Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

A Mboni za Yehova Anayankha Modekha Atakumana ndi Ansembe Olusa

A Mboni za Yehova Anayankha Modekha Atakumana ndi Ansembe Olusa

 Woyang’anira dera wina wa ku Armenia dzina lake Artur amachezera mpingo wina wa Mboni za Yehova. Iye anapeza kuti abale amumpingowu sanayambe ulaliki wa m’malo opezeka anthu ambiri womwe umaphatikizapo kugwiritsa ntchito timashelefu tamatayala. Pofuna kulimbikitsa abale kuti azichita ulaliki wa mtunduwu, Artur ndi mkazi wake Anna komanso wa Mboni wina dzina lake Jirayr anaika ka shelefu m’tauni inayake yaing’ono. Iwo anasankha kuima pamalo amene anthu ambiri oyenda pansi amadutsa.

 Nthawi yomweyo anthu odutsa anayamba kusonyeza chidwi ndipo ankatenga mabuku ndi magazini. Komabe otsutsa nawonso anaona kuti abale athu akulalikira pogwiritsa ntchito kashelefu. Ansembe awiri anafika pamene panali kashelefuko ndipo mwadzidzidzi, mmodzi anangokamenya theche. Kenako anamenya mbama Artur n’kumugwetsera magalasi ake a maso. Artur, Anna ndi Jirayr anayesetsa kukambirana ndi ansembewo moleza mtima koma sizinathandize. Ansembewo anapondaponda kashelefuko ndipo mabuku onse anangomwazikana. Pamapeto pake anayankhula mawu a chipongwe komanso oopseza a Mboniwo n’kumapita.

 Artur, Anna ndi Jirayr anapita kupolisi ya m’deralo n’kukadandaula za nkhaniyi. Iwo anafotokoza zomwe zinachitika ndipo anauzanso apolisi angapo ndi ogwira ntchito ena mfundo za m’Baibulo. Kenako, a Mboni atatuwa anauzidwa kuti apite kwa mkulu wa apolisiwo. Poyamba ankangofuna kumva madandaulo awo. Koma atamva kuti Artur yemwe ndi mwamuna wadzitho sanabwezere a nsembe aja atamumenya mbama, wapolisiyo anasiya kufunsa mafunso okhudza mlanduwo ndipo anayamba kufunsa zomwe a Mboni amakhulupirira. Zimenezi zinachititsa kuti anthuwa akambirane kwa maola 4. Wapolisiyo anasangalala kwambiri ndi zimene anauzidwazo moti ananena mofuula kuti: “Chipembedzo koma chimenechi! Nanenso ndikufuna kulowa chipembedzo chimenechi!”

Artur ndi Anna

 Tsiku lotsatira Artur atapitanso kokalalikira munthu wina amene ankaona zomwe zinachitika zija anapita pamene Artur anaima. Iye anathokoza Artur chifukwa chougwira mtima komanso kusabwezera. Ananenanso kuti zomwe anaona zamuchititsa kuti asamawapatsenso ulemu ansembe aja.

 Madzulo a tsikuli, mkulu wa apolisi uja anauza Artur kuti apitenso kupolisi kuja. Koma m’malo mokambirana za mlandu uja ankangofunsa mafunso ambirimbiri okhudza nkhani za m’Baibulo. Apolisi enanso awiri anabwera pamakambirano aja.

 Tsiku lotsatira Artur anapitanso kwa mkulu wa apolisi uja kuti akamusonyeze mavidiyo a nkhani za m’Baibulo. Mkulu wa apolisiyu anaitananso apolisi ena kuti adzaonere nawo mavidiyowo.

 Khalidwe loipa la ansembe aja linathandiza kuti apolisi ambiri amve koyamba uthenga wa m’Baibulo. Apolisiwa anadzionera okha kuti a Mboni za Yehova ndi anthu a khalidwe labwino.