7 JANUARY, 2022
ALBANIA
Tatha Zaka 100 Tikulalikira Uthenga Wabwino ku Albania Ngakhale Kuti Ntchito Yathu Inali Italetsedwa kwa Zaka Zambiri
Pofika chaka cha 2022, n’kuti Mboni za Yehova zitakwanitsa zaka 100 m’dziko la Albania.
Nasho Idrizi anali m’modzi wa anthu oyambirira a ku Albania kukhala wa Mboni za Yehova. Iye anayamba kuphunzira Baibulo ali ku United States cha m’ma 1920 ndi gulu la Ophunzira Baibulo, dzina lomwe a Mboni za Yehova ankadziwika nalo panthawiyo.
A Idrizi anabwerera ku Albania mu 1922. Patapita nthawi, anthu ena a ku Albania omwe anaphunzira Baibulo ali ku United States, anabwerera kwawo kuti akaphunzitse anzawo zomwe anaphunzirazo.
Thanas Duli anali mmodzi wa anthu oyambirira kukhala m’gulu la Ophunzira Baibulo ku Albania. Iye ananena kuti: “Mu 1925, ku Albania kunali mipingo itatu kuphatikizapo ophunzira Baibulo ena komanso anthu achidwi omwe ankakhala m’madera osiyanasiyana a m’dzikoli.”
M’zaka zoyambirirazo, mabuku ambiri monga Zeze wa Mulungu komanso lachingelezi lakuti A Desirable Government, anali atamasuliridwa m’chiabaniya. Nsanja ya Olonda ya December 1, 1925 inanena kuti: “anthu ambiri ku Albania analandira mabuku [a m’chiabaniya] ndipo enanso ambiri akusangalala kuphunzira Baibulo.”
Anthu ambiri anayamba kutchula Amboni kuti ungjillorë, kutanthauza kuti “alaliki” chifukwa cha khama lomwe ankasonyeza pa ntchito yolalikira. A Nasho Dori omwe anabatizidwa mu 1930 anafotokoza kuti: “Mu 1935 gulu lathu linachita hayala basi kuti tikalalikire m’tawuni ya Këlcyrë. Pambuyo pake tinakonza zopita m’matawuni ena monga Përmet, Leskovik, Ersekë, Korçë, Pogradec ndi Elbasan. Ulendo wathu unakathera ku Tirana, pa nthawi imene tinkafunika kuchita Mwambo Wokumbukira Imfa ya Yesu Khristu.”
Mu 1939, boma la Italy lomwe linali lopondereza, linayamba kulamulira dziko la Albania ndipo linaletsa ntchito ya Mboni za Yehova. Abale athu anayamba kuzunzidwa chifukwa chokana kumenya nawo nkhondo. a Nthawi imeneyo abale okwana 15 anatsekeredwa m’ndende. M’bale Nikodhim Shyti anatumizidwa kundende yozunzirako anthu koma sanabwererenso.
Mu 1944, chakumapeto kwa Nkhondo Yachiwiri ya Padziko Lonse, Chipani cha Chikomyunizimu chinayamba kulamulira ku Albania. Panthawiyo, abale athu anapitirizabe kuzunzidwa ndipo ambiri anatsekeredwa m’ndende komwe ankachitiridwa nkhanza. Ndipo ena anatumizidwa kundende zozunzirako anthu zomwe zinali kutali ndi kwawo. Nthawi imeneyo, dziko la Albania linkasalidwa ndi mayiko onse. Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 1959 linanena kuti: “Ngakhale olamulira anasiyanitsa abale athu a ku Albania ndi anzawo omwe adzalowe nawo m’Dziko Latsopano, koma sangaletse Mzimu Woyera wa Mulungu kuti uzithandiza abale athuwa.” Mu 1967 boma la Albania linakhala loyamba kulengeza kuti iwo sakhulupirira kuti kuli Mulungu. Gulu lochepa la Amboni omwe anatsalabe m’dzikoli, anapitirizabe kutsatira zomwe amakhulupirira koma mosamala kwambiri.
Pa 22 May 1992, a Mboni za Yehova anakalembetsa ku boma. Apa n’kuti ulamuliro wa Chikomyunizimu utatha komanso patapita zaka zoposa 50 kuchokera pomwe ntchito ya Mboni za Yehova inaletsedwa.
Panopa ku Albania kuli Amboni okwana 5,550 omwe akutumikira m’mipingo 89. Tikusangalala ndi abale athu a ku Albania chifukwa “Mawu a Yehova anapitiriza kufalikira ndi kugonjetsa zopinga zambiri” ngakhale kuti akhala akuzunzidwa.—Machitidwe 19:20.
a Nkhondoyi inali ya pakati padziko la Greece ndi Italy ndipo inayamba pa 28 October 1940 mpaka pa 23 April, 1941. Nkhondoyi ndi imene inachititsa kuti Nkhondo Yachiwiri ya Padziko Lonse iyambike.