Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

29 AUGUST 2023
ARGENTINA

Kulalikira Kumalo Opezeka Anthu Ambiri pa Nthawi ya FIFA U-20 World Cup ku Argentina

Kulalikira Kumalo Opezeka Anthu Ambiri pa Nthawi ya FIFA U-20 World Cup ku Argentina

Kuyambira pa 20 May  mpaka pa 11 June 2023, masewera a FIFA U-20 World Cup anachitika m’mizinda 4 ikuluikulu ya ku Argentina. Pafupifupi anthu oposa 400,000 am’dzikolo komanso ochokera kumayiko ena anapezekako ndipo masewerawa anatenga milungu itatu. Mashelefu amatayala anaikidwa m’malo osiyanasiyana pa nthawi zosiyanasiyananso. Pafupifupi abale ndi alongo 500 anagwira nawo ntchito yolalikira ndipo anagawira mabuku oposa 500. Anthu ambiri anadziwitsidwa za webusaiti ya jw.org yomwe angapezepo mayankho amafunso awo okhudza Baibulo.

Munthu wina anabwera pafupi ndi pamene panaikidwa shelefu ndipo ananena kuti amakonda kumvetsera nkhani zojambulidwa akamachita masewera olimbitsa thupi. Kenako m’bale wina anamusonyeza webusaiti ya jw.org n’kumufotokozera mmene angapangire dawunilodi mabuku ndi zinthu zina zongomvetsera. Munthuyo ananena kuti ayamba kumvetseranso zinthu zathu zojambulidwa.

Pofuna kufikira alendo ambiri amene anabwera kudzaonerera masewerawa, mabuku athu anaikidwa pamashelefu m’zinenero 9. Komanso, ofalitsa ambiri anaphunzira moni wa zinenero zosiyanasiyana n’cholinga choti azitha kulankhulana mosavuta ndi anthu omwe ankabwera pamashelefu. M’bale wina yemwe anagwira nawo ntchito yolalikira pamashelefu, ananena kuti: “Kulalikira kwa anthu amitundu yosiyanasiyana kwasonyeza kuti Yehova ndi wokoma mtima komanso wopanda tsankho. Zimenezi zandisangalatsa kwambiri.”

N’zochititsa chidwi kuti akuluakulu a masewerawa analola kuti a Mboni za Yehova aike mashelefu awo m’malo amene alendo sankaloledwa kukumanapo, chifukwa cha chitetezo. Iwo anafotokoza kuti: “Tikudziwa kuti a Mboni za Yehova ndi anthu amtendere ndipo sangabweretse chisokonezo.” Zimenezi zinachititsa kuti oyang’anira zachitetezo amvetsere uthenga wathu.

N’zolimbikitsa kuona atumiki a Yehova akuyesetsa mwakhama kufikira anthu amitundu yonse komanso kudzala mbewu za choonadi chokhudza Ufumu padziko lonse lapansi.​—Mlaliki 11:6.