Anadzipereka ndi Mtima Wonse ku Guyana
“Sindingathe kufotokoza chimwemwe chomwe ndinali nacho chifukwa chotumikira m’gawo lomwe kukufunika olalikira ambiri.” Zimenezi ndi zimene Joshua ananena. Iye amakhala ku United States koma nthawi ina anatumikirapo m’dziko la Guyana. Dzikoli lili ku South America ndipo anthu ambiri kumeneko ali ndi chidwi chofuna kuphunzira za Yehova. A Mboni ambiri omwe anatumikirapo m’dzikoli nawonso amamva ngati mmene Joshua anamvera. * Kodi tingaphunzire zotani kwa anthu amene anatumikirapo kumene kukufunika olalikira ambiri? Kodi zimene iwo ananena zingakuthandizeni bwanji kukonzekera kukatumikira kudziko lina ngati mukufuna kutero?
N’chiyani Chinawalimbikitsa Kukatumikira Kudziko Lina?
M’bale wina dzina lake Linel asanasamukire ku Guyana, ankalalikira kwawo ku United States m’gawo lomwe sililalikidwa kawirikawiri. Iye anati: “Tinali gulu la anthu 20 ndipo tinapatsidwa gawo loti tizilalikira m’dera lina la kumidzi ku West Virginia. Kugwira nawo ntchito yolalikira komanso kucheza ndi anthu kwa milungu iwiri yomwe ndinakhala m’deralo kunasintha moyo wanga. Ndinatsimikiza ndi mtima wanga wonse kuti ndizichita zonse zomwe ndingathe potumikira Yehova.”
Garth ndi mkazi wake Erica anayamba kuganizira mofatsa za cholinga chawo chokatumikira kudziko lina ndipo anasankha kupita ku Guyana. N’chifukwa chiyani anasankha kukatumikira kumeneku? Erica anafotokoza kuti: “Ine ndi mwamuna wanga tinkadziwana ndi banja lina lomwe linali litasamukira ku Guyana. Khama komanso chikondi chomwe anali nacho potumikira zinatilimbikitsa kuti nafenso tipite kumeneko.” Erica ndi Garth anatumikira mosangalala kwa zaka zitatu ndipo iwo ananena kuti unali “utumiki wosaiwalika.” Garth anati: “Tinalawa kutumikira m’dziko lina ndipo tinaona kuti utumiki umenewu ndi wabwino.” Iye ndi mkazi wake anadzalowa Sukulu ya Giliyadi ndipo panopa akutumikira ku Bolivia.
Anakonzekera Bwanji?
Mfundo za m’Baibulo zimatilimbikitsa kukhala moyo wosalira zambiri. (Aheberi 13:5) Timalimbikitsidwanso kuti tiziwerengera mtengo wake tikamapanga zosankha zazikulu pa moyo wathu. (Luka 14:26-33) Zimenezi zikuphatikizapo zosankha zokhudza kusamukira kudziko lina. Garth analemba kuti: “Tisanasamukire ku Guyana, ine ndi Erica tinasintha zinthu zina kuti tiyambe kukhala moyo wosalira zambiri. Kuti zimenezi zitheke, tinagulitsa bizinezi yathu, nyumba yathu komanso zinthu zonse zosafunika zomwe tinasunga m’nyumba yathu. Kuchita zimenezi kunatitengera zaka zingapo. Pa nthawi yomwe tinkachita zimenezi, sitinasinthe cholinga chathu chokatumikira ku Guyana pokhalabe ndi cholinga chathucho m’maganizo komanso tinkapita kudzikoli chaka ndi chaka.”
Chinthu china chofunika kuchiganizira ndi ndalama. M’madera ena, anthu omwe akutumikira m’gawo lomwe kukufunika olalikira ambiri amagwira ntchito m’dziko lomwe asamukiralo ngati malamulo a m’dzikolo amawalola kutero. Ena amagwirabe ntchito yomwe ankagwira kwawo pogwiritsa ntchito kompyuta. Ena amasankha kumapita kwawo kuti akagwire ntchito kwa nthawi yochepa. Paul ndi mkazi wake Sinead ankabwerera kwawo ku Ireland kukagwira ntchito pachaka kamodzi. Kuchita zimenezi kunawathandiza kuti atumikire ku Guyana kwa zaka 18, kuphatikizapo zaka 7 mwana wawo wamkazi atabadwa.
Lemba la Salimo 37:5 limati: “Lola kuti Yehova akutsogolere panjira yako, umudalire ndipo iye adzachitapo kanthu.” Christopher ndi Lorissa omwe kwawo ndi ku United States nthawi zonse ankapempherera cholinga chawo chokatumikira kudziko lina. Komanso pa kulambira kwawo kwa pabanja, anakambirana zimene anayenera kuchita kuti ziwayendere bwino akasamuka, ndipo analemba ubwino komanso mavuto omwe angakhalepo akasamuka. Chifukwa choti ankafuna kusamukira kudziko lomwe sakafunika kuphunzira chinenero china, iwo anasankha kusamukira ku Guyana chifukwa Chingelezi n’chimene chimagwiritsidwa ntchito kwambiri.
Kenako anachita zinthu zogwirizana ndi mfundo ya pa Miyambo 15:22, yomwe imati: “Zolingalira sizikwaniritsidwa ngati anthu sakambirana moona mtima, koma aphungu akachuluka zimakwaniritsidwa.” Choncho analembera ofesi ya nthambi yomwe imayang’anira ntchito yathu ku Guyana, * ndipo anafotokoza zokhudza iwowo komanso kuti anali okonzeka kukatumikira m’gawo limene kukufunika olalikira ambiri. Iwo anafunsanso ofesi ya nthambi zokhudza zachipatala, nyengo, komanso chikhalidwe cha m’dzikolo. Ofesi ya nthambiyo inayankha mafunso awo ndipo inapanga zoti athe kulumikizana ndi bungwe la akulu la m’dera lomwe adzasamukire.
Linel yemwe tamutchula kale uja, panopa ndi woyang’anira dera ku Guyana. Asanasamukire m’dzikoli, m’baleyu nayenso anagwiritsa ntchito mfundo ya pa Miyambo 15:22. Iye anati: “Kupatulapo kusunga ndalama za ulendowu, ndinalankhula ndi anthu ena omwe anatumikirapo m’dziko lina. Ndinakambirana za nkhaniyi ndi banja langa, akulu a mumpingo wanga ndiponso woyang’anira dera wathu. Komanso ndinawerenga nkhani zonse zomwe ndinapeza m’mabuku athu zokhudza kutumikira kumene kukufunika olalikira ambiri.”
Anthu ambiri omwe akufuna kukatumikira m’dziko lina amaona kuti ndi nzeru kupita kukaonako kaye. Joseph ndi mkazi wake Christina anati: “Nthawi yoyamba yomwe tinapita ku Guyana, tinakhalako kwa miyezi itatu. Nthawiyi inali yokwanira kudziwa kuti ndi kotani. Titabwerera kwathu, tinayamba kukonzekera, ndipo kenako tinasamuka.”
Anatani Kuti Azolowere Moyo Wina?
Kuti zinthu ziwayendere bwino potumikira Mulungu kudziko lina, abale ndi alongo omwe asamukira kumene kukufunika olalikira ambiri ayenera kukhala ndi mzimu wodzimana komanso wololera kusintha kuti azolowere chikhalidwe komanso moyo wa kumene asamukira. Mwachitsanzo, amene amachokera m’mayiko ozizira kwambiri n’kupita m’madera otentha, nthawi zambiri amapeza kuti m’maderawa muli tizilombo tosiyanasiyana. Joshua yemwe tamutchula kale uja anati: “Ndinali ndisanazolowere kukhala m’dera la tizilombo tambirimbiri. Ndipo tizilombo ta ku Guyana tinkaoneka tatikulu kwambiri! Koma patapita nthawi ndinazolowera. Komanso ndinaona kuti ukamasamalira pakhomo pako tizilombo timachepa. Zimenezi zikuphatikizapo kutsuka mbale, kutaya zinyalala komanso kuyeretsa m’nyumba pafupipafupi.”
Kuti munthu azolowere moyo wa m’dziko lina, amafunikanso kuzolowera zakudya zachilendo komanso kuphunzira kaphikidwe kake. Joshua anati: “Ine ndi mnzanga yemwe ndinkakhala naye tinapempha abale ndi alongo kuti atiphunzitse kaphikidwe ka zakudya za m’dera lomwe tinkakhala. Tikaphunzira kaphikidwe ka chakudya chinachake, tinkaitana abale ndi alongo ena a mumpingo wathu kuti adzadye nafe limodzi. Imeneyi inali njira yosangalatsa yodziwana ndi abale komanso kupeza anzathu.”
Pa nkhani ya chikhalidwe cha anthu a m’dera lomwe ankakhala, Paul ndi mkazi wake Kathleen anati: “Tinkafunika kuphunzira zimene anthu a m’deralo ankaona kuti ndi kachitidwe ka zinthu kaulemu komanso kavalidwe kovomerezeka ka anthu omwe amakhala m’madera otentha, ndipo zimenezi zinali zatsopano kwa ife. Choncho tinafunikira kudzichepetsa komanso kusintha, kwinaku tikuchita zinthu mogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo. Kuchita zinthu mogwirizana ndi chikhalidwe cha kumene tinkakhala kunachititsa kuti tizigwirizana kwambiri ndi abale mumpingo komanso zinathandiza kuti anthu azimvetsera tikamalalikira.”
Kodi Anapindula Bwanji?
Anthu ambiri omwe anakatumikirapo kudziko lina amanena zofanana ndi zimene Joseph ndi mkazi wake Christina ananena, omwe anati: “Madalitso omwe amakhalapo ndi ambiri kuposa mavuto omwe umakumana nawo. Kuchita zinthu zatsopano komanso zovuta kunatithandiza kuti tisinthe zinthu zomwe tinkaziona kuti n’zofunika. Zinthu zomwe poyamba tinkaziona kuti ndi zofunika kwambiri tinasiya kuziona kukhala zofunika. Zinthu zomwe tinakumana nazo zinatilimbikitsa kupitiriza kuchita zonse zomwe tikanatha potumikira Yehova. Tinkakhala moyo wokhutira ndi zimene tinkachita.”
Erica yemwe tamutchula uja anati: “Kutumikira kumene kukufunika olalikira ambiri kwathandiza ine ndi mwamuna wanga kumvetsa bwino zomwe kudalira Yehova kumatanthauza. Taona dzanja lake likutithandiza m’njira zomwe tinali tisanazionepo. Ndiponso kukumana ndi zinthu zatsopano limodzi kunatithandiza kuti tizigwirizana kwambiri monga banja.”