BAIBULO LIMASINTHA ANTHU
“Zinkaoneka Ngati Zinthu Zikundiyendera”
CHAKA CHOBADWA: 1962
DZIKO: Canada
POYAMBA: Ndinkakonda zachiwerewere
KALE LANGA
Ndinabadwira ku Canada mumzinda waukulu wa Montreal koma m’dera lotchedwa Quebec. Tinkakhala m’mudzi wosangalatsa kwambiri wa Rosemont. M’banja mwathu tinalimo ana 4 ndipo makolo athu ankatikonda kwambiri. Zinthu zinkatiyendera bwino ndipo tinkasangalala.
Ndili mwana ndinkakonda kuwerenga Baibulo. Ndimakumbukira kuti ndili ndi zaka 12, ndinawerenga nkhani yokhudza moyo Yesu mu Chipangano Chatsopano ndipo inandisangalatsa kwambiri. Ndinaona kuti Yesu anali munthu wachikondi komanso ankamvera ena chifundo ndipo ndinkafunitsitsa nditakhala ngati iyeyo. Koma n’zomvetsa chisoni kuti pamene ndinkakula, maganizowa anayamba kusintha ndipo ndinayamba kugwirizana ndi anthu a makhalidwe oipa.
Bambo anga anali katswiri woimba mtundu winawake wa chitoliro chotchedwa saxophone. Patapita nthawi anandipatsa chitolirocho. Bambo anandipangitsa kuti ndizikonda kwambiri kuimba moti ndinkafuna kuti ndidzakhale woimba ndikadzakula. Nyimbo zinkandisangalatsa kwambiri moti ndinaphunziranso kuimba gitala. Patapita nthawi, ndinayambitsa bandi ya chamba cha rock ndi anzanga ena ndipo tinkakaimba m’malo osiyanasiyana. Akatswiri ena ojambula nyimbo anachita chidwi ndi nyimbo zanga ndipo anandilonjeza kuti azindithandiza. Ndinachitanso mgwirizano ndi kampani ina yayikulu yojambula nyimbo. Nyimbo zanga zinatchuka kwambiri ndipo nthawi zambiri zinkamveka pawailesi ku Quebec.
Zinkaoneka ngati zinthu zikundiyendera. Ngakhale kuti ndinali wamng’ono, ndinatchuka kwambiri ndipo ndinkapanga ndalama zambiri ndi nyimbo zomwe ndinkaimba. Ndinkatanganidwa kwambiri moti kukacha, ndinkakachita masewera olimbitsa thupi, kukacheza ndi atolankhani, kukasainira pa zinthu zomwe anthu andipempha komanso kukachita nawo pulogalamu ya pa TV. Ndipo kukada, ndinkakaimba m’malo ambiri komanso kupita ku mapate. Kuti ndichotse mantha pachigulu cha anthu, ndinayamba kumwa mowa ndili wamng’ono kwambiri ndipo kenako ndinadzayamba kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Ndinalowerera kwambiri moti ndinkakonda chiwerewere.
Anthu ambiri ankandisirira chifukwa ankaona kuti ndimasangalala. Koma sindinkapeza mtendere mumtima makamaka ndikakhala kwandekha. Nthawi zambiri ndinkakhala ndi nkhawa komanso wopanikizika. Mwadzidzidzi anthu awiri omwe ankandithandiza kwambiri potulutsa nyimbo anamwalira ndi matenda a EDZI. Ndinasokonezeka kwambiri. Ngakhale kuti ndinkakonda kwambiri kuimba, zinthu zomwe ndinkachita zinkandinyansa kwambiri.
MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA
Ngakhale ndinali munthu wotchuka, ndinkaona kuti zinthu sizikuyenda bwino padzikoli. Ndinkadzifunsa kuti, “n’chifukwa chiyani pali zinthu zambiri zopanda chilungamo?” Sindinkamvetsa kuti n’chifukwa chiyani Mulungu ankangoyang’anira osachitapo chilichonse. Nthawi zambiri ndinkapempha Mulungu kuti andithandize. Nthawi ina nditachoka kutchuthi, ndinayambiranso kuwerenga Baibulo. Ngakhale kuti zinthu zambiri zomwe ndinkawerengazo sindinkazimvetsa, ndinkaona kuti dzikoli lilidi kumapeto.
Tsiku lina ndikuwerenga Baibulo, ndinapeza kuti nthawi ina Yesu anapita kuchipululu komwe anakasala kudya kwa masiku 40. (Mateyu 4:1, 2) Ndinayamba kuganiza kuti ngati inenso ndingachite zomwezo, ndiye kuti Mulungu andithandiza kuti ndimudziwe. Choncho ndinakonza tsiku loti ndidzayambe kusala kudya. Kutangotsala mawiki awiri kuti ndiyambe kusala kudya, a Mboni za Yehova awiri anagogoda pakhomo langa. Ndinawalandira ndi manja awiri ngati kuti ndimadziwa zoti abwera. Ndinayang’anitsitsa m’modzi wa a Mboniwo dzina lake Jacques n’kumufunsa kuti: “Kodi tingadziwe bwanji kuti tikukhaladi m’masiku otsiriza?” Poyankha, anangotsegula Baibulo lake ndikuwerenga pa 2 Timoteyo 3:1-5. Kenako ndinawapanikiza ndi mafunso ambirimbiri. Ndinachita chidwi ndi mayankho ogwira mtima omwe anandipatsa chifukwa ankachokera m’Malemba. Jacques ndi mnzakeyo atabwera kunyumba kwa maulendo angapo, ndinaona kuti panalibenso chifukwa chosalira kudya.
Ndinayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboniwo. Posakhalitsa ndinameta tsitsi langa lalitali ndipo ndinayamba kupezeka pamisonkhano yonse ku Nyumba ya Ufumu. Mmene abale ndi alongo ankandilandirira kumisonkhanoko, zinanditsimikizira kuti ndapezadi choonadi.
Ndinkafunika kusintha zambiri kuti ndizitsatira zimene ndinkaphunzira m’Baibulo. Mwachitsanzo, ndinkafunika kusiya kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo komanso kuchita zachiwerewere. Ndinkafunikanso kusintha khalidwe langa lodzikonda kuti ndizichita zinthu moganizira ena. Ndinali ndi ana anga awiri omwe ndinkalera ndekha. Ndinkafunika kuyesetsa kusamalira anawo komanso kuwathandiza kuti azikonda Mulungu. Ndiyeno ndinasiya kuimba n’kuyamba kugwira ntchito ya malipiro ochepa ku fakitale inayake.
Sizinali zophweka kuti ndisinthe moyo wanga. Pamene ndinkayesetsa kuti ndisiye kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, ndinkavutika ndi chibaba ndipo nthawi zina ndinkapezeka kuti ndayambiranso. (Aroma 7:19, 21-24) Zinkandivutanso kwambiri kuti ndisiyiretu khalidwe la chiwerewere. Ntchito imene ndinkagwira inali yotopetsa komanso ya malipiro ochepa. Ndinkafunika kuigwira kwa miyezi itatu kuti ndipeze ndalama yofanana ndi imene ndinkapeza pa maola awiri okha pa nthawi imene ndinali woimba.
Kupemphera ndiponso kuwerenga Baibulo tsiku lililonse kunandithandiza kwambiri kuti ndisinthe. Ndinkasankha Malemba ogwirizana ndi khalidwe langa ndipo ankandilimbikitsa kwambiri. Mwachitsanzo, ndinkakonda lemba la 2 Akorinto 7:1 lomwe limalimbikitsa Akhristu kuti ‘adziyeretse ndipo achotse chinthu chilichonse choipitsa thupi kapena mzimu.’ Lemba linanso lomwe linanditsimikizira kuti n’zotheka kusintha ndi la Afilipi 4:13 lomwe limanena kuti: “Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kuchokera kwa iye amene amandipatsa mphamvu.” Yehova Mulungu anayankha mapemphero anga ndipo anandithandiza kumvetsa mfundo za m’Baibulo komanso kuzigwiritsa ntchito. Zimenezi zinandipangitsa kuti ndidzipereke kwa iye. (1 Petulo 4:1, 2) Pofika mu 1997, ndinabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova.
MADALITSO AMENE NDAPEZA
Sindikukayikira kuti ndikanakhala kuti sindinasinthe khalidwe langa, sindikanafika lero. Panopa ndimaona kuti ndikusangalala zenizeni. Komanso nditakhala wa Mboni ndinakwatira Elvie. Mkazi wangayu amandithandiza kwambiri. Tonse ndife atumiki a nthawi zonse ndipo timasangalala kuphunzitsa anthu ena Baibulo. Ndimachita kumva bwino mumtimamu moti ndimakhala wokhutira. Ndimasangalala kwambiri kuti Yehova anandikoka kuti ndizimutumikira.—Yohane 6:44.