Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

JANUARY 10, 2020
AUSTRALIA

Moto Wolusa Siukutha ku Australia

Moto Wolusa Siukutha ku Australia

M’chaka cha 2019, ku Australia kunatentha kwambiri kuposa zaka zina m’mbuyomu ndipo kunabuka moto wolusa womwe ukupitirizabe kuyaka kwambiri. Kuyambira mu September 2019, moto wolusawu wakhala ukuyaka m’chigawo chilichonse ku Australia ndipo ukupitirirabe. Madera omwe akhudzidwa kwambiri ndi Victoria komanso New South Wales, komwe ndi kufupi ndi nyanja ndiponso kum’mwera chakum’mawa kwa dzikoli.

Palibe m’bale kapena mlongo aliyense amene wavulala kapena kufa chifukwa cha motowu. Komabe, nyumba zambiri zinaonongeka kuphatikizapo nyumba 9 zomwe zinapseratu. Pofika pano, abale ndi alongo oposa 700 athawa m’nyumba zawo. Mabanja ambiri a Mboni za Yehova anasankha kusamuka m’madera omwe anakhudzidwa ndi motowu chifukwa cha utsi woopsa. Akatswiri ena akukhulupirira kuti utsiwu waononga kwambiri mpweya ndipo ukhoza kuononga thanzi la anthu. Ambiri mwa abale ndi alongowa akukhala m’nyumba za achibale awo, anzawo kapenanso ofalitsa a m’mipingo ya m’madera oyandikana nawo komwe sikumafika moto.

Ofesi ya nthambi ya Australasia yakonza makomiti awiri kuti alimbikitse abalewa pogwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo ndiponso kupereka chithandizo. Oyang’anira madera awiri komanso abale a m’Komiti ya Nthambi akulimbikitsa abale ndi alongo athuwa m’madera omwe anakhudzidwa ndi motowu. Ngakhale kuti zimenezi zinachititsa kuti ambiri mwa abale ndi alongo omwe anakhudzidwa atope kwambiri komanso akhale ndi nkhawa, ambiri akuyamikira mochokera pansi pa mtima chikondi chenicheni chomwe abale ndi alongo athu akupitirizabe kuwasonyeza.—1 Petulo 2:17.