Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Vidiyo ya pa Intaneti Ikuthandiza Kwambiri

Vidiyo ya pa Intaneti Ikuthandiza Kwambiri

Msonkhano wapachaka wa bungwe la Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania wa nambala 129, unachitika Loweruka pa October 5, 2013. Anthu okwana 257,294 ochokera m’mayiko 21, anapezekapo kapena kuonerera msonkhanowu pa vidiyo ya pa Intaneti pa nthawi yomwe msonkhanowu unkachitika. Kenako mlungu womwewo, msonkhanowu anauonetsanso kachiwiri pa vidiyo. Anthu onse a Mboni amene anaonera msonkhanowu pa nthawiyi anali ochokera m’mayiko 31 ndipo analipo 1,413,676. Msonkhano wapachaka wa Mboni za Yehova umenewu unali waukulu kwambiri kuposa misonkhano ina yonse imene inachitikapo m’mbuyomu. Anthu amene anamvetsera msonkhano wapachakawu anali ochuluka zedi kuposa anthu 1,327,704, omwe anamvetsera msonkhano wapadera ku Mexico ndi ku Central America, pa April 28, 2013.

Kuyambira m’ma 1920, a Mboni za Yehova anayamba kulumikiza misonkhano yawo pa telefoni komanso kuiulutsa pa wailesi n’cholinga choti anthu ambiri m’mayiko osiyanasiyana azitha kumvetsera misonkhanoyo. Koma masiku ano kuli Intaneti ndipo ikuthandiza kuti anthu a m’mayiko ndi madera osiyanasiyana, ngakhale akutali kwambiri, azitha kuona ndi kumvetsera misonkhano pa nthawi imene ikuchitika kapena ikangotha kumene. Bambo William, omwe ndi a Mboni za Yehova ku United States, akukumbukira msonkhano wa Mboni womwe unalumikizidwa pa telefoni m’chaka cha 1942, ndipo anaumvetsera ku Richmond m’dera la Virginia. Poyerekezera msonkhano umenewo ndi msonkhano wapachaka wa chaka chathachi, bambowa anati: “Umapindula kwambiri ukamaonera msonkhano pa vidiyo chifukwa zimakhala ngati uli pamalo amene msonkhanowu ukuchitikira. Sitingayerekezere n’komwe ndi kumvetsera msonkhano pa telefoni.”

Panali ntchito yaikulu zedi yokonzekera kuti msonkhanowu udzaonetsedwe pa vidiyo ya pa Intaneti. Anthu ochokera m’mayiko osiyanasiyana amene amagwira ntchito m’maofesi a Mboni za Yehova, anagwira ntchito kwa nthawi yoposa chaka chimodzi polumikiza zipangizo zothandiza kuonetsa vidiyo pa Intaneti. Pa tsiku limene msonkhanowu unachitika komanso pa tsiku lotsatira, anthu a Mboni omwe ndi akatswiri amene analumikiza makina oonetsera vidiyo pa Intaneti, ankayendetsa zonse ali ku ofesi ya ku Brooklyn m’dera la New York. Iwo anaonetsetsa kuti kwa masiku onse awiri, masana ndi usiku omwe, pali anthu amene akuyendetsa zinthu pamakina. Izi zinali choncho chifukwa msonkhanowu unaonetsedwa m’madera ndi mayiko osiyanasiyana ndipo nthawi inali yosiyananso kwambiri. Munthu wina amene anali m’gulu la akatswiri amene ankayendetsa zinthu pamakina anali Ryan. Iye ananena kuti: “Sitinagone. Komabe tikusangalala chifukwa tikudziwa kuti ntchito yomwe tinkagwirayo inathandiza anthu ambirimbiri omwe anaonera msonkhanowu pa vidiyo.”

Akuonerera msonkhano pa vidiyo ya pa Intaneti ku Katherine m’dera la Northern Territory, m’dziko la Australia