Madzi Osefukira Anabweretsa Uthenga Wabwino
M’chaka cha 2017, abale ndi alongo okwanira 12 anayamba ulendo wapaboti kuchokera m’chigawo cham’mbali mwa nyanja chotchedwa Mosquito (Miskito) ku Nicaragua. Boti lomwe anakwera linkatchedwa Sturi Yamni. Mmodzi wa oyendetsa botilo, dzina lake Stephen, anati: “Cholinga chathu chinali kukalimbikitsa gulu laling’ono la a Mboni omwe ankakhala m’dera lina lakutali, komanso kukawathandiza kulalikira uthenga wabwino m’gawo lawo lomwe linali lalikulu kwambiri.”
Ulendo wawo unayambira padoko lotchedwa Pearl Lagoon ndipo anayenda makilomita 200 mumtsinje wotchedwa Río Grande de Matagalpa. Anthuwa sankadziwa kuti dzina la boti lawo lija, lomwe limatanthauza “Uthenga Wabwino” m’chinenero cha Miskito, lidzakhala ndi tanthauzo lapadera kwambiri kwa anthu am’deralo. Atayenda kwa maola 12, osawerengera nthawi imene anagona usiku, a Mboniwo anafika m’mudzi womwe ankapita wotchedwa La Cruz de Río Grande. A Mboni 6 akumeneko anawalandira mwansangala kwambiri.
Usiku wa tsiku lomwe anafikalo kunawomba chimphepo chamkuntho komanso kunagwa chimvula. Mvulayi inachititsa kuti mtsinje wa Río Grande de Matagalpa udzaze kwambiri. Patangodutsa maola ochepa, mtsinjewo unasefukira ndipo madzi anapitirizabe kukwera kwa masiku awiri. Nyumba ya Ufumu yam’mudziwo komanso nyumba za anthu ena zinalowa madzi. Alendowo ataona zimenezi, anayamba kuthandiza anthu kuchoka m’nyumba zawo. Ambiri mwa anthuwa anagona masiku awiri m’nyumba yansanjika ya wa Mboni wina.
Usiku wa tsiku lachitatu, meya wa ku La Cruz anapita kwa a Mboni amene anabwera kudzalalikira aja n’kukawapempha kuti athandizepo. Popeza boti la Sturi Yamni ndi lokhalo lomwe likanatha kuyenda mumtsinje wosefukirawo, meyayu anapempha abalewo kuti atenge gulu la anthu oti akathandize kumunsi kwa mtsinjewu. Abalewo anasangalala kuchita zimenezi.
Kutacha m’mawa, abale atatu ananyamuka paboti lija limodzi ndi gulu la anthu okathandiza aja. Stephen anati: “Pa nthawiyi mtsinjewo unali utakwiyiratu. Mitengo ikuluikulu yomwe inazulidwa ndi madzi inkayandama mumtsinjewo. Madziwo ankathamanga kwambiri mwina kuposa makilomita 18 pa ola limodzi ndipo ankachita thovu.” Ngakhale zinthu zinali zovuta chonchi, botilo linakwanitsa kufika kumidzi itatu.
A Mboni atatu aja anagwiritsa ntchito mwayi umenewu kulimbikitsa anthu omwe anakhudzidwa ndi madzi osefukirawo. Anagawiranso anthu magazini ya Galamukani! ya 2017 yomwe inali ndi mutu wogwirizana kwambiri ndi tsoka linachitikali. Mutu wake unali wakuti, “Zimene Tingachite Kuti Tipulumuke Pakachitika Ngozi Zadzidzidzi.”
Anthu am’midziyo anayamikira kwambiri zimene a Mboniwa anachita powathandiza komanso kuwalimbikitsa ndi uthenga wa m’Baibulo. Ena anati: “Anthu amenewa sanadandaule kutithandiza pa nthawi yovutayi.” Enanso ankati: “Iwo amakondadi anzawo.” Anthuwa ataona zimene a Mboni anachita pothandiza abale ndi alongo awo komanso anthu ena, ambiri anayamba kumvetsera uthenga wotonthoza wa m’Baibulo.
Marco, mmodzi wa anthu omwe ankayendetsa boti la Sturi Yamni akupita kukauza anthu uthenga wabwino
Boti la Sturi Yamni litaima m’mudzi wina womwe unasefukira madzi