Mfundo Zothandiza Anthu Ogwira Ntchito Zachipatala Omwe Ali Ndi Nkhawa
Bryn, yemwe amakhala ku North Carolina ku U.S.A., ndi mmodzi wa anthu omwe ali mu Komiti Yolankhulana ndi Achipatala m’deralo. Komitiyi imagwira ntchito ndi achipatala posamalira odwala omwe ndi a Mboni za Yehova.
Chifukwa cha mliri wa COVID-19, zipatala zambiri sizinkalola anthu ena kulowa kuti akaone odwala. Bryn anaimbira foni mkulu wanthambi yoyang’anira odwala pachipatala china m’deralo kuti adziwe mmene angaperekere thandizo kwa odwala omwe ndi a Mboni za Yehova.
Foni imene anaimbayo inafikira kwa munthu wina yemwe anali wachiwiri kwa wamkulu wapachipatalayo. Chifukwa chakuti pachipatalapo sankalola kukaona odwala, anapempha ngati nambala yake ingaperekedwe kwa odwala omwe ndi a Mboni n’cholinga choti alankhulane nawo. Iwo anamuyankha kuti n’zotheka.
Kenako Bryn anaganizira za ogwira ntchito pachipatalacho. Iye anamuuza wachiwiri kwa wamkulu wapachitalayo kuti akuyamikira kwambiri ntchito imene azachipatalawo akugwira ndipo akukhulupirira kuti onse ali bwino. Iye ananenanso kuti wawerenga kuti anthu ambiri a m’madera osiyanasiyana, makamaka ogwira ntchito zachipatala akumakhala ndi nkhawa kwambiri chifukwa cha mliriwu.
Mkuluyo anavomerezadi kuti COVID-19 wachititsa anthu ogwira ntchito zachipatala kuti akhale ndi nkhawa kwambiri.
Ndiyeno Bryn ananena kuti: “Pawebusaiti yathu pali nkhani zosiyanasiyana zimene zingathandize anthu kuchepetsa nkhawa. Mutapita pa webusaiti yathu ya jw.org n’kulemba mawu akuti ‘nkhawa’ mu kabokosi kofufuzira mukhoza kupezapo nkhani zimene zingalimbikitse anthu amene mumagwira nawo ntchito.”
Ndipo pamene ankakambirana mkuluyo anapitadi pa webusaitiyo n’kufufuza mawu akuti “nkhawa” ndipo ataona nkhani zimene zinapezeka anati: “Eee ndiwaonetsa abwana anga. Nkhanizi zithandiza kwambiri amene timagwira nawo ntchito komanso anthu ena. Ndizipulinta n’kuzigawa ka anthu onse.”
Patapita masiku ochepa, Bryn analankhulana ndi mkulu uja ndipo anamutsimikiziradi kuti anafika pawebusaiti yathu ndi kupulinta nkhani zokhudza nkhawa ndipo anazigawira kwa manesi ndi anthu ena ogwira ntchito pachipatalapo.
Bryn ananena kuti: “Mkuluyo anayamikira kwambiri chifukwa cha ntchito imene timagwira komanso chifukwa cha nkhani zolembedwa bwino. NKhanizi zinali zothandizadi kwambiri.”