FEBRUARY 25, 2020
ARGENTINA
Malo Atsopano Osungirako Zinthu Zakale Atsegulidwa Ku Ofesi ya Nthambi ya Argentina
Pa 11 December 2019, ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Argentina yomwe ili mumzinda wa Buenos Aires inatsegula malo atsopano osungirako zinthu zakale. Malowa ali ndi mbali ziwiri zokhala ndi mitu yakuti, “Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo” komanso “Mawu Anu Adzakhalapo Mpaka Kalekale.”
Mbali yakuti “Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo” ikusonyeza mbiri yokhudza a Mboni za Yehova ku Argentina ndi ku Uruguay kuyambira pamene anali kagulu kochepa cha m’ma 1920 mpaka mmene achulukira masiku ano. Mbaliyi ili ndi gawo lapadera losonyeza zimene abale athu ankachita pazaka zimene ntchito yathu inali yoletsedwa ku Argentina. Ikufotokozanso zokhudza ana a a Mboni omwe ankachotsedwa sukulu chifukwa chokana kuchitira sawatcha mbendera komanso abale ambirimbiri amene anatsekeredwa m’ndende kwa zaka zambiri chifukwa chokana kulowa usilikali. Ambiri mwa abale achinyamatawa anamenyedwa komanso kuchitiridwa nkhanza zosiyanasiyana ndipo abale osachepera atatu anaphedwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo.
Mbali yakuti “Mawu Anu Adzakhalapo Mpaka Kalekale” ikusonyeza Mabaibulo osiyanasiyana komanso ntchito imene anthu anagwira mwakhama kwa zaka zambiri pomasulira Baibulo m’Chisipanishi. Muli Mabaibulo 47 ofunika kwambiri omwe sapezekapezeka monga la mu 1630 lotchedwa Ferrara Bible. Baibulo limeneli linali limodzi mwa Mabaibulo athunthu omwe ndi oyambirira kumasuliridwa m’Chisipanishi kuchokera ku Malemba Achiheberi, ndipo lili ndi dzina la Mulungu pachikuto chake. Komanso, mbaliyi ikusonyeza Baibulo lotchedwa Reina-Valera Bible lomwe linamasuliridwa koyamba mu 1602. Mubaibuloli muli dzina la Mulungu lakuti Yehova m’malo onse omwe limayenera kupezeka m’Chipangano Chakale. Pa Mabaibulo onse a Chisipanishi, Baibulo la Reina-Valera Bible ndi limene limagwiritsidwa ntchito kwambiri.
Malowa akusonyeza Mabaibulo omwe anamasuliridwa m’zinenero zomwe zimalankhulidwa ndi anthu ochokera kumadera ena omwe anafika ku Argentina m’zaka za m’ma 1800. Izi zili choncho chifukwa choti kwa nthawi yaitali, anthu ambiri akhala akusamukira ku Argentina kuchokera kumayiko ena. Alendo akumaona Mabaibulo a zinenero za Chiameniya, Chikolowesha, Chingelezi, Chijeremani, Chiheberi, Chihangale, Chiayilishi Gaeli, Chitaliyana, Chipwitikizi komanso Chiwewushi.
Mbali yosonyeza Mabaibulowa ilinso ndi Mabaibulo omwe anawamaliza kumasulira ku Argentina monga la Nuevo Testamento lomasuliridwa ndi by Pablo Besson mu 1919 ndiponso omwe anamasuliridwa masiku ano m’zinenero zobadwira monga la Chorote, Mapudungún, Mocoví, Pilagá, Toba del Oeste, Toba Qom, ndi Wichí.
M’bale Timoteo Costantino yemwe amatumikira ku ofesi ya nthambi ya Argentina anati: “Tikuthokoza anthu onse amene anathandiza nawo pokonza malo oonetsera Mabaibulowa. Malowa athandiza kuti anthu ochokera ku Argentina ndiponso kumayiko ena aphunzire zambiri zokhudza mbiri ya Baibulo komanso a Mboni za Yehova ku Argentina ndi Uruguay.”