Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Zithunzi Zosonyeza Ntchito Yomanga ku Warwick Gawo 6 (Kuyambira March Mpaka August 2016)

Zithunzi Zosonyeza Ntchito Yomanga ku Warwick Gawo 6 (Kuyambira March Mpaka August 2016)

Zithunzi izi zikusonyeza mmene ntchito yomanga likulu latsopano la Mboni za Yehova inayendera komanso mmene antchito ongodzipereka anathandizira ntchito yomangayi kuyambira mu March mpaka August 2016.

Kuyambira pa nambala 1 mpaka 8:

  1. Galaja

  2. Poimika Magalimoto Alendo

  3. Nyumba Yokonzeramo Zinthu Komanso Koimika Magalimoto

  4. Nyumba Yogona B

  5. Nyumba Yogona D

  6. Nyumba Yogona C

  7. Nyumba Yogona A

  8. Maofesi

 

16 March, 2016​—Ku Warwick

Anthu ogwira ntchito yodzala kapinga akutsitsa mitengo yoti adzale. Panopa akudzala mitengo yatsopano yoposa 1,400.

23 March, 2016—Galaja

Ogwira ntchito ku Warwick akuchita mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye ndipo pamwambowu panasonkhana anthu okwana 384. A Mboni za Yehova padziko lonse amachita mwambo umenewu kamodzi pa chaka.

15 April, 2016​—Ku Warwick

Makalipentala akuika mawindo pa kanyumba ka pa geti. Anthu amene azidzakhala m’kanyumba kameneka azidzalandira anthu, kuonetsetsa kuti kuli chitetezo chokwanira komanso kuthandiza magalimoto olowa ndi kutuluka pamalowa.

19 April, 2016​—Maofesi

Bambo ndi mwana wake akulumikiza zidutswa za makalapeti m’njira ya m’mwamba ya nyumba yosanja yachiwiri. Makalapeti oduladulawa anaikidwanso m’malo amene amagwiritsidwa ntchito ndi anthu ambiri chifukwa makalapetiwa akawonongeka savuta kubwezeretsapo ena.

27 April, 2016​—Maofesi

Makalipentala akugawa maofesi ndipo zipangizo zomwe akugwiritsa ntchito zidzathandiza anthu a m’madipatimenti kuti azidzatha kukulitsa kapena kuchepetsa malo m’maofesi awo ngati pangadzafunike kutero.

10 May, 2016​—Maofesi

Wogwira ntchito akukonza zina ndi zina m’matoileti omwe ali pafupi ndi malo ofikira alendo.

26 May, 2016​—Ku Warwick

Gulu la ozimitsa moto komanso lothandiza pakachitika ngozi zadzidzidzi likukonzekera kuzimitsa moto. Kukonzekereratu zinthu ngati zimenezi mwamsanga, n’kothandiza kuti ogwira ntchito yozimitsa motowa azitha kuteteza anthu ogwira ntchito komanso nyumba zimene zili kumalowa ngati moto utabuka.

30 May, 2016​—Maofesi

Woperekera zakudya akuthandiza anthu kupeza malo m’chipinda chodyera, pulogalamu ya Kulambira kwa M’mawa isanayambe komanso asanalumikizane ndi abale akumadera ena.

31 May, 2016​—Nyumba Yokonzeramo Zinthu Komanso Koimika Magalimoto

Kalipentala akugwiritsa ntchito kachipangizo kogwira ntchito ngati levulo poika kamodzi mwa tizikwangwani toposa 2,500 tomwe tizidzathandiza anthu okhala m’nyumbazi komanso alendo kudziwa komwe angalowere.

1 June, 2016​—Maofesi

Wogwira ntchito yowotcherera, akuwotcherera mahandulo pamasitepe ochokera kofikira alendo kukafika kuholo. Bulangete likuoneka pansilo, likuteteza zitsulo zina zomwe zawotchereredwa kale kuti zisawonongeke.

9 June, 2016​—Maofesi

Wogwira ntchito m’dipatimenti yoika makoma komanso siling’i akumalizitsa kukonza khoma lolowera kumalo oonetsera zinthu zosiyanasiyana zokhudza mbiri ya Mboni za Yehova omwe ali ndi mutu wakuti, “Mboni za Yehova Zinasonyeza Chikhulupiriro.” Malowa ndi amodzi mwa malo atatu omwe anapangidwa m’njira yoti alendo asamavutike kukafika kumalo oonetsera zinthu zosiyanasiyana. Gawo lililonse limasonyeza mutu wofotokozera zithunzi zomwe zili pa gawolo.

16 June, 2016​—Galaja

Ogwira ntchito akukonza zoti konkire igwirane ndi kukhala yolimba kwambiri. Zimene akuchitazi zithandizanso kuti konkireyo isamasungire fumbi ndi madindo a matayala a magalimoto komanso zithandiza kuti isamavute kukonza ikawonongeka.

29 June, 2016​—Maofesi

Gulu la makalipentala likuika denga pamalo ofikirapo alendo. Zinthu zomwe akukonzera dengali zizipangitsa kuti kuwala kuzilowa mkati mwa malo ofikira alendowa.

29 June, 2016​—Maofesi

Mwamuna ndi mkazi wake akuika matailosi pakhomo lopita kumalo oonetsera zinthu a mutu wakuti, “Dzina la Mulungu M’Baibulo.”

6 July, 2016​—Maofesi

Kalipentala akuika mipando mu holo yayikulu. Holoyi ndi yokwana mipando 1,018 ndipo ndi mmene banja la beteli lizidzachitiramo Phunziro la Nsanja ya Olonda komanso zinthu zina zokhudza kulambira.

9 July, 2016​—Maofesi

Makalipentala, ogwira ntchito zamagetsi ndi ogwira ntchito zinanso akuika chikwangwani chomwe chizidzawala pamalo ofikira alendo. Chikwangwanichi chili ndi mawu olandirira alendo.

13 July, 2016​—Maofesi

Anthu awiri a m’dipatimenti yothandiza ntchito yomanga akuperekera madzi oti anthu omwe akugwira ntchito pamalo ofikira alendo azimwa. Makamaka nthawi yotentha, ogwira ntchito ankalimbikitsidwa kumwa madzi ambiri.

19 July, 2016​—Maofesi

Kalipentala akukonza malo osungiramo ma Baibulo omwe sapezeka mwachisawawa. Malowa amadziwika kuti, “Dzina la Mulungu M’Baibulo” ndipo mkati mwa mabokosiwa adzaikamo Mabaibulo akale kwambiri omwe sapezekapezeka masiku ano. Pamalowa aziikaponso Mabaibulo enanso komanso zinthu zina zakale zokhudza Baibulo mosinthasintha.

22 July, 2016​—Maofesi

Kalipentala akujambula mapu osonyeza dziko la Australia komanso zilumba za ku Southeast Asia pamalo ofikira alendo. Kalipentalayu wapanga mapulani ake pakhoma omuthandiza kuti asavutike kujambula mapuwo. Pakhomali pakuonekanso dzina lakuti Mboni za Yehova m’zilankhulo pafupifupi 700.

23 July, 2016​—Maofesi

Abale ndi alongo a ku beteli ali pamsonkhano wophunzira kugwiritsa ntchito zinthu zosiyanasiyana zomwe zili kumalowa. Msonkhanowu unakonzedwa pofuna kuthandiza anthu komanso atsopano amene angadzabwere kudzatumikira pa beteli ku Warwick. Komanso kuwaphunzitsa mmene angapewere ngozi kumalowa.

17 August, 2016​—Situdiyo ya JW Broadcasting

Anthu akupachika chinthu chooneka ngati ling’i chomwe chizidzawala ndipo akuika zitsulo zochirikizira pamwamba. Pansipo padzakhala tebulo la wochititsa JW Broadcasting. Panopa zipangizo zambiri zogwiritsa ntchito pokonza situdiyoyi zinabwera kuchokera kumalo athu akale ku Brooklyn.

24 August, 2016​—Ku Warwick

Wogwira ntchito zamagetsi akuika chikwangwani chatsopano pafupi ndi geti lalikulu ndipo mawu a pachikwangwanipo azidzawala. Pofika pa 1 September, madipatimenti ambiri a kulikulu lathu anali atayamba kugwira ntchito ku Warwick.