Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

22 JANUARY 2024
ANGOLA

Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu Latulutsidwa mu Chichokwe

Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu Latulutsidwa mu Chichokwe

Pa 13 January 2024, M’bale Jeffrey Winder wa mu Bungwe Lolamulira anatulutsa Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu mu Chichokwe. Baibuloli linatulutsidwa pamsonkhano wapadera womwe unachitikira ku ofesi ya nthambi ya Luanda m’dziko la Angola. Pamsonkhanowu panali abale ndi alongo okwana 187 ndipo enanso 353,427 analumikizidwa kudzera pa vidiyokomfelensi. Chiwerengerochi chikuphatikizapo abale ndi alongo 1,644 olankhula Chichokwe. Anthu ambiri amene anasonkhana analandira Baibulo la Malemba Achigiriki Achikhristu losindikizidwa. Baibuloli linatulutsidwanso lapazipangizo zamakono.

Anthu pafupifupi 3 miliyoni amalankhula Chichokwe ku Angola, Democratic Republic of the Congo, ndi Zambia. Pofika pano, abale ndi alongo okwana 462 akutumikira m’mipingo ya Chichokwe ku Angola. Pamene ku Democratic Republic of the Congo, abale ndi alongo okwana 734 akutumikira mumipingo 21 ya Chichokwe.

Pamene ankalengeza za kutulutsidwa kwa Baibuloli, M’bale Winder ananena kuti dzina la Mulungu lakuti Yehova likupezeka maulendo 237 mu Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu. M’bale wina ananena kuti: “Lemba la Aroma 10:13 limanena kuti ‘aliyense woitana pa dzina la Yehova adzapulumuka.’ Komabe Mabaibulo ena a Chichokwe safotokoza momveka bwino tanthauzo la lembali. Ndiye ndikuyembekezera mwachidwi kugwiritsa ntchito Malemba Achigiriki Achikhristu pothandiza anthu kuona mmene kudziwa dzina la Yehova kumathandizira kuti munthu adzapulumuke. Baibuloli ndi mphatso yapadera kwambiri!”

Tikudziwa kuti Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu la Chichokwe lithandiza anthu ambiri kuphunzira za Yehova komanso kumukonda ndi mtima wawo wonse komanso mphamvu zawo zonse.​—Maliko 12:33.