DECEMBER 10, 2019
ALBANIA
Ku Albania Kwachitika Chivomezi Champhamvu
Palibe wa Mboni aliyense yemwe anaphedwa kapena kuvulala chifukwa cha chivomezi chomwe chachitika ku Albania posachedwapa. Chivomezichi chinali champhamvu kwambiri pa zivomezi zomwe zakhala zikuchitika m’dzikoli m’zaka 40 zapitazi. Komabe, nyumba 35 za abale athu komanso nyumba zitatu zomwe zinkagwiritsidwa ntchito ngati Nyumba za Ufumu sizilinso malo otetezeka.
Chivomezichi chinachitika pa 26 November, 2019 ndipo chinali champhamvu zokwana 6.4. Anthu 51 anafa, oposa 3,000 anavulala komanso anthu masauzande ambiri anathawa m’nyumba zawo. A Mboni omwe anathawa m’nyumba zawo akukhala ndi achibale awo kapenanso abale ndi alongo a m’mipingo ina. Mipingo yomwe Nyumba za Ufumu zake zinawonongeka, ikusonkhana m’Nyumba za Ufumu zina m’madera omwe sanakhudzidwe ndi chivomezichi.
Mkulu wa mumpingo wina anafotokoza mmene kukhala okonzeka ngozi isanachitike kunathandizira banja lake. Iye anati: “Chivomezi chitangochitika, nthawi yomweyo tinatenga ‘zikwama za pa nthawi ya zinthu zogwa mwadzidzidzi’ ndipo tinatuluka m’nyumba. M’zikwamamo tinasungamo zinthu zofunika monga: mabulangete, madzi, mankhwala komanso chakudya. Tikuthokoza kwambiri Yehova ndi Bungwe Lolamulira chifukwa chotisonyeza chikondi.”
Mwamsanga, oyang’anira madera anapita kukalimbikitsa abale athu kumalo omwe anakhudzidwa ndi chivomezichi. Woyang’anira dera wina ndi mkazi wake anathawa m’nyumba yawo itawonongeka. Ngakhale kuti anakumana ndi mavuto amenewa, woyang’anira derayo ndi mkazi wake ankalimbikitsa ena kwa nthawi yaitali.
Abale a m’Komiti ya Nthambi anapitanso kukayendera madera omwe anakhudzidwa kwambiri ndi chivomezichi. Komiti yopereka chithandizo ikuyendetsa ntchito yothandiza abale ndi alongo omwe anakhudzidwa ndi ngoziyi.
Tikupemphera kuti abale ndi alongo athu ku Albania apitirize kupirira. Tikuyembekezera nthawi imene sikudzakhalanso ngozi zam’chilengedwe.—Aroma 8:25.