Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

FEBRUARY 15, 2019
AUSTRALIA

Madzi Osefukira Awononga Kwambiri ku Queensland M’dziko la Australia

Madzi Osefukira Awononga Kwambiri ku Queensland M’dziko la Australia

Mvula yamphamvu kwambiri yachititsa kuti madzi asefukire kumpoto chakummawa kwa dziko la Australia. Madzi osefukirawa achititsa kuti anthu masauzande ambiri okhala m’derali athawe m’nyumba zawo, katundu wambiri awonongeke komanso kuzimitsa magetsi.

Ofesi ya nthambi ya ku Australasia inanena kuti chifukwa cha kusefukira kwa madziku, ofalitsa 58 a m’mipingo itatu ankafunika kusamukira kunyumba za achibale awo kapena kwa a Mboni ena. Madzi osefukirawa anafika kunyumba 10 za abale athu, ndipo ziwiri zinaonongeka.

Ofesi ya nthambi yakhazikitsa Komiti Yothandiza Pangozi Zadzidzidzi, ndipo woyang’anira dera komanso akulu a m’derali akulimbikitsa ofalitsa omwe anakhudzidwa ndi madzi osefukirawa. Tikupempherera abale ndi alongo athu kuti apitirize kupirira komanso kutonthozedwa ndi abusa a chikondi amenewa.—1 Petulo 5:2.