Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Ankabisa Notsi Pansi pa Mashini Ochapira Zovala

Ankabisa Notsi Pansi pa Mashini Ochapira Zovala

 Zarina atabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova, anachoka ku Russia komwe ankakhala ndipo anabwerera kwawo ku Central Asia. Iye anali wokonzeka kuphunzitsa ana ake aakazi awiri mfundo za m’Baibulo. Chifukwa choti analibe ndalama zokwanira, iye, mchimwene wake ndi mlamu wake, ankakhala kwa makolo ake m’nyumba yawo yomwe inali yopanda chipinda. Makolo ake anamuletsa kuti asaphunzitse ana ake mfundo za m’Baibulo. Anauzanso anawo kuti asamalankhule ndi mayi awo nkhani zokhudza Baibulo.

 Zarina anaganizira kwambiri zimene angachite kuti athandize ana ake kuphunzira za Yehova. (Miyambo 1:8) Choncho anapemphera kwa Yehova mochokera pansi pamtima kuti amupatse nzeru komanso kuti amutsogolere. Kenako iye anayamba kuchita zinthu zomwe zikanathandiza kuti zomwe anapemphererazo zitheke. Iye ankapita kukayenda ndi ana akewo ndipo ankacheza nawo nkhani zokhudza zinthu zochititsa chidwi zomwe zili m’chilengedwe. Zimenezi zinathandiza kuti anawo ayambe kuchita chidwi ndi Mlengi.

 Kenako Zarina anapeza njira yoti akulitse chidwi cha anawo pogwiritsa ntchito buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? * Iye ankakopera ndime komanso mafunso a m’bukulo patimapepala. Iye analembanso zinthu zina zoonjezera pofuna kuthandiza ana ake kumvetsa zomwe amawerengazo. Kenako anabisa timapepalato ndi pensulo pansi pa mashini ochapira zovala m’bafa. Anawo ankawerenga ndimezo n’kulemba mayankho awo akapita kubafako.

 Zarina anakwanitsa kuphunzira machaputala awiri a buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani ndi ana akewa pogwiritsa ntchito njira imeneyi asanapeze nyumba ina yoti azikhala. Kenako anasamuka ndipo pa nthawiyi anali womasuka kulera anawo popanda chosokoneza. Mu October 2016, atsikanawa anabatizidwa ndipo anasangalala kuti amayi awo anachita zinthu mwanzeru kuti awathandize kuphunzira choonadi chochokera m’Baibulo.

^ Panopa anthu ambiri amagwiritsa ntchito buku la Zimene Baibulo Limaphunzitsa.