Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

A Claudio Romero omwe ndi wachiwiri kwa nduna (kumanzere) akupereka satifiketi kwa M’bale Miguel Puchetti (kumanja) wa m’Komiti ya Nthambi ya Argentina

DECEMBER 31, 2019
ARGENTINA

Akuluakulu a Boma ku Buenos Aires Anapereka Mphoto kwa Mboni za Yehova Poyamikira Msonkhano Wamayiko wa 2019

Akuluakulu a Boma ku Buenos Aires Anapereka Mphoto kwa Mboni za Yehova Poyamikira Msonkhano Wamayiko wa 2019

Akuluakulu a boma ananena kuti msonkhano wamayiko wa 2019 womwe unachitikira mumzinda wa Buenos Aires, unali wofunika kwambiri mumzindawo pa nkhani zachipembedzo komanso zachikhalidwe. Pa 12 December, 2019, nduna ya boma inapereka satifiketi kwa abale athu pamsonkhano umene ndunayi inaitanitsa. Satifiketiyi inali yoyamikira kuti msonkhano umene Mboni za Yehova zinapanga ndi wofunika kwambiri.

Akuluakulu awiri a boma, a Claudio Romero ndi a Federico Pugliese, anayamikira a Mboni za Yehova chifukwa cha ntchito yawo ku Buenos Aires. A Claudio Romero anati: “Ndikufuna kukuthokozani chifukwa chakuti mfundo zachipembedzo chanu komanso mtendere ndi mgwirizano womwe muli nawo, zimathandiza kwambiri m’dera lathu. Ndikufuna kuti mudziwe kuti ndimasirira kwambiri chipembedzo chanu chifukwa mumadzipereka kwambiri pogwira ntchito yanu. Ndikuganiza kuti aliyense ayenera kulemekeza zimene mumachita posonyeza ena chikondi mukamawathandiza kudziwa zimene mumakhulupirira.” A Federico Pugliese anati: “Lero mwasonkhana kuti muphunzire za chikondi pa mutu wakuti, ‘Chikondi Sichitha.’ Ndikudziwa kuti mumasonyezana chikondi, osati pa nthawi ya msonkhano yokha koma mumachita zimenezi tsiku lililonse chifukwa mumaona kuti chikondi n’chofunika kwambiri.”

Satifiketi imeneyi ndi yoyamikira chikondi chimene abale ndi alongo athu amasonyeza kwa anthu ena. Timasonyeza chikondi choterechi, osati pofuna kuti tidziwike koma timafuna kulemekeza Mulungu wathu wachikondi, Yehova.—1 Yohane 4:8.