Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

DECEMBER 13, 2019
AUSTRALIA

Moto Wolusa Unawononga M’madera Ambiri ku Australia

Moto Wolusa Unawononga M’madera Ambiri ku Australia

Nyumba ya banja lina la Mboni inapsa ndi moto umene unawotcha dera lokwana maekala pafupifupi 2.5 miliyoni ku New South Wales ndi Queensland, m’dziko la Australia. Palibe wa Mboni aliyense yemwe anafa kapena kuvulala chifukwa cha motowu. Palibenso Nyumba za Ufumu kapena Nyumba za Misonkhano zomwe zinakhudzidwa ndi motowu.

Akuluakulu a boma akuganiza kuti anthu ndi amene anayambitsa motowu m’madera ena. Kuyambira mu September, motowu wapha anthu 6 komanso wawotcha nyumba zosachepera 650.

Abale ndi alongo 200 omwe anathawa m’nyumba zawo tsopano abwerera. Banja lomwe nyumba yawo inapsa likukhala limodzi ndi a Mboni ena. Akulu a m’mipingo akulimbikitsa abale ndi alongo omwe anakhudzidwa ndi motowu.—Machitidwe 20:28.