Mfundo Zachidule Zokhudza a Mboni ku Armenia
A Mboni za Yehova amalambira mwaufulu ku Republic of Armenia ndipo sakumana ndi mavuto aakulu akamagwira ntchito zokhudza chipembedzo chawo. Iwo analembetsa kuti akhale ovomerezeka ndi boma mu October 2004.
Usanafike mwezi wa October 2013, vuto lalikulu limene a Mboni ankakumana nalo ku Armenia linali loti anthu okana usilikali sankapatsidwa ntchito zina m’malo mwa usilikali, chifukwa dziko la Armenia linkayang’aniridwa ndi asilikali ndipo linkapondereza anthu. Kuyambira mu 1993, anyamata a Mboni mahandiredi ambiri omwe ankakana usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira, ankapatsidwa chigamulo choti akhale m’ndende zaka zambiri ndipo ena ankakhala mozunzika kwambiri. Koma pa 8 June, 2013, boma la Armenia linasintha lamulo loti anthu okana kulowa usilikali azipatsidwa ntchito zina m’malo mwa usilikali kuti ligwirizane ndi mfundo zimene mayiko a ku Europe amayendera. Pa 23 October, 2013, akuluakulu a boma anavomera zomwe a Mboni 57 anapempha zoti awapatse ntchito zina m’malo mwa usilikali. Zimenezi zathandiza a Mboniwo chifukwa akugwira ntchito zothandiza dziko lawo ndi chikumbumtima chabwino.
Ngakhale kuti zinthu zasintha chonchi, a Mboni za Yehova amasalidwa. Akuluakulu ena oyang’anira mizinda amakana kupatsa a Mboni chilolezo choti amange malo awo olambirira, akuluakulu oona za katundu wolowa ndi kutuluka m’dzikolo amatchaja ndalama zokwera kwambiri pa mabuku omwe a Mboni amalowetsa m’dzikoli, komanso anthu otsutsa amafalitsa nkhani zabodza zokhudza a Mboni pogwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana. A Mboni za Yehova anakasuma ku makhoti a m’dzikolo komanso a m’mayiko ena pofuna kuthetsa mavutowa.