Ankaganiza Kuti Ndi M’busa
Tsiku lina a Osman, akazi awo ndi mwana wawo wamkazi ankalalikira pogwiritsa ntchito kashelefu kamatayala kunja kwa manda enaake m’dziko la Chile. Mwadzidzidzi, gulu la anthu odzaika maliro linafika pamalowa likuimba nyimbo mofuula. Ena mwa anthuwo ankaganiza kuti a Osman ndi abusa a tchalitchi chawo cha evanjeliko. Choncho anapita pamene anali, kuwakumbatira, n’kufuula kuti: “Zikomo kwambiri chifukwa chofika pa nthawi yake, Abusa, timakuyembekezerani!”
Ngakhale kuti a Osman anayesa kufotokoza kuti iwowo si abusa a tchalitchicho, anthuwo sanamve chifukwa cha phokoso. Kenako gululo litalowa mkati mwa manda, anthu angapo anabwerera n’kuuza a Osman kuti, “Abusa, tikukudikirani kumandaku.”
Phokoso lija litatha, a Osman anafotokozera anthuwo kuti iwowo ndi ndani komanso chifukwa chimene anapezekera kumeneko. Anthuwo ananena kuti akhumudwa chifukwa choti abusa awo sanabwere kenako anapempha a Osman kuti, “Mungabwere kuti mutifotokozereko mawu ochepa a m’Baibulo?” A Osman anavomera.
Pamene ankapita kumanda, a Osman anafunsa anthuwo mafunso okhudza munthu yemwe anamwalirayo ndipo anaganizira malemba angapo oti awawerengere. Atafika komwe kunali gulu la anthuwo, anayamba ndi kuzidziwikitsa komanso kufotokoza kuti monga wa Mboni za Yehova, amagwira ntchito yolalikira uthenga wabwino kwa anthu.
Kenako, anagwiritsa ntchito lemba la Chivumbulutso 21:3, 4 ndi la Yohane 5:28, 29 pofotokoza kuti sichinali cholinga cha Mulungu kuti anthu azimwalira. Iwo ananena kuti ndithudi posachedwapa Mulungu aukitsa akufa ndipo adzakhala ndi chiyembekezo chokhala padziko lapansi kwamuyaya. A Osman atamaliza kulankhula, anthu ambiri anawakumbatira ndi kuwathokoza chifukwa chofotokoza “uthenga wabwino wochokera kwa Yehova.” Kenako anabwerera pakashelefu kamatayala kaja.
Mwambo wamaliro utatha, anamfedwa anapita pakashelefuko ndipo anafunsa a Osman ndi banja lawo mafunso okhudzana ndi Baibulo. Iwo anacheza ndi anthuwo kwa nthawi yaitali ndipo anthu anatenga pafupifupi mabuku onse omwe anali pa kashelefuko.