A Joseph Anaperekezedwa ndi Apolisi
Ngati ndinu wa Mboni za Yehova ndipo mukulalikira nyumba ndi nyumba, kodi mungamve bwanji apolisi atamakuperekezani khomo lililonse? Zimenezi n’zimene zinachitikira a Joseph a ku Micronesia mu 2017. Iwo limodzi ndi anzawo atatu omwenso ndi a Mboni ankagwira ntchito yapadera yolalikira kwa anthu a m’zilumba zakutali.
Cha m’ma 12 koloko masana, a Mboniwo anafika pakachilumba komwe kali ndi anthu okwana 600 ndipo analandiridwa ndi meya wa pachilumbacho. Pofotokoza zomwe zinachitika a Joseph anati: “Meyayo ananena kuti apolisi akhoza kutiperekeza pagalimoto yawo kunyumba zonse. Zimenezi zinatidabwitsa kwambiri koma tinakana mwaulemu chifukwa tinkafuna kuyendera anthu m’nyumba zawo mmene timachitira nthawi zonse.”
Kenako ofalitsawo ananyamuka wapansi ndipo ankafunitsitsa kulalikira kwa anthu ambiri. Iwo ananena kuti: “Anthu anatilandira bwino ndipo anali ndi chidwi ndi uthenga wathu. Zimenezi zinachititsa kuti tizikhala nthawi yayitali panyumba iliyonse kuposa mmene tinkaganizira.”
Pa nthawi ina galimoto ya apolisi inadutsa a Joseph kawiri ndipo kachitatu inaima. Apolisiwo anafunsa a Joseph ngati zingatheke kuti awanyamule kuti awapititse ku nyumba zomwe zinali zitatsala. A Joseph ananena kuti: “Ndinawauza kuti ayi. Koma apolisiwo anakakamira ndipo ananena kuti, ‘Wangotsala ndi nthawi yochepa yokhalira pachilumba pano, ndiye tikuperekeza kunyumba zomwe zatsala.’ Pa nthawiyi sindinakane chifukwa panali nyumba zambiri zoti ndipiteko. Tikamayandikira nyumba iliyonse, apolisiwo ankandiuza dzina la eni ake a nyumbayo ndipo ankandiuza kuti akapanda kuyankha pambuyo poti ndagogoda, iwowo aziliza hutala ya galimoto kuti eniake a nyumbawo adziwe kuti kwabwera anthu.”
“Zimene anachitazi zinatithandiza kuti tilalikire ku nyumba zonse tsiku limeneli. Tinagawira mabuku ambiri komanso tinagwirizana ndi anthu ambiri omwe anasonyeza chidwi kuti tidzapitenso.
Apolisiwo anauza a Joseph kuti “anasangalala kwambiri kulalikira nawo uthenga wabwino.” Pa nthawi yomwe a Mboniwo ankanyamuka, apolisi omwe anali pachilumbachi anawabayibitsa kwinaku akumwetulira mabuku omwe analandira ali m’manja.