Armenia
Boma la Armenia Lazindikira Kuti Anthu Okana Usilikali Ali Ndi Ufulu
Zimene Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe lakhala likugamula, zathandiza kwambiri dziko la Armenia pa nkhani yopereka ntchito zina kwa anthu okana usilikali ndipo panopa zinthu zikuyenda bwino.
Gulu Loyamba la Mboni za Yehova ku Armenia Lamaliza Kugwira Ntchito Zimene Linapatsidwa Litakana Kulowa Usilikali
Panopo a Mboni ku Armenia angathe kugwira ntchito zimene sizikusemphana ndi zomwe amakhulupirira ndipo ntchitozo zimathandiza anthu ambiri.
Dziko la Armenia Layamba Kupereka Ntchito Zina kwa Anthu Okana Kulowa Usilikali
Werengani zimene a Mboni za Yehova, anthu amene akugwira nawo ntchito ndiponso amene akuwayang’anira ananena zokhudza dongosololi.
Dziko la Armenia Latulutsa M’ndende Anthu Amene Anamangidwa Chifukwa Chokana Kulowa Usilikali
Kodi chinachitika n’chiyani pa mlandu wokhudza kumangidwa kwa anthu a Mboni za Yehova mpaka kutulutsidwa kwawo m’ndende?
Dziko la Armenia Latulutsa M’ndende Anthu Onse a Mboni za Yehova
Kwa nthawi yoyamba kuchokera m’chaka cha 1993, palibe wa Mboni za Yehova amene ali m’ndende ku Armenia chifukwa chokana kulowa usilikali kapena kukana ntchito yosagwirizana ndi zimene amakhulupirira.
Dziko la Armenia Layamba Kupereka Ntchito Zina kwa Anthu Amene Akukana Kulowa Usilikali Chifukwa cha Zimene Amakhulupirira
Dziko la Armenia layamba kulemekeza ufulu wa anthu okana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira. A Mboni za Yehova ambiri apatsidwa ntchito zosagwirizana ndi usilikali.
Khoti Lalamula Dziko la Armenia Kuti Lipereke Chipukuta Misozi kwa Anthu 17 a Mboni za Yehova
Pa November 27, 2012, Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya linalamula dziko la Armenia kuti lipereke chipukuta misozi cha ndalama zokwana madola 145,226 kwa anthu 17 chifukwa chowaphwanyira ufulu. Anthuwa anakana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira.