26 AUGUST, 2022
AUSTRALIA
Mmene Ntchito Yojambula Mbali Yoyamba ya Vidiyo Yakuti Moyo wa Yesu Komanso Utumiki Wake Yayendera
Chigawo choyamba chojambula Mbali Yoyamba ya Vidiyo ya Moyo wa Yesu Komanso Utumiki Wake chinamalizidwa pa 12 August, 2022. Ngakhale kuti ntchitoyi inasokonezedwa kwa nthawi yochepa, chigawo chachiwiri chojambula vidiyoyi chiyamba posachedwa ndipo chikuyembekezeka kudzamalizidwa mu October 2022.
Mogwirizana ndi zimene tinanena mulipoti la m’mbuyomu, abale anayamba kujambula vidiyo ya Moyo wa Yesu Komanso Utumiki Wake pa 20 May, 2022 ndipo anayamba ndi kujambula mbali yosonyeza zochitika m’nyumba. Panthawiyi abale anali akuyembekezera kulandira mapepala omaliza otsimikizira kuti akhoza kuyamba kujambula mbali yosonyeza zochitika panja. Mapepalawa anamaliza kuwakonza pa 15 July, 2022. Dipatimenti Yazomangamanga ya Nthambi ya Australasia inapereka chilolezo ku Gulu Lojambula Mavidiyo kuti ingathe kuyamba kugwiritsa ntchito nyumba zomwe zinamangidwazo komanso kuti zonse zinali m’malo kuti ntchito yojambula iyambe. Tsopano malo onsewa ndi oti akhoza kugwiritsidwa ntchito kujambulirapo vidiyo.
Anthu odzipereka oposa 500 ochokera ku Australia ndi ku New Zealand, ndi omwe anagwira ntchito yomanga zinthu zosiyanasiyana pamalowa. Malo onsewa ndi aakulu kuposa masikweya mita 7,000. Pofotokozapo za ntchito yomanga malowa, M’bale Russell Grygorcewicz amene ndi wogwirizanitsa wa Komiti Yazomangamanga ananena kuti: “Ngakhale kuti tikukumana ndi mavuto ambiri, tikuona umboni wotsimikizira kuti Yehova akutithandiza kulimbana ndi mavutowa. Ndipo ndi zosakayikitsa kuti mbali ya ntchito yomwe tamalizayi, yatheka ndi mzimu wa Yehova.”
M’bale Ronald Curzan amene ndi wothandiza Komiti Yoona za Ntchito Yophunzitsa, nthawi zambiri ankakhalapo pomwe chigawo choyamba cha ntchitoyi chinkajambulidwa. Iye anati: “Panali mgwirizano komanso kuchita zinthu mwaubwenzi pakati pa abale ogwira ntchito zomangamanga ndi abale a m’banja la Beteli ndipo izi ndi zotamandika kwambiri. Ndi zosangalatsa kwambiri kuona kuti malo onse ojambulira ayamba kugwira ntchito patatha zaka zambiri tikupanga mapulani komanso kugwira ntchito yomanga. Zinalinso zolimbikitsa kwambiri kuona mmene abale ndi alongo okhala m’gawo la nthambi ya Australasia athandizira pa ntchitoyi. Sitikukayikira kuti vidiyoyi yomwe idzakhala ndi zigawo 18, idzalimbikitsa anthu padziko lonse.”
M’bale Kenneth Cook wa m’Bungwe Lolamulira, amenenso analipo pamasiku omaliza ojambula Gawo Loyamba, ananena kuti: “N’zoonekeratu kuti Atate wathu wachikondi akudalitsa ntchitoyi. Tikuthokoza Yehova ndi onse omwe agwira nawo ntchitoyi chifukwa cha kudzipereka komanso khama lawo. Ndi pemphero lathu kuti vidiyo yapaderayi idzathandize anthu ambiri kuti azitsatira kwambiri Yesu komanso kuyandikira kwambiri Yehova.”
Polowera kumalo osonyeza nyumba zakale
Chithunzi chojambulidwa kuchokera m’mwamba chosonyeza mbali ina ya nyumba zakale zomwe zinamalizidwa
Khola la nkhosa (chapatsogolo) lomwe lili kunja kwa nyumba zakale
Msika
Maofesi a boma