9 DECEMBER, 2022
ANGOLA
Mabuku a M’Baibulo a Mateyu ndi Machitidwe Atulutsidwa M’chilankhulo cha Chichokwe ndi Chibinda
Pa 3 December 2022, M’bale Samuel Campos wa m’Komiti ya Nthambi ku Angola, anatulutsa Baibulo la mabuku a Mateyu ndi Machitidwe m’chilankhulo cha Chichokwe ndi Chibinda. Mabuku a m’Baibulowa anatulutsidwa pazipangizo zamakono pamsonkhano wochita kujambulidwa ndipo anthu 2,000 anamvetsera pulogalamuyi.
Kagulu koyamba ka chinenero cha Chichokwe kanakhazikitsidwa mu 2007. Ndipo panopa ku Angola kuli mipingo 10 ya Chichokwe, pomwe ku Democratic Republic of the Congo iliko 23.
Mmodzi mwa abale omwe anamasulira Chichokwe ananena kuti: “Pali Mabaibulo ambiri omwe amapezeka m’chilankhulo cha Chichokwe. Limodzi mwa Mabaibulowa ndi losavuta kumva koma anasintha mawu ena pomasulira. Pomwe lina linamasuliridwa lathunthu koma ndi lovuta kumvetsa. Ndikamawerenga Baibulo latsopanoli, ndimamva kuti Yehova akundilankhula mwachindunji.”
Mpingo woyamba wa Chibinda unakhazikitsidwa mu 2014. Ndipo panopa kuli mipingo 13. Mabaibulo a mabuku a Mateyu ndi Machitidwe asanatulutsidwe, panalibe ngakhale mbali yochepa chabe ya Baibulo lomwe linkapezeka m’Chibinda, choncho abale omasulira anagwiritsa ntchito Baibulo la Dziko Latsopano la Chipwitikizi. Mmodzi mwa abale omwe anamasulira Chibinda, ananena kuti: “Pali mavesi ena a m’Baibulo amene ndawerenga kambirimbiri koma panopa m’pamene ndikuwamvetsa bwino kwambiri. Ndi mwayi waukulu kuti ndinagwira nawo ntchito yomasulirayi. Zimenezi zalimbitsa chikhulupiriro changa.”
Tikukhulupirira kuti kutulutsidwa kwa mabuku a m’Baibulo m’Chichokwe ndi m’Chibinda kuthandiza abale ndi alongo athu kuti apitirize kuyandikira kwambiri Yehova.—Yakobo 4:8.