Pitani ku nkhani yake

NOVEMBER 20, 2013
ARMENIA

Dziko la Armenia Latulutsa M’ndende Anthu Onse a Mboni za Yehova

Dziko la Armenia Latulutsa M’ndende Anthu Onse a Mboni za Yehova

YEREVAN, Armenia—Pa November 12, 2013, dziko la Armenia linatulutsa m’ndende anthu 14 a Mboni za Yehova amene linawamanga chifukwa chokana kulowa usilikali. Kuyambira pa October 8, 2013, anthu a Mboni amene akhala akutulutsidwa m’ndende ndi okwana 28. Anthuwa anamangidwa chifukwa chokana kuchita zinthu zosemphana ndi zimene amakhulupirira. Izi zikusonyeza kuti tsopano dziko la Armenia likusintha mfundo zake pa nkhani yokhudza kulemekeza ufulu wa anthu amene amakana kuchita zinthu zina zosemphana ndi zimene amakhulupirira. Kwa zaka 20 zapitazo, dzikoli lakhala likumanga anyamata a Mboni za Yehova oposa 450. Kwa nthawi yoyamba kuchokera m’chaka cha 1993, tsopano m’ndende za m’dziko la Armenia mulibe munthu aliyense wa Mboni za Yehova amene wamangidwa chifukwa chokana kulowa usilikali.

Anthuwa asanatulutsidwe m’ndende pa November 12, dziko la Armenia linatulutsa m’ndende anthu 8 a Mboni za Yehova pa October 8 ndi 9, potsatira malamulo ochotsera miyezi 6 pa nthawi imene akaidi ayenera kukhala m’ndende. Anthu enanso a Mboni okwana 6 anatulutsidwa pa October 24. Anthu 6 amenewa anali oyamba kupindula ndi malamulo a dzikolo amene anakonzedwanso n’kuyamba kugwira ntchito pa June 8, 2013. Malamulowo anasinthidwa n’cholinga chakuti azipereka mwayi kwa anthu okana kulowa usilikali kuti azigwira ntchito zina zosagwirizana ndi usilikali. Tsopano anthu amene akana kulowa usilikali ali ndi mwayi woti azitha kugwira ntchito zina zosakhudzana ndi usilikali m’malo motsekeredwa m’ndende.

Panopa anthu a Mboni oposa 90 apempha kuti apatsidwe ntchito zina m’malo molowa usilikali. Pa October 23 ndi pa November 12, 2013, bungwe lina loona za malamulo m’dzikoli (Republican Commission) linakambirana ndi kuvomereza pempho la anyamata 71 pa gulu la a Mboni amenewa. Ndipo bungweli linalengeza kuti m’masiku angapo akubwerawa, limalizitsa kukambirana mapempho a anyamata ena otsalawo.

Bambo David A. Semonian, omwe ndi mneneri wa Mboni za Yehova kulikulu lawo ku New York, anati: “Ndife okondwa chifukwa boma la Armenia lamasula anyamatawa ndipo zikuoneka kuti nkhaniyi, yomwe yakhala ikuvuta kwa nthawi yaitali, tsopano yatha.”

Lankhulani ndi:

Kuchokera M’mayiko ena: David A. Semonian, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000

Armenia: Tigran Harutyunyan, tel. +374 93 900 482