BAIBULO LIMASINTHA ANTHU
Anapeza “Ngale . . . Yamtengo Wapatali”
Yesu anaphunzitsa kuti Ufumu wa Mulungu udzathetsa mavuto onse omwe anthu akukumana nawo. (Mateyu 6:10) Pa Mateyu 13:44-46, iye anafotokoza mafanizo awiri otsatirawa pofuna kusonyeza kufunika kwa choonadi chonena za Ufumu wa Mulungu:
Mwamuna wina ankalima m’munda, kenako mwadzidzidzi anaona chuma chomwe chinabisidwa m’mundamo.
Munthu wina wochita malonda amene ankayendayenda pofufuza ngale zabwino, anapeza ngale imodzi yamtengo wapatali.
Anthu awiriwa, anagulitsa katundu wawo yense kuti apeze zinthu zamtengo zomwe anaona. Amunawa akuimira anthu omwe amaona zinthu zokhudza Ufumu kukhala zofunika kwambiri moti amalolera kusintha zinthu zambiri pa moyo wawo ndi cholinga choti apeze madalitso a Ufumuwo. (Luka 18:29, 30) Muvidiyoyi muphunzira za anthu awiri omwe anachita zinthu ngati amuna otchulidwa mufanizo la Yesu.