NOVEMBER 6, 2018
ARGENTINA
Ntchito Yayikulu Yolalikira Inachitika pa Nthawi ya Mpikisano wa Olympic wa Masewera a Achinyamata ku Argentina
Kuyambira pa 6 mpaka pa 18 October 2018, abale athu anagwira ntchito yaikulu yolalikira yomwe inachitika pa nthawi ya Mpikisano wa Olympic wa Masewera a Achinyamata, womwe unachitikira ku Buenos Aires m’dziko la Argentina.
Achinyamata opitirira 4,000 azaka 15 mpaka 18 ochokera m’mayiko 206 anapanga nawo mpikisano wa chaka chinowu. Anthu ambiri amaona kuti mpikisano wa achinyamatawu ndi waukulu kwambiri padziko lonse womwe pamachitika masewera osiyanasiyana. Choncho, pofuna kuthandiza achinyamata ochokera m’mayiko ena omwe amadzachita nawo masewera ndi alendo ena kuti amve uthenga wa m’Baibulo, a Mboni za Yehova oposa 6,400 anagwira nawo ntchito yolalikira. Abalewa anaika mashelefu amateyala okwana 390 m’malo pafupifupi 100.
Popeza kuti mpikisanowu ndi wa achinyamata, abale amagawira mabuku monga Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa buku loyamba ndi lachiwiri komanso kabuku kakuti Mayankho a Mafunso 10 Omwe Achinyamata Amadzifunsa. Mabukuwa ankapezeka a zinenero zosiyanasiyana, monga Chiarabiki, Chitchainizi, Chingelezi, Chifulenchi, Chijeremani, Chikoreya, Chipwitikizi, Chirasha, Chisipanishi, ndi Chinenero Chamanja cha ku Argentina. Pa nthawiyi ya mpikisanowu, abale ankagawira mabuku pafupifupi 800 patsiku.
Abale ndi alongo amene anagwira nawo ntchitoyi anasangalala kwambiri kuuzako ana ndi akulu omwe uthenga wa m’Baibulo wopatsa chiyembekezo.—Salimo 110:3.