesetsa kuthandiza anthu amene alibe udindo ulionse kapenanso omwe ali ndi maudindo ochepa?” Kenako anawalimbikitsa kuti: “Muzikayesetsa kulemekeza anthu chifukwa chakuti amasonyeza makhalidwe achikhristu.”

Ophunzirawa angasonyeze kuti amatsanzira Yehova ngati angapitirize kukonda anthu mosayang’ana nkhope. (Salimo 113:6, 7) Iwo analimbikitsidwanso kuti asakasiye kusonyeza mtima wodzichepetsa ngakhale pa nthawi imene anthu omwe akutumikira nawo akulephera kusonyeza mtima wodzichepetsa. M’bale Noumair ananenanso kuti: “Musamakadzione kuti ndinu apamwamba kuposa ena. Ndipo muzikasamalira nkhosa za Yehova mmene iye angazisamalire.”

“Kuchitira Umboni pa Nthawi Iliyonse Yoyenera.” M’bale William Samuelson wa mu Dipatimenti Yoyang’anira Sukulu Zophunzitsa Atumiki a Mulungu anafotokoza kuti Paulo ndi chitsanzo chabwino pa nkhani yolalikira uthenga wabwino pa mpata uliwonse. (Machitidwe 17:17) M’baleyu anapempha ophunzira ena kuti asonyeze zinthu zosangalatsa zimene zinawachitikira muutumiki wa kumunda pa nthawi ya maphunziro awo. Mwachitsanzo, banja lina linakumana ndi mayi wina wogulitsa m’sitolo ya zakudya. Banjali linadikira kuti anthu achepe kaye m’sitolomo, kenako linaonetsa mayiyo vidiyo ya mutu wakuti, N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo? Linamusonyezanso webusaiti ya jw.org kuti awerenge nkhani za m’chinenero chake, chomwe ndi Chilaoti. Tsiku lina banjali linapitanso kwa mayiyu ndipo linakapitiriza kukambirana moti mayiyu anayamba kuchita chidwi ndi uthenga wa m’Baibulo.

“Pitirizani Kudzipereka pa Ntchito ya Ufumu.” A William Nonkes, omwe amagwira ntchito mu Dipatimenti ya Utumiki ku ofesi ya nthambi ya ku United States anafunsa mafunso ophunzira 4. Ngakhale kuti anadzipereka kale kuti atumikire Mulungu potsatira zimene lemba la Yesaya 6:8 limanena, zimene anaphunzira kusukuluyi zinawathandiza kuti akhale odzipereka kwambiri pomutumikira. Mlongo Snolia Maseko ananena kuti zimene waphunzira kusukulu ya Giliyadi zamuthandiza kuzindikira mbali zimene angayesetse kuchita bwino. Mwachitsanzo, anazindikira mmene angagwiritsire ntchito nthawi mwanzeru tsiku lililonse ngakhale kuti amakhala atachita kale zambiri pa tsikulo. Iye ananena kuti: “Maphunzirowa andithandiza kuti ndizichita zambiri zimene ndinkaganiza kuti sindingakwanitse.” M’bale Dennis Nielsen anaphunzira mmene mfundo ya pa Zefaniya 3:17 ingamuthandizire kuti asamafooke akakhala mu utumiki. Iye anati: “Ndikakhala kuti sindikuona zotsatira za ntchito yanga mu utumiki, nthawi zonse ndizikumbukira kuti Yehova akufuula mosangalala ndipo inenso ndiyenera kumafuula mosangalala.”

“Onetsetsani Mbalame Zam’mlengalenga.” (Mateyu 6:26) A Stephen Lett a m’Bungwe Lolamulira anakamba nkhani yaikulu pamwambowu. Iwo ananena zinthu zambiri zimene tingaphunzire pa zimene Yesu anaphunzitsa kuti ‘tizionetsetsa,’ kapena kuti tizichita chidwi kwambiri ndi mbalame.​—Yobu 12:7.

Mwachitsanzo, tingaphunzire kuti Yehova angatisamalire monga mmene amasamalira mbalame. Ifeyo ndife anthu a “m’nyumba ya Mulungu,” ndipo amatitsimikizira kuti adzasamalira anthu “a m’banja lake.” (1 Timoteyo 3:15; 5:8) Komabe tiyenera kuchita mbali yathu ngati mmene mbalame zimachitira. Izo zimafunafuna chakudya chimene Mulungu amapereka. Ifenso tiyenera “kufunafuna ufumu choyamba” kuti tilandire madalitso amene Mulungu amapereka.​—Mateyu 6:33.

M’bale Lett ananenanso kuti mbalame zambiri zikaona chinthu choopsa zimalira pofuna kuchenjezana. Ifenso timachenjeza anzathu tikaona kuti akufunika kuchenjezedwa. Mwachitsanzo, timachita zimenezi tikaona kuti m’bale wathu “wapatuka n’kuyamba kulowera njira yolakwika mosazindikira.” (Agalatiya 6:1) Komanso tikamalalikira, timachenjeza anthu za “tsiku la Yehova” lomwe layandikira kwambiri. (Zefaniya 1:14) M’bale Lett anafotokozanso chitsanzo cha zimene mbalame zina zimachita zikamasamuka. Mbalamezi zimatha kuuluka n’kudutsa m’mapiri aatali. Mofanana ndi zimenezi, Yehova amatithandiza kuthana ndi mavuto amene angaoneke ngati ovuta kuthana nawo.​—Mateyu 17:20.

Mawu Omaliza. Ophunzira atalandira madipuloma awo, mmodzi mwa ophunzirawo anawerenga kalata yoyamikira imene onse analemba. Kenako M’bale Herd ananena mawu omaliza a mwambowu. M’baleyu anayerekezera zimene munthu angachite kuti adziwe maganizo a Yehova ndi zimene oika njanji za sitima amachita. Amafunika kukhoma kwambiri njanjiyo ndi zitsulo zolimba n’cholinga choti njanjiyo ikhale yolimba kwambiri. Mofanana ndi zimenezi, analimbikitsa ophunzirawo kuti apitirize kuganizira zimene anaphunzira kusukulu ya Giliyadi. M’baleyu ananena kuti: “Muzikhala ndi nthawi yokwanira yokhomereza maganizo a Yehova m’mitima yanu ndipo muziwagwiritsa ntchito pamoyo wanu. Mukatero, mudzadalitsidwa kwambiri.”