A Mboni za Yehova Anachita Misonkhano Yachigawo Yapadera M’mayiko 7
Chaposachedwapa, a Mboni za Yehova anachita misonkhano yachigawo yapadera ku Brazil, Costa Rica, Hong Kong, Ireland, Israel, New Zealand ndi Sweden. Msonkhano woyambirira unachitika ku Sweden mu July 2012, ndipo misonkhano itatu yomaliza inachitika ku Costa Rica ndi ku New Zealand mu January 2013.
Mofanana ndi misonkhano yachigawo yonse yomwe imachitika kwa masiku atatu chaka ndi chaka, pa misonkhano yachigawo yapaderayi panakambidwa nkhani za m’Baibulo, panali zitsanzo ndiponso masewero.
Alendo ochokera m’mayiko ena anaitanidwa kumisonkhano yapaderayi. Alendowo anali ndi mwayi woona malo osiyanasiyana m’mayiko amene mumachitikira misonkhanoyo, ndipo ankachita zimenezi misonkhanoyo isanayambe kapena ikatha.
Munthu wina amene anapita ku Brazil kukachita nawo msonkhano anati: “Zinali zosangalatsa kwambiri kuona mtima wochereza komanso chikondi chenicheni pakati pa abale ndi alongo. Nditangofika, zinangokhala ngati nthawi yomweyo ndapeza anthu a m’banja mwanga.”
Munthu winanso amene anapita ku Hong Kong kukachita msonkhano anati: “Ndinasangalala kwambiri nditaona nkhope zachimwemwe. Anthu ena ankachita kulira chifukwa cha chisangalalo atalandira mabuku atsopano ofotokoza nkhani za m’Baibulo a chinenero cha Chimandarin.”
Chaka chilichonse, a Mboni za Yehova amachita misonkhano yachigawo m’mayiko osiyanasiyana padziko lonse lapansi, ndipo anthu mamiliyoni ambirimbiri amafika kumisonkhano imeneyi.
Misonkhano imathandiza anthu amene afikako kuti asonyezane chikondi chenicheni komanso asangalale ndi ubale wathu wapadziko lonse. Zimenezi makamaka zimachitika kwambiri pamisonkhano yapadera kapena yamayiko. Misonkhanoyi isanayambe kapena ikatha, anthu amene afika pa msonkhanowo amacheza, kupatsana mphatso, manambala a foni ndi ma adiresi, kujambula zithunzi ndiponso kukumbatirana mwachikondi.
Mofanana ndi misonkhano yathu yonse, anthu amene si a Mboni za Yehova ndi olandiridwa kumisonkhanoyi.