Anthu Ongodzipereka Akugwira Ntchito Yotamandika ku Tuxedo
Tsiku lina nthawi itakwana 6:45 m’mawa, anthu omwe anavala zovala zogwirira ntchito anali pikitipikiti kulowa m’nyumba ina yosanjikizana ka 4 imene ili ku Tuxedo, m’chigawo cha New York. Kunja kunacha bwino moti kumwamba kunali mbee, kopanda mitambo. Madzi a m’nyanja yaing’ono imene ili kuseri kwa nyumbayi anali atayamba kuundana. Anthu amenewa anali ochokera m’madera osiyanasiyana m’chigawo chomwechi cha New York, monga ku Patterson ndi ku Wallkill. Komanso ena anachokera ku Brooklyn ndipo anayenda mtunda wa makilomita pafupifupi 80 kuti adzafike kuno ku Tuxedo. Ena ankagona m’mahotelo koma ena kunyumba za pa Beteli.
Tsikuli lisanafike, ambiri mwa anthuwa anafika m’derali kuchokera m’madera osiyanasiyana a m’dziko la United States ndiponso a m’mayiko ena. Iwo anabwera kuti adzagwire nawo ntchito kuno mongodzipereka, ena kwa mlungu umodzi, ena kwa milungu 6 ndipo ena kwa nthawi yotalikirapo. Anthuwa analipira okha ndalama zoyendera podzagwira ntchitoyi.
Patsikulo, panali anthu ongodziperekawa okwana pafupifupi 120, ndipo chiwerengerochi chinawonjezereka patapita miyezi ingapo. Anthuwo analowa m’chipinda chodyera cha nyumba yosanjikizana ka 4 ija ndipo ambiri mwa anthuwo ankatunga khofi kenako n’kukakhala patebulo yawo. Patebulo iliyonse pankakhala anthu 10. Kafungo kabwino ka nyama ya nkhumba komwe kankachokera kukhitchini kanadzaza m’chipinda chodyeracho. Nthawi itangokwana ndendende 7 koloko m’mawawo, pulogalamu yokambirana lemba la tsiku lochokera m’Baibulo inayamba. Patapita mphindi 15, abale operekera zakudya anayamba kubweretsa chakudya cha m’mawa. Panali chakudya cha mwanaalirenji monga nyama ya nkhumba, buledi, mazira, phala ndi zina zotero.
Atamaliza kudya ndiponso pemphero lomaliza litaperekedwa, anthuwo ananyamuka ulendo wokagwira ntchito. Nkhani zili pakamwa, anayamba kuvala zipewa zawo zazigoba, magalasi oteteza maso, zovala zoonekera patali komanso malamba akuluakulu okolekamo zipangizo zogwirira ntchito.
Ntchito imene anthuwa amakonzekera kukagwira inali yokonzanso nyumba ina imene inali kampani yokonza mapepala ku Tuxedo. Iwo amakonza nyumbayo kuti ikhale malo osungirapo zipangizo zomangira nyumba zomwe zikhale likulu la Mboni za Yehova. Likululi limangidwa m’tauni ya Warwick yomwe ili pa mtunda wa makilomita ochepa kuchokera ku Tuxedo. Nyumba zina zomwe zinali za kampaniyi akuzikonza kuti zikhale nyumba zogona, maofesi, malo okonzera zinthu komanso malo osungira katundu. Ndipo Lachiwiri pa March 12, 2013, akuluakulu a boma oona za mapulani a zomangamanga anavomereza zoti ntchitoyi ikhoza kuyambika ku Tuxedo.
Kodi anthu amene amadzipereka kuti agwire nawo ntchitoyi kwa kanthawi amalandiridwa bwanji akafika ku Beteli? M’bale wina wa ku New Jersey dzina lake William, anati: “Ukangofika kumene pamalo olandirira alendo ku Beteli, abale amene akulandira alendo amakuuza zinthu zofunika. Amakuuza mmene ungagwiritsire ntchito makiyi, kumene kuli chipinda chako chogona komanso mmene ungayendere malo osiyanasiyana pa Beteli. Aliyense amakhala wofunitsitsa kukuthandiza. Ndiyeno ukafika ku Tuxedo, pambuyo pa chakudya cham’mawa, umakumana ndi m’bale amene akutsogolera gulu lanu logwira ntchito ndipo amakufotokozera ntchito imene uzigwira.”
Kodi ntchito imayenda bwanji tsiku lililonse? Yajaira ndi mwamuna wake, omwe anachokera ku Puerto Rico ndipo akugwira nawo ntchito yomangayi, anati: “Tsiku lililonse timadzuka cha m’ma 4:30 m’mawa. Tikatero timakonza m’chipinda chathu, kumwa khofi, kenako timakwera basi imene timayendera. Pofika madzulo timakhala titatopa, komabe timakhala osangalala ndipo sititopa n’kuseka. Aliyense amene akugwira nawo ntchitoyi ndi wosangalala kwabasi.”
Malo amene kukumangidwa nyumba zomwe zikhale likulu la padziko lonse la Mboni za Yehova ali pakati pa nkhalango. Zach ndi mkazi wake Beth, omwe ndi ochokera ku Minnesota, amasangalala kuthandiza pa ntchito imene ikuchitika ku Warwick. Atafunsidwa kuti n’chifukwa chiyani anabwera kudzagwira nawo ntchitoyi, Beth anayankha kuti: “Tikukhulupirira kuti palibenso ntchito yabwino imene munthu angagwire pa moyo wake kuposa kutumikira Yehova. Tinaona kuti ndi bwino kugwiritsa ntchito luso lathu potumikira Yehova.”