Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

BAIBULO LIMASINTHA ANTHU

“Sindinkachedwa Kupsa Mtima”

“Sindinkachedwa Kupsa Mtima”
  • Chaka Chobadwa: 1975

  • Dziko: Mexico

  • Poyamba: Ndinkakonda zachiwawa ndipo ndinamangidwapo

KALE LANGA

 Ndinabadwira m’katauni kena kakang’ono kotchedwa San Juan Chancalaito ku Mexico. Makolo anga ndi a mtundu wa Chimaya. M’banja mwathu tinabadwa ana 12 ndipo ine ndi wa nambala 5. Ndili mwana, ine ndi azibale anga tinkaphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova. Koma chomvetsa chisoni n’chakuti nthawi imeneyo sindinatsatire mfundo zomwe tinkaphunzira m’Baibulo.

 Nditafika zaka 13 ndinayamba kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo komanso kuba. Pamsinkhu umenewu ndinachoka pakhomo pa makolo anga ndipo sindinkakhazikika malo amodzi. Ndili ndi zaka 16, ndinayamba kugwira ntchito pa famu ina yolima chamba. Ndinakhala kumeneko pafupifupi kwa chaka chimodzi. Tsiku lina usiku tinkafuna kuzembetsa matumba a chamba paboti kuti tikagulitse, koma gulu lina lokhala ndi mfuti lomwe linkazembetsanso mankhwala linatipeza. Atayamba kuwombera ndinathawira m’madzi n’kuyamba kusambira mpaka kuwoloka mtsinje. Kenako ndinathawira ku United States.

 Ku United States ndinapitiriza kugulitsa mankhwala osokoneza bongo ndipo zimenezi zinandibweretsera mavuto ambiri. Ndili ndi zaka 19, ndinamangidwa chifukwa cha kuba moopseza ndi mfuti komanso kufuna kupha anthu. Kundendeko ndinalowa m’gulu linalake la zigawenga ndipo ndinapitiriza kuchita zinthu zambiri zachiwawa. Chifukwa cha zimenezi, akuluakulu a kundendeko ananditumiza ku ndende ina ya chitetezo chokhwima mumzinda wa Lewisburg, ku Pennsylvania.

 Kundende ya ku Lewisburg, makhalidwe anga anafika poipa kwambiri. Popeza kuti ndinali nditadzilemba kale matatuu, sindinavutike kudziwana ndi gulu lina la zigawenga. Ndinkachita zinthu mwankhanza kwambiri ndipo ndinkangokhalira kuchita ndewu. Tsiku lina tinamenyana ndi akaidi anzathu kundende. Inali ndewu yoopsa kwambiri moti tinamenyana ndi ndodo komanso zitsulo. Kuti ndewuyi ithe, alonda anapopera utsi wokhetsa misozi. Kenako akuluakulu a ndende anandiika m’kachipinda kosungiramo anthu oopsa. Ndinali ndi mtima wapachala komanso ndinkakonda kutukwana. Ndinkangokhalira kumenya anthu. Ndikachita zimenezi ndinkamva bwino kwambiri ndipo sindinkadziimbanso mlandu.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA

 Popeza kuti nthawi zambiri ndinkangokhala ndekhandekha m’kachipinda kaja, ndinayamba kumawerenga Baibulo kuti ndizitayitsako nthawi. Tsiku lina, mlonda wina anandipatsa buku lakuti Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha M’paradaiso pa Dziko Lapansi. a Ndikamawerenga bukuli ndinkakumbukira zinthu zambiri zomwe ndinaphunzira ndili mwana. Zimenezi zinandichititsa kuona kuti ndalowerera kwambiri komanso makhalidwe anga afika poipa kwambiri. Ndinaganiziranso za banja lathu. Pa nthawiyi, azichemwali anga awiri aja anali atakhala a Mboni za Yehova. Kenako ndinadzifunsa kuti, ‘Ndiye kuti azichemwali angawa adzakhala ndi moyo mpaka kalekale m’paradaiso?’ Nanga ineyo ndilephelerenji? Kuchokera pamenepo ndinatsimikiza zosintha moyo wanga.

 Komabe ndinkadziwa kuti pakufunika winawake wondithandiza kuti ndisinthe moyo wanga. Choyamba, ndinapempha Yehova Mulungu kuti andithandize. Kenako ndinalemba kalata ku nthambi ya Mboni za Yehova ku United States yopempha kuti anditumizire munthu woti azidzandiphunzitsa Baibulo. Ofesiyi inatumiza munthu kuchokera kumpingo wapafupi ndi kundende imene ndinali. Pa nthawiyo anthu amene si achibale anga sankaloledwa kudzandiona. Ndiyeno wa Mboniyo ankangonditumizira makalata ondilimbikitsa komanso mabuku kudzera pa imelo ndipo zimenezi zinandithandiza kuti ndisinthe mosavuta.

 Ndimaona kuti ndinasintha kwambiri nditatsimikiza zochoka m’gulu la zigawenga lomwe ndinakhalamo kwa nthawi yayitali. Mkulu wathu wa zigawenga anaikidwanso m’kachipinda kosungiramo anthu oopsa. Ndiyeno pa nthawi yomwe tinkachita masewera olimbitsa thupi ndinamuuza kuti ndikufuna ndikhale wa Mboni za Yehova. Ndinadabwa akundiyankha kuti: “Ngati ukunenadi zoona, panga zomwezo. Ine sindingalimbane ndi Mulungu. Koma ngati ukungofuna kuthawa gulu lathuli, uona polekera.”

 Patadutsa zaka ziwiri, akuluakulu oyang’anira ndende anaona kuti khalidwe langa lasintha moti anayamba kundikonda kwambiri. Mwachitsanzo, alonda anasiya kumandimanga akamandiperekeza kubafa. Ndipo mlonda wina anayamikira makhalidwe anga abwino moti anandilimbikitsa kuti ndisasinthenso. Kuwonjezera pamenepa, m’chaka changa chomaliza, oyang’anira ndende ananditumiza ku kampu ina ya kufupi ndi ndendeyi komwe kunali chitetezo chocheperako. Mu 2004, nditakhala m’ndende kwa zaka 10, ananditulutsa n’kunditumiza kwathu ku Mexico pa basi ya kundende.

 Nditangofika ku Mexico ndinafufuza komwe kunali Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova. Ndinasonkhana koyamba nditavala zovala za akaidi chifukwa zovala zabwino zomwe ndinali nazo zinali zokhazo. Koma a Mboniwo anandilandira bwino kwambiri posatengera mmene ndinavalira. Zimenezi zinandichititsa kuona kuti ndili pakati pa Akhristu enieni. (Yohane 13:35) Kenako akulu a mumpingowo anakonza zoti munthu wina azindiphunzitsa Baibulo. Pa 3 September 2005, ndinabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova. Pa nthawiyi n’kuti patadutsa chaka chimodzi kuchokera pamene ndinayamba kuphunzira.

 Mu January 2007, ndinayamba utumiki wa nthawi zonse ndipo ndinkathera maola 70 mwezi uliwonse ndikuphunzitsa anthu. Mu 2011, ndinalowa nawo Sukulu Yophunzitsa Baibulo ya Abale Osakwatira yomwe masiku ano imatchedwa Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu. Sukuluyi inandithandiza kwambiri kuti ndizitha kukwaniritsa udindo wanga mumpingo.

Panopa ndimasangalala kuphunzitsa ena kuti nawonso azikhala mwamtendere

 Mu 2013, ndinakwatira mlongo wina dzina lake Pilar. Ndikamafotokozera mkazi wanga zimene ndinkachita kale, zimamuvuta kukhulupirira. Panopa sindinong’oneza bondo kuti ndinasiya zomwe ndinkachita. Ine ndi mkazi wanga timakhulupirira kuti mmene moyo wanga ulili panopa ndi umboni wakuti Baibulo lili ndi mphamvu zotha kusintha munthu.​—Aroma 12:2.

PHINDU LIMENE NDAPEZA

 Ndimangomva ngati mawu a Yesu a pa Luka 19:10 analembera ineyo. Iye anati: ‘Pakuti ndinabwera kudzafunafuna ndi kupulumutsa anthu osochera.’ Panopa sindimadzionanso kuti ndine wosochera. Ndinasiya kumangokhalira kupsera mtima anthu. Ndimathokoza kuti Baibulo linandithandiza kudziwa kuti moyo uli ndi cholinga. Tsopano ndimakhala mwamtendere ndi anthu ena. Koma ndimaona kuti chofunika kwambiri ndi ubwenzi womwe ndili nawo ndi Yehova, yemwe ndi Mlengi wathu.

[MAWU A M’MUNSI]

a Bukuli linkafalitsidwa ndi a Mboni za Yehova koma panopa anasiya kusindikiza. Panopa buku lomwe amagwiritsa ntchito pophunzitsa anthu Baibulo ndi lakuti Zimene Baibulo Limaphunzitsa.