Ankavala Yunifolomu Yokhala ndi Kachigamba Kapepo
Maud yemwe amakhala ku France, amagwira ntchito pasukulu ina. Iye ntchito yake ndi yothandiza ana olumala panthawi yomwe akuphunzira. Chaposachedwapa, ana a m’kalasi ina ankaphunzira za anthu ambirimbiri omwe anaphedwa kundende zozunzirako anthu mu ulamuliro wa boma la Nazi ku Germany. Panthawiyo akaidi ankawapatsa yunifolomu yosokerera kachigamba kamtundu winawake. Mtundu komanso mmene kachigambako ankakadulira, zinkaimira mlandu umene munthuyo anamangidwira.
Ponena za kachigamba kapepo kokhala ndi makona atatu komwe ankakasokerera pa yunifolomu ya akaidi ena, mphunzitsi wina ananena kuti: “Ndikuganiza kuti ankawapatsa yunifolomu ya kachigambaka chifukwa anthu ake ankagonana amuna kapena akazi okhaokha.” Pambuyo poti ana aweruka, Maud analankhula ndi mphunzitsiyo ndipo anamufotokozera kuti boma la Nazi linkapereka yunifolomu yokhala ndi kachigambaka kwa akaidi a Mboni za Yehova. * Maud analonjeza zomubweretsera mphunzitsiyo zinthu zina zofotokoza za nkhaniyi. Mphunzitsiyo anavomera ndipo anapemphanso Maud kuti adzafotokozere ana a sukulu zokhudza nkhaniyi.
Tsiku lina, mphunzitsi winanso anaonetsa ana a kalasi ina tchati cha zizindikiro zosiyanasiyana zomwe zinkaikidwa pa yunifolomu ya akaidi. Tchaticho chinasonyeza kuti kachigamba kansalu yamakona atatu kamtundu wapepo, kankaimira a Mboni za Yehova. Ana ataweruka, Maud anauza mphunzitsiyo kuti akudziwa bwino zokhudza nkhaniyo. Mphunzitsiyo anasangalala ndi zomwe anauzidwazo moti anakonza zoti Maud afotokozere ana a m’kalasiyo zokhudza nkhaniyi.
Maud anakonzekera kuti akalankhule ndi ana a m’kalasi yoyamba ija kwa 15 minitsi. Koma nthawiyo itafika, anauzidwa kuti: “Takupatsa ola lathunthu.” Maud anayamba kuonetsa vidiyo yofotokoza mmene boma la Nazi linkazunzira a Mboni za Yehova. Vidiyoyo itafotokoza kuti boma la Nazi linalanda ana Amboni okwana 800 kuchoka kwa makolo awo, Maud anaimitsa kaye vidiyoyo n’kuyamba kuwerenga nkhani zokhudza ana ena atatu omwe anali pagululo. Atamaliza kuonetsa vidiyo ija, Maud anamaliza ndikuwerenga kalata ya m’chaka cha 1940. Kalatayo inalembedwa ndi mnyamata wina Wamboni yemwe anali ndi zaka 19 dzina lake Gerhard Steinacher. Mnyamatayu anali wa ku Austria ndipo analemba kalatayi potsanzikana ndi makolo ake kutangotsala maola ochepa kuti aphedwe ndi asilikali a boma la Nazi. *
Maud anakaonetsanso vidiyoyi ku kukalasi yachiwiri ija. Tikuyamikira kwambiri kuti Maud anachita zinthu molimba mtima. Aphunzitsi awiri aja tsopano amakumbukira kunena zokhudza a Mboni za Yehova akamaphunzitsa za anthu omwe anazunzidwa kundende zozunzirako anthu za boma la Nazi.
^ Panthawi ya Nkhondo Yachiwiri ya Padziko Lonse, Mboni za Yehova za ku Germany zomwe zinkadziwikanso kuti Bibelforscher (Ophunzira Baibulo), zinamangidwa chifukwa chokana kukhala kumbali ya boma la Nazi.
^ Gerhard Steinacher anagamulidwa kuti aphedwe chifukwa chokana kulowa m’gulu la asilikali a dziko la Germany. M’kalata yake yotsanzika analemba kuti: “Ndidakali mwana ndipo pandekha sindingathe kupirira. Ndikupempha Ambuye kuti andithandize.” Gerhard anaphedwa m’mawa wa tsiku lotsatira. Pamanda ake panalembedwa mawu akuti: “Anafa pofuna kulemekeza Mulungu.”